Salimo
א [Aleph]
119 Osangalala ndi anthu amene salakwitsa kanthu* mʼnjira zawo,
Amene amatsatira chilamulo cha Yehova.+
3 Iwo sachita zinthu zosalungama.
Amayenda mʼnjira zake.+
4 Inu mwalamula
Kuti tizitsatira malamulo anu mosamala.+
6 Zikanatero sindikanachita manyazi,+
Pa nthawi imene ndikuganizira malamulo anu onse.
7 Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,
Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.
8 Ndidzasunga malangizo anu.
Choncho musandisiye ndekha.
ב [Beth]
9 Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake?
Akamadzifufuza nthawi zonse kuti aone ngati zochita zake zikugwirizana ndi mawu anu.+
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse.
Musalole kuti ndisochere nʼkuchoka pa malamulo anu.+
12 Mutamandike, inu Yehova.
Ndiphunzitseni malamulo anu.
13 Ndi milomo yanga ndalengeza
Zigamulo zonse zimene inu mwanena.
14 Ndimasangalala ndi zikumbutso zanu,+
Kuposa mmene ndimasangalalira ndi zinthu zina zonse zamtengo wapatali.+
16 Ndimakonda malamulo anu.
Sindidzaiwala mawu anu.+
ג [Gimel]
17 Ndichitireni zinthu mokoma mtima, ine mtumiki wanu,
Kuti ndikhale ndi moyo komanso kuti ndisunge mawu anu.+
18 Tsegulani maso anga kuti ndione bwinobwino
Zinthu zodabwitsa zamʼchilamulo chanu.
19 Ine ndine mlendo mʼdzikoli.+
Musandibisire malamulo anu.
20 Ndimalakalaka kwambiri
Nditadziwa zigamulo zanu nthawi zonse.
21 Mumadzudzula anthu odzikuza,
Otembereredwa amene akusochera nʼkusiya kutsatira malamulo anu.+
22 Muwachititse kuti asiye* kusandilemekeza komanso kundinyoza,
Chifukwa ndatsatira zikumbutso zanu.
23 Ngakhale pamene akalonga asonkhana pamodzi nʼkumakambirana zoti andiukire,
Ine mtumiki wanu ndimaganizira mozama* malangizo anu.
ד [Daleth]
25 Ndagona pafumbi.+
Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi mawu anu.+
26 Ndinakuuzani za njira zanga ndipo munandiyankha.
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
27 Ndithandizeni kumvetsa tanthauzo la* malamulo anu,
28 Ine ndakhala ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.
Ndilimbitseni mogwirizana ndi mawu anu.
29 Ndithandizeni kuti ndisakhale munthu wachinyengo,+
Ndipo mundikomere mtima pondipatsa chilamulo chanu.
30 Ine ndasankha kuti ndizichita zinthu mokhulupirika.+
Ndimadziwa kuti zigamulo zanu ndi zolungama.
31 Ndimatsatira zikumbutso zanu nthawi zonse.+
Inu Yehova, musalole kuti ndikhumudwe.*+
32 Ndidzatsatira* malamulo anu ndi mtima wonse,
Chifukwa mwandithandiza kuti ndiwamvetse bwino.
ה [He]
33 Ndiphunzitseni inu Yehova,+ kuti ndizichita zinthu mogwirizana ndi malangizo anu,
Ndipo ndidzawatsatira kwa moyo wanga wonse.+
34 Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira
Kuti nditsatire chilamulo chanu,
Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wanga wonse.
36 Ndithandizeni kuti mtima wanga uzikonda zikumbutso zanu,
Osati kupeza phindu mwachinyengo.+
37 Ndithandizeni kuti ndizipewa kuyangʼana zinthu zopanda pake.+
Ndithandizeni kuyenda mʼnjira yanu kuti ndikhalebe ndi moyo.
38 Kwaniritsani zimene munalonjeza* mtumiki wanu,
Kuti anthu azikuopani.
