Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • nwt Joshua 1:1-24:33
  • Yoswa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yoswa
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Yoswa

YOSWA

1 Mose mtumiki wa Yehova atamwalira, Yehova anauza Yoswa*+ mwana wa Nuni, mtumiki+ wa Mose, kuti: 2 “Mose mtumiki wanga wamwalira.+ Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodano ndi kulowa mʼdziko limene ndikulipereka kwa Aisiraeli.+ 3 Malo alionse amene phazi lanu lidzapondapo ndidzakupatsani, mogwirizana ndi zimene ndinalonjeza Mose.+ 4 Dziko lanu lidzayambira kuchipululu kufika ku Lebanoni mpaka kumtsinje waukulu wa Firate, dziko lonse la Ahiti+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu* kumadzulo.+ 5 Palibe amene adzakugonjetse masiku onse a moyo wako.+ Ndidzakhala nawe ngati mmene ndinakhalira ndi Mose+ ndipo sindidzakutaya kapena kukusiya.+ 6 Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iweyo ndi amene utsogolere anthuwa kuti akatenge dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndidzawapatsa.+

7 Ukhale wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula. Usapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uzichita zinthu mwanzeru kulikonse kumene ungapite.+ 8 Buku la Chilamulo ili lisachoke pakamwa pako.+ Uziliwerenga ndi kuganizira mozama* masana ndi usiku, kuti uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo.+ Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.+ 9 Ndakulamula kale kuti ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, chifukwa Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene ungapite.”+

10 Kenako Yoswa analamula akapitawo a anthuwo kuti: 11 “Pitani mumsasa wonsewu, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani ndipo mupezeretu zinthu zonse zofunikira, chifukwa pakapita masiku atatu muwoloka Yorodano nʼkulowa mʼdzikolo kuti mukalitenge, dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.’”+

12 Ndiyeno Yoswa anauza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti: 13 “Kumbukirani mawu amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani+ akuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndipo wakupatsani dziko ili. 14 Akazi anu ndi ana anu atsale limodzi ndi ziweto zanu kutsidya lino la Yorodano,+ pamalo amene Mose wakupatsani. Koma asilikali amphamvu nonsenu,+ muwoloke ndipo muzikayenda patsogolo pa abale anu,+ mutakonzeka kumenya nkhondo. Muyenera kuwathandiza. 15 Yehova akadzapereka mpumulo kwa abale anu, ngati mmene waperekera kwa inu, nawonso abale anu akakatenga malo amene Yehova Mulungu akuwapatsa, mʼpamene inuyo mudzabwerere. Mudzabwerera kumalo anu amene Mose mtumiki wa Yehova wakugawirani, tsidya lino la Yorodano, kumʼmawa kuno.’”+

16 Iwo anayankha Yoswa kuti: “Zonse zimene mwatilamula tichita, ndipo kulikonse kumene mungatitumize tipita.+ 17 Tidzamvera chilichonse chimene mungatiuze ngati mmene tinkachitira ndi Mose. Yehova Mulungu wanu akhale nanu ngati mmene anakhalira ndi Mose.+ 18 Munthu aliyense wophwanya dala malamulo anu, ndi wosamvera mawu anu pa chilichonse chimene mungamulamule, aphedwe.+ Inuyo mukhale wolimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.”+

2 Tsopano Yoswa mwana wa Nuni anatuma amuna awiri mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu+ kuti akafufuze zokhudza dziko la Kanani. Anawauza kuti: “Pitani mukafufuze zokhudza dzikolo, makamaka mzinda wa Yeriko.” Choncho iwo anapita nʼkukafika kunyumba kwa mayi wina dzina lake Rahabi,+ yemwe anali hule, ndipo anakhala kumeneko. 2 Kenako mfumu ya Yeriko inauzidwa kuti: “Kwabwera Aisiraeli usiku uno kudzafufuza zokhudza dzikoli.” 3 Mfumu ya Yeriko itamva zimenezi, inatumiza anthu kukauza Rahabi kuti: “Tulutsa amuna amene abwera kuno ndipo ali mʼnyumba mwako, chifukwa abwera kudzafufuza dziko lonseli.”

4 Koma mayiyo anatenga amuna awiriwo nʼkuwabisa. Kenako anayankha kuti: “Nʼzoona, amunawo anabweradi, koma sindinadziwe kuti achokera kuti. 5 Mmene kumada, nthawi yotseka geti itayandikira, amunawo anatuluka. Sindikudziwa kumene alowera. Athamangireni mwamsanga. Muwapeza amenewo.” 6 (Koma iye anali atapita nawo padenga, nʼkuwabisa pansi pa mapesi a fulakesi* omwe anali padengapo.) 7 Anthuwo anathamangira amuna aja cha kowolokera mtsinje wa Yorodano.+ Ndipo atangotuluka pageti la mzinda, nthawi yomweyo getilo linatsekedwa.

