Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide.
55 Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa,+
Ndipo musanyalanyaze pempho langa lakuti mundichitire chifundo.*+
2 Ndimvetsereni ndipo mundiyankhe.+
Mtima wanga suli mʼmalo chifukwa cha nkhawa zanga,+
Ndipo ndikuvutika mumtima mwanga
3 Chifukwa cha zimene mdani wanga akunena
Komanso chifukwa chakuti woipa akundipanikiza.
Iwo andiunjikira mavuto,
Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+
5 Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera,
Komanso ndikunthunthumira.
6 Nthawi zonse ndimanena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!
Ndikanaulukira kutali nʼkukakhala malo otetezeka.
7 Ndikanathawira kutali.+
Ndikanapita kukakhala mʼchipululu.+ (Selah)
8 Ndikanathawira kumalo otetezeka,
Kutali ndi mphepo yamphamvu, kutali ndi mphepo yamkuntho.”
9 Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani mapulani awo,*+
Chifukwa ndaona zachiwawa ndi mikangano mumzinda.
10 Masana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.
Ndipo mumzindawo muli chidani ndi mavuto.+
11 Mmenemo muli mavuto okhaokha.
Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizimachoka kubwalo la mzindawo.+
12 Chifukwa amene akundinyoza si mdani.+
Akanakhala mdani ndikanapirira.
Amene wandiukira si munthu wodana nane kwambiri.
Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.
14 Tinali mabwenzi apamtima.
Tinkayenda limodzi ndi gulu la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.
15 Iwo awonongedwe!+
Atsikire ku Manda* ali amoyo.
Chifukwa mʼmalo amene amakhala komanso mʼmitima yawo muli zoipa.
16 Koma ine ndidzafuulira Mulungu,
Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+
18 Iye adzandipulumutsa* kwa anthu amene akundiukira nʼkundipatsa mtendere,
Chifukwa gulu la anthu landiukira.+
19 Mulungu adzamva ndipo adzawapatsa chilango,+
Amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale.+ (Selah)
Iwo adzakana kusintha,
Anthu amene sanaope Mulungu.+
21 Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta amumkaka,+
Koma mumtima mwake amakonda nkhondo.
Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta,
Koma ali ngati malupanga akuthwa.+
Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.*+
23 Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipawo mʼdzenje lakuya.+
Anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso achinyengowo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+
Koma ine ndidzakhulupirira inu.