Salimo
78 Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.*
Tcherani khutu ku mawu apakamwa panga.
2 Ndidzatsegula pakamwa panga nʼkunena mwambi.
Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale.+
3 Zinthu zimene tinamva ndipo tikuzidziwa,
Zimene makolo athu anatifotokozera,+
4 Sitidzazibisa kwa ana awo.
Tidzafotokozera mʼbadwo wamʼtsogolo+
Tidzawafotokozera zinthu zotamandika zimene Yehova anachita komanso mphamvu zake,+
Zinthu zodabwitsa zimene wachita.+
5 Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,
Ndipo anaika chilamulo mu Isiraeli.
Iye analamula makolo athu
Kuti auze ana awo zinthu zimenezi,+
6 Kuti mʼbadwo wotsatira,
Ana amene adzabadwe mʼtsogolo, adzadziwe zimenezi.+
Nawonso adzazifotokoze kwa ana awo.+
7 Zikadzatero anawo azidzadalira Mulungu.
8 Akadzachita zimenezi sadzakhala ngati makolo awo,
Mʼbadwo wosamva komanso wopanduka,+
Mʼbadwo umene mtima wawo unali wosakhazikika*+
Komanso wosakhulupirika kwa Mulungu.
9 Anthu a fuko la Efuraimu anali ndi mauta,
Koma anathawa pa tsiku lankhondo.
13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,
Ndipo anaimitsa madzi nʼkukhala ngati khoma.+
14 Iye ankawatsogolera ndi mtambo masana
Ndipo usiku wonse ankawatsogolera ndi kuwala kwa moto.+
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu,
Anawalola kumwa madziwo mpaka ludzu kutha ngati kuti akumwa madzi amʼnyanja.+
16 Iye anatulutsa madzi ochuluka pathanthwe,
Ndipo anachititsa madzi ambiri kuti ayende ngati mitsinje.+
17 Koma iwo anapitiriza kumuchimwira
Popandukira Wamʼmwambamwamba mʼchipululu.+
18 Iwo anayesa Mulungu mʼmitima yawo+
Pomuumiriza kuti awapatse chakudya chimene ankalakalaka.
19 Choncho iwo analankhula mawu amwano kwa Mulungu
Kuti: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya mʼchipululu muno?”+
20 Iye anamenya thanthwe
Moti panatuluka madzi ambiri ndipo mitsinje inasefukira.+
Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,
Kapena kodi angapatse anthu ake nyama?”+
21 Yehova atamva zimene ankanenazo anakwiya kwambiri.+
Moto+ unayakira Yakobo,
Ndipo mkwiyo wake unayakira Isiraeli+
22 Chifukwa chakuti sanakhulupirire Mulungu.+
Sanakhulupirire kuti iye angathe kuwapulumutsa.
23 Choncho Mulungu analamula mitambo yamumlengalenga,
Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba.
24 Iye anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.
Anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+
26 Anachititsa kuti mphepo yakumʼmawa iwombe mumlengalenga,
Komanso ndi mphamvu zake, anachititsa kuti mphepo yakumʼmwera iwombe.+
27 Iye anawagwetsera nyama yochuluka ngati fumbi,
Anawagwetsera mbalame zochuluka ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.
28 Anawagwetsera zimenezi mumsasa wawo,
Kuzungulira matenti awo onse.*
29 Iwo anadya nʼkukhuta kwambiri.
Iye anawapatsa zimene ankalakalaka.+
Iye anapha amuna amphamvu pakati pawo.+
Anapha anyamata a mu Isiraeli.
32 Ngakhale zinali choncho, iwo anapitiriza kumuchimwira,+
Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+
33 Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya,+
Ndipo anawabweretsera masoka amene anachititsa kuti afe mwadzidzidzi.
34 Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo ankamufunafuna.+
Iwo ankabwerera nʼkuyamba kufunafuna Mulungu,
35 Chifukwa choti ankakumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+
36 Koma iwo ankafuna kumupusitsa ndi pakamwa pawo
Komanso kumunamiza ndi lilime lawo.
Nthawi zambiri ankabweza mkwiyo wake+
Mʼmalo moonetsa ukali wake wonse.
39 Iye ankakumbukira kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+
Ali ngati mphepo imene imadutsa ndipo sibwereranso.*
42 Iwo sanakumbukire mphamvu za* Mulungu,
Tsiku limene anawapulumutsa* kwa mdani wawo,+
43 Sanakumbukire mmene anasonyezera zizindikiro zake ku Iguputo,+
Komanso zinthu zodabwitsa zimene anachita mʼdera la Zowani,
44 Sanakumbukirenso mmene anasandutsira madzi amʼngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+
Moti sanathe kumwa madziwo.
45 Mulungu anawatumizira ntchentche zoluma kuti ziwasowetse mtendere,+
Komanso achule kuti awawononge.+
46 Anapereka zokolola zawo kwa dzombe lowononga,
Anapereka zipatso za ntchito yawo kwa dzombe lochuluka.+
47 Anawononga mitengo yawo ya mpesa+
Komanso mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala.
48 Anapha nyama zawo zonyamula katundu pogwiritsa ntchito matalala,+
Ndiponso ziweto zawo ndi mphezi.
49 Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,
Komanso ukali wake ndipo anawabweretsera mavuto,
Anawatumizira magulu a angelo kuti awabweretsere tsoka.
50 Mkwiyo wake anaulambulira njira.
Sanawapulumutse ku imfa,
Ndipo anawagwetsera mliri.*
51 Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa a ku Iguputo,+
Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka mʼmatenti a Hamu.
52 Kenako anatulutsa anthu ake mʼdzikolo ngati gulu la nkhosa,+
Ndipo anawatsogolera mʼchipululu ngati nkhosa.
54 Kenako anawalowetsa mʼdziko lake lopatulika,+
Mʼdera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu kuichotsa pamaso pawo.+
Iye anawagawira dzikolo kuti likhale cholowa chawo pochita kuwayezera ndi chingwe.+
Anachititsa mafuko a Isiraeli kuti akhale mʼnyumba zawozawo.+
56 Koma iwo anapitiriza kuyesa Mulungu Wamʼmwambamwamba komanso kumupandukira.+
Sanamvere zikumbutso zake.+
57 Iwo anasiyanso Mulungu ndipo ankachita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+
Anali osadalirika ngati uta wosakunga kwambiri.+
58 Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+
59 Mulungu anamva ndipo anakwiya kwambiri,+
Choncho anawakaniratu Aisiraeli.
61 Analola kuti adani atenge chizindikiro cha mphamvu zake,
Analola kuti ulemerero wake ukhale mʼmanja mwa adani.+
62 Iye anapereka anthu ake ku lupanga,+
Ndipo anakwiyira cholowa chake.
63 Moto unapsereza anyamata ake,
Ndipo anamwali ake sanawaimbire nyimbo zapaukwati.*
65 Kenako Yehova anadzuka ngati kuti anali mtulo,+
Ngati mmene amadzukira munthu wamphamvu+ pambuyo pomwa vinyo wambiri.
66 Iye anathamangitsa adani ake nʼkuwabweza,+
Anachititsa kuti adaniwo akhale onyozeka mpaka kalekale.
67 Iye anakana tenti ya Yosefe,
Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu.
69 Anachititsa kuti malo ake opatulika akhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba,*+
Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+