Miyambo
3 Mwana wanga, usaiwale zimene ndimakuphunzitsa,*
Ndipo mtima wako uzisunga malamulo anga.
2 Ukamachita zimenezi, udzakhala ndi masiku ochuluka
Komanso moyo wazaka zambiri ndi mtendere.+
3 Usalole kuti chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika* zichoke mwa iwe.+
Uzimange mʼkhosi mwako
Ndi kuzilemba pamtima pako.+
4 Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu+
Adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.
7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+
Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.
8 Zimenezi zidzachiritsa thupi lako*
Ndi kutsitsimutsa mafupa ako.
9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+
Ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.*+
10 Ukatero nyumba zako zosungiramo zinthu zidzadzaza kwambiri,+
Ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.
11 Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+
Ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+
12 Chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amamukonda,+
Ngati mmene bambo amadzudzulira mwana amene amasangalala naye.+
13 Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru,+
Ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira.
14 Chifukwa kupeza nzeru nʼkwabwino kuposa kupeza siliva,
Ndipo kukhala nazo monga phindu nʼkwabwino kuposa kukhala ndi golide.+
15 Nʼzamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,*
Palibe chimene umalakalaka chimene chingafanane nazo.
16 Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali.
Mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero.
17 Kuyenda mʼnjira zake kumasangalatsa,
Ndipo kuyenda mʼmisewu yake kumabweretsa mtendere.+
18 Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye,
Ndipo anthu amene amazigwiritsitsa adzatchedwa osangalala.+
19 Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+
Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+
20 Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuya
Ndipo kumwamba kwa mitambo kunagwetsa mame.+
21 Mwana wanga, zimenezi* zisachoke pamaso pako.
Uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.
22 Zidzakupatsa moyo
Komanso zidzakhala zokongoletsera mʼkhosi mwako.
23 Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,
28 Mnzako usamuuze kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndipo ndidzakupatsa,”
Ngati ungathe kumupatsa nthawi yomweyo.
29 Usakonze zochitira mnzako zoipa+
Pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.
31 Usasirire munthu wachiwawa+
Kapena kusankha kuyenda mʼnjira yake iliyonse,
32 Chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso,+
Koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.+
35 Anzeru adzalandira ulemu,
Koma opusa amalemekeza zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+