Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira “Mbawala Yaikazi ya Mʼbandakucha.”* Nyimbo ya Davide.
22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+
Nʼchifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?
Nʼchifukwa chiyani simukumva kubuula kwanga?+
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimakuitanani masana, koma simundiyankha.+
Ndipo usiku sindikhala chete, ndimaitanabe.
7 Anthu onse amene amandiona amandiseka.+
Iwo amandinyogodola nʼkumapukusa mitu yawo mondinyoza nʼkumati:+
8 “Anadzipereka kwa Yehova. Tiyeni tione ngati angamupulumutse!
Musiyeni Mulungu amupulumutse, chifukwa amamukonda kwambiri!”+
9 Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba,+
Ndinu amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinkayamwa mabere a mayi anga.
10 Ndinaperekedwa kwa inu kuti muzindisamalira* kuyambira pamene ndinabadwa.
Kuyambira ndili mʼmimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine, chifukwa mavuto ali pafupi+
Ndipo palibe winanso amene angandithandize.+
12 Ngʼombe zazingʼono zamphongo zochuluka zandizungulira.+
Ngʼombe zamphongo zamphamvu za ku Basana zandizungulira.+
13 Iwo atsegula pakamwa pawo nʼkumandiopseza,+
Ngati mkango wobangula umene umakhadzulakhadzula nyama.+
14 Ndathiridwa pansi ngati madzi.
Mafupa anga onse aguluka.
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale.+
Lilime langa lamatirira kunkhama zanga,+
Ndipo mwandilowetsa mʼdzenje kuti ndife.+
16 Adani anga andizungulira ngati agalu.+
Andizungulira ngati gulu la anthu ochita zoipa,+
Mofanana ndi mkango, iwo akundiluma manja ndi mapazi.+
17 Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+
Adaniwo akuona zimenezi ndipo akundiyangʼanitsitsa.
18 Iwo akugawana zovala zanga,
Ndipo akuchita maere pa zovala zanga.+
19 Koma inu Yehova, musakhale kutali ndi ine.+
Inu ndinu mphamvu zanga, ndithandizeni mofulumira.+
20 Ndipulumutseni ku lupanga,
Pulumutsani moyo wanga wamtengo wapatali* mʼkamwa* mwa agalu.+
21 Ndipulumutseni mʼkamwa mwa mkango+ komanso kunyanga za ngʼombe zamphongo zamʼtchire.
Mundiyankhe ndi kundipulumutsa.
23 Inu amene mumaopa Yehova, mutamandeni!
Inu nonse mbadwa* za Yakobo, mʼpatseni ulemerero!+
Muopeni, inu nonse mbadwa* za Isiraeli.
24 Chifukwa iye sananyoze kapena kunyansidwa ndi kuvutika kwa munthu woponderezedwa.+
Sanabise nkhope yake kwa iye.+
Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+
25 Ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+
Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu amene amamuopa.
Musangalale ndi moyo* mpaka kalekale.
27 Anthu onse ochokera kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova nʼkupita kwa iye.
Ndipo mabanja onse a mitundu ya anthu adzagwada pamaso panu.+
28 Chifukwa Yehova ndi Mfumu,+
Ndipo akulamulira mitundu ya anthu.
29 Anthu onse olemera* padziko lapansi adzadya ndipo adzamuweramira.
Anthu onse amene amabwerera kufumbi adzagwada pamaso pake,
Ndipo palibe aliyense wa iwo amene angapulumutse moyo wawo.
30 Mbadwa* zawo zidzamutumikira.
Mibadwo yamʼtsogolo idzauzidwa zokhudza Yehova.
31 Adzabwera nʼkunena za chilungamo chake.
Adzauza anthu amene adzabadwe zimene iye wachita.