39 Chotsani zinthu zochititsa manyazi zimene ndikuziopa,
Chifukwa zigamulo zanu ndi zabwino.+
40 Taonani mmene ndikulakalakira malamulo anu.
Ndithandizeni kukhalabe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.
ו [Waw]
41 Ndione chikondi chanu chokhulupirika, inu Yehova,+
Komanso mundipulumutse mogwirizana ndi lonjezo lanu.*+
42 Mukatero ndiyankha amene akundinyoza,
Chifukwa ine ndimadalira mawu anu.
43 Ndithandizeni kuti ndipitirize kunena mawu a choonadi,
Chifukwa ndikuyembekezera* chigamulo chanu.
44 Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,
Mpaka kalekale.+
46 Ndidzanena zokhudza zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,
Ndipo sindidzachita manyazi.+
47 Ndimakonda kwambiri malamulo anu,
Inde, ndimawakonda.+
48 Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+
ז [Zayin]
50 Izi ndi zimene zimandilimbikitsa ndikakhala pamavuto,+
Chifukwa mawu anu andithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.
51 Anthu odzikuza andinyoza koopsa.
Koma ine sindinasiye kutsatira chilamulo chanu.+
53 Ndakwiya kwambiri chifukwa cha oipa,
Amene akusiya chilamulo chanu.+
54 Kwa ine, malangizo anu ali ngati nyimbo,
Kulikonse kumene ndimakhala.*
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+
Kuti ndisunge chilamulo chanu.
56 Ndakhala ndikuchita zimenezi
Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.
ח [Heth]
59 Ndaganizira mozama za njira zanga,
Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.+
60 Ndimafulumira ndipo sindizengereza
Kusunga malamulo anu.+
61 Zingwe za oipa zandikulunga,
Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.+
62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikuyamikeni+
Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.
63 Ine ndine mnzawo wa anthu amene amakuopani,
Ndiponso wa anthu amene amasunga malamulo anu.+
64 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chadzaza dziko lapansi.+
Ndiphunzitseni malamulo anu.
ט [Teth]
65 Inu Yehova, mwandichitira zabwino ine mtumiki wanu,
Mogwirizana ndi mawu anu.
66 Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira komanso wodziwa zinthu,+
Chifukwa ndimadalira malamulo anu.
68 Inu ndinu wabwino+ ndipo ntchito zanu ndi zabwino.
Ndiphunzitseni malamulo anu.+
69 Anthu odzikuza akundinenera zinthu zambiri zabodza,
Koma ine ndimasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.
71 Zili bwino kuti ndakumana ndi mavuto,+
Kuti ndiphunzire malamulo anu.
72 Chilamulo chimene mwapereka nʼchabwino kwa ine,+
Nʼchabwino kwambiri kuposa ndalama zagolide ndi zasiliva masauzande ambiri.+
י [Yod]
73 Manja anu anandipanga komanso kundiumba.
Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira,
Kuti ndiphunzire malamulo anu.+
75 Inu Yehova, ndikudziwa kuti zigamulo zanu ndi zolungama+
Komanso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.+
76 Chikondi chanu chokhulupirika+ chindilimbikitse,
Mogwirizana ndi zimene munandilonjeza* ine mtumiki wanu.
77 Ndisonyezeni chifundo kuti ndipitirize kukhala ndi moyo,+
Chifukwa ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
78 Odzikuza achite manyazi,
Chifukwa amandilakwira popanda chifukwa.
Koma ine ndidzaganizira mozama* malamulo anu.+
79 Anthu amene amakuopani abwerere kwa ine,
Amene amadziwa zikumbutso zanu.
כ [Kaph]
83 Chifukwa ndili ngati thumba lachikopa limene lauma mu utsi,
Koma sindinaiwale malangizo anu.+
84 Kodi ine mtumiki wanu ndidikira mpaka liti?
Kodi anthu amene akundizunza mudzawaweruza liti?+
85 Anthu odzikuza andikumbira dzenje kuti ndigweremo,
Anthu amene safuna kutsatira chilamulo chanu.
86 Malamulo anu onse ndi odalirika.
Anthu akundizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+
87 Iwo anangotsala pangʼono kundifafaniza padziko lapansi,
Koma ine sindinasiye kutsatira malamulo anu.
88 Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika,
Kuti ndisunge zikumbutso zimene mwatipatsa.
ל [Lamed]
89 Inu Yehova, mawu anu adzakhazikika kumwamba,+
Mpaka kalekale.
90 Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwo yonse.+
Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lipitirizebe kukhalapo.+
91 Ntchito zanu zilipobe mpaka pano chifukwa cha zigamulo zanu,
Chifukwa zonsezo zimakutumikirani.
92 Ndikanakhala kuti sindimakonda kwambiri chilamulo chanu,
Ndikanakhala nditafa chifukwa cha mavuto anga.+
93 Sindidzaiwala malamulo anu,
Chifukwa mwandithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo pogwiritsa ntchito malamulo amenewo.+
95 Oipa amayembekezera kuti andiwononge,
Koma ine ndimamvetsera mwatcheru zikumbutso zanu.
96 Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire,
Koma malamulo anu alibe malire.*
מ [Mem]
97 Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+
Ndimaganizira mozama* chilamulocho tsiku lonse.+
98 Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,+
Chifukwa ali ndi ine mpaka kalekale.
99 Ndine wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse,+
Chifukwa ndimaganizira mozama* zikumbutso zanu.
100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,
Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.
101 Ndimakana kuyenda mʼnjira iliyonse yoipa,+
Kuti ndisunge mawu anu.
102 Sindinasiye kutsatira zigamulo zanu,
Chifukwa inu mwandilangiza.
103 Mawu anu amatsekemera kwambiri mʼkamwa mwanga,
Kuposa mmene uchi umakomera!+
104 Ndimachita zinthu mozindikira chifukwa cha malamulo anu.+
Nʼchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
נ [Nun]
105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,
Komanso kuwala kounikira njira yanga.+
106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,
Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.
107 Ndavutika kwambiri.+
Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi mawu anu.+
108 Inu Yehova, chonde sangalalani ndi nsembe zanga zaufulu zokutamandani,*+
Ndipo mundiphunzitse zigamulo zanu.+
110 Oipa anditchera msampha,
Koma ine sindinasochere nʼkusiya kutsatira malamulo anu.+
111 Ndimaona kuti zikumbutso zanu ndi chuma changa mpaka kalekale,*
Chifukwa zimasangalatsa mtima wanga.+
112 Ndatsimikiza mtima kumvera malamulo anu
Nthawi zonse, mpaka ndidzamwalire.
ס [Samekh]
114 Inu ndinu malo anga obisalamo komanso chishango changa,+
115 Mukhale kutali ndi ine, anthu oipa inu,+
Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.
116 Inu Mulungu, ndithandizeni mogwirizana ndi zimene munalonjeza,*+
Kuti ndikhalebe ndi moyo.
Musalole kuti ndichite manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.*+
118 Onse amene amasochera nʼkusiya kutsatira malangizo anu mumawakana,+
Chifukwa ndi abodza komanso achinyengo.
119 Anthu onse oipa apadziko lapansi mumawataya ngati zinthu zopanda ntchito zimene zimatsalira poyenga zitsulo.+
Nʼchifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.
120 Chifukwa choopa inu, thupi langa limanjenjemera.
Ndikuopa zigamulo zanu.
ע [Ayin]
121 Ndachita zinthu zachilungamo komanso zoyenera.
Musandipereke kwa anthu amene amandipondereza.
122 Lonjezani kuti mudzandithandiza ine mtumiki wanu.
Musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
124 Ndisonyezeni chikondi chanu chokhulupirika ine mtumiki wanu,+
Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+
125 Ine ndine mtumiki wanu. Ndithandizeni kukhala wozindikira,+
Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.
126 Nthawi yoti Yehova achitepo kanthu yakwana,+
Chifukwa iwo aphwanya chilamulo chanu.
128 Choncho ndimaona kuti malangizo* onse ochokera kwa inu ndi abwino.+
Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+
פ [Pe]
129 Zikumbutso zanu nʼzodabwitsa.
Nʼchifukwa chake ine ndimazitsatira.
130 Mawu anu akafotokozedwa amathandiza munthu kuti akhale wozindikira,+
Amathandiza munthu wosadziwa zambiri kuti akhale wozindikira.+
132 Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima,+
Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu amene amakonda dzina lanu.+
133 Nditsogolereni ndi mawu anu kuti ndiyende mʼnjira yotetezeka.
Musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+
134 Ndipulumutseni* kwa anthu amene akundipondereza,
Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.
136 Misozi ikutsika mʼmaso mwanga ngati mtsinje
Chifukwa anthu sakusunga chilamulo chanu.+
צ [Tsade]
138 Zikumbutso zimene mumapereka ndi zolungama
Komanso nʼzodalirika kwambiri.
139 Kudzipereka kwanga kwa inu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga,+
Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.
141 Anthu ena amandiona ngati wopanda ntchito komanso wonyozeka.+
Komabe sindinaiwale malamulo anu.
143 Ngakhale kuti ndinakumana ndi zowawa komanso mavuto,
Ndinapitirizabe kukonda malamulo anu.
144 Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.
Ndithandizeni kukhala wozindikira+ kuti ndikhalebe ndi moyo.
ק [Qoph]
145 Ndaitana ndi mtima wanga wonse. Ndiyankheni inu Yehova.
Ndidzatsatira malangizo anu.
146 Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!
Ndidzasunga zikumbutso zanu.
147 Ndadzuka mʼbandakucha kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+
Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*
149 Imvani mawu anga chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+
Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.
150 Anthu amene amakonda kuchita khalidwe lochititsa manyazi* abwera pafupi ndi ine.
Iwo ndi otalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu.
152 Kale kwambiri, ndinaphunzira zokhudza zikumbutso zanu,
Kuti munazikhazikitsa kuti zikhalepo mpaka kalekale.+
ר [Resh]
153 Onani mavuto anga ndipo mundipulumutse,+
Chifukwa sindinaiwale chilamulo chanu.
154 Nditetezeni pa mlandu wanga* ndipo mundipulumutse.+
Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi lonjezo lanu.*
155 Chipulumutso chili kutali kwambiri ndi anthu oipa,
Chifukwa sanaphunzire malamulo anu.+
156 Chifundo chanu nʼchachikulu, inu Yehova.+
Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.
157 Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+
Koma ine sindinasiye kutsatira zikumbutso zanu.
158 Ndimanyansidwa ndi anthu ochita zinthu mwachinyengo,
Chifukwa sasunga mawu anu.+
159 Onani mmene ndimakondera malamulo anu.
Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+
160 Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,+
Ndipo zigamulo zanu zonse zolungama zidzakhalapo mpaka kalekale.
ש [Sin] kapena kuti [Shin]
162 Ndimasangalala ndi mawu anu,+
Mofanana ndi munthu amene wapeza chuma chambiri.
164 Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,
Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.
165 Anthu amene amakonda chilamulo chanu amakhala ndi mtendere wochuluka,+
Palibe chimene chingawakhumudwitse.*
166 Ndimayembekezera ntchito zanu zachipulumutso, inu Yehova,
Ndipo ndimatsatira malamulo anu.
167 Ndimasunga zikumbutso zanu,
Ndipo ndimazikonda kwambiri.+
168 Ndimasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,
Chifukwa inu mukudziwa zinthu zonse zimene ndimachita.+
ת [Taw]
169 Inu Yehova, imvani kulira kwanga kopempha thandizo.+
Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, mogwirizana ndi mawu anu.+
170 Pempho langa lakuti mundikomere mtima lifike kwa inu.
Ndipulumutseni mogwirizana ndi zimene munalonjeza.*
171 Milomo yanga isefukire ndi mawu okutamandani,+
Chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu.
172 Lilime langa liimbe zokhudza mawu anu,+
Chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.
174 Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,
Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+
175 Ndithandizeni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni,+
Zigamulo zanu zindithandize.