8 Amuna aja asanagone, Rahabi anakwera padengapo. 9 Ndipo anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani dzikoli+ ndipo tonse tikuchita nanu mantha.+ Aliyense mʼdzikoli mtima wake suli mʼmalo chifukwa cha inu.+ 10 Tinamva mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamene munkachoka ku Iguputo.+ Komanso mmene munaphera mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya* kwa mtsinje wa Yorodano. 11 Titangomva zimenezi tinataya mtima,* ndipo chifukwa cha inu, palibe aliyense amene akulimba mtima. Ndithu, Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 12 Tsopano, chonde lumbirani pamaso pa Yehova, kuti chifukwa choti ndakusonyezani chikondi chokhulupirika, inunso mudzasonyeze anthu a mʼbanja la bambo anga chikondi chokhulupirika, ndipo mundipatse chizindikiro chodalirika. 13 Musadzaphe bambo anga, mayi anga, azichimwene anga ndi azichemwali anga limodzi ndi mabanja awo. Mudzatisiye amoyo.”+

14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe mʼmalo mwa inu. Mukapanda kuulula nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dzikoli, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima* ndipo tidzakhala okhulupirika.” 15 Kenako mayiyo anawapatsa chingwe ndipo iwo anatulukira pawindo pogwiritsa ntchito chingwecho, chifukwa mpanda wa mzindawo unalinso khoma la nyumba yake. Tingoti khoma la nyumba yakeyo linali mbali ya mpandawo.+ 16 Iye anauza amunawo kuti: “Muthawire kumapiri kuti amene akukusakani aja asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu, mpaka iwo atabwerako, kenako muzikapita kwanu.”

17 Amunawo anayankha kuti: “Tisungadi pangano limene watilumbiritsali, ndipo tidzakhala opanda mlandu+ 18 ngati pobwera tidzapeza utamangirira chingwe chofiirachi pawindo limene watitulutsirapoli. Uuze bambo ako, mayi ako, azichimwene ako, azichemwali ako ndi onse a mʼbanja la bambo ako kuti adzakhale mʼnyumba mwakomu.+ 19 Aliyense amene adzatuluke mʼnyumba yako kupita panja, magazi ake adzakhala pamutu pake ndipo ife tidzakhala opanda mlandu. Koma aliyense amene adzakhalebe nawe mʼnyumbamu akadzaphedwa, magazi ake adzakhala pamutu pathu. 20 Ndipo ngati ungaulule nkhaniyi,+ tidzakhalanso opanda mlandu pa pangano limene watilumbiritsali.” 21 Mayiyo anayankha kuti: “Zikhale momwemo.”

Atatero anawauza kuti azipita ndipo iwo ananyamuka. Kenako mayiyo anamanga chingwe chofiira chija pawindopo. 22 Choncho amuna aja anapita kumapiri ndipo anakhala kumeneko masiku atatu mpaka anthu owasakawo atabwerera. Owasakawo anali atawafunafuna mumsewu uliwonse, koma osawapeza. 23 Amuna awiri aja anachoka kumapiriko, ndipo anawoloka mtsinje nʼkukafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Atafika anamufotokozera zonse zimene zinawachitikira. 24 Iwo anauza Yoswa kuti: “Yehova wapereka dziko lonselo mʼmanja mwathu.+ Ndipo anthu onse a mʼdzikomo akuchita mantha chifukwa cha ife.”+

3 Mʼmamawa kutacha, Yoswa ndi Aisiraeli* onse ananyamuka ku Sitimu+ nʼkuyenda kukafika kumtsinje wa Yorodano. Iwo anagona kumeneko asanawoloke.

2 Patatha masiku atatu, akapitawo+ a anthuwo anapita mumsasa wonse, 3 ndipo anauza anthuwo kuti: “Mukangoona likasa la pangano la Yehova Mulungu wanu litanyamulidwa ndi Alevi omwe anali ansembe,+ musamuke pamalo panu nʼkuyamba kulitsatira, 4 koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi likasalo pakhale mtunda wokwana mikono pafupifupi 2,000.* Mukatero mudzadziwa koyenera kupita, chifukwa kumeneko simunayambe mwapitako.”

5 Tsopano Yoswa anauza anthuwo kuti: “Mudziyeretse,+ chifukwa mawa Yehova akuchitirani zinthu zodabwitsa.”+

6 Kenako Yoswa anauza ansembe kuti: “Nyamulani likasa+ la pangano ndipo muziyenda patsogolo pa anthuwa.” Choncho ansembewo ananyamula likasa la panganolo nʼkumayenda patsogolo pa anthuwo.

7 Ndipo Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndiyamba kukulemekeza pamaso pa Aisiraeli onse+ nʼcholinga choti adziwe kuti ndidzakhala nawe+ ngati mmene ndinkachitira ndi Mose.+ 8 Ulamule ansembe onyamula likasa la pangano kuti: ‘Mukakafika mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano, mukalowe mʼmadzimo nʼkuima.’”+

9 Ndiyeno Yoswa anauza Aisiraeli kuti: “Bwerani kuno mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu.” 10 Kenako Yoswa anati: “Mukaona zimene zichitike pano, mudziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu+ ndipo adzathamangitsadi Akanani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.+ 11 Likasa la pangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi liyenda patsogolo panu kulowa mumtsinje wa Yorodano. 12 Tsopano tengani amuna 12 mʼmafuko a Isiraeli, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.+ 13 Zimene zichitike nʼzakuti, mapazi a ansembe onyamula likasa la Yehova, Ambuye wa dziko lonse lapansi, akangoponda mʼmadzi a mumtsinje wa Yorodano, madzi ochokera kumtunda aima nʼkukhala ngati khoma.”+

14 Choncho anthuwo anachotsa mahema awo, nʼkunyamuka kuti awoloke Yorodano, ndipo ansembe onyamula likasa+ la pangano anali patsogolo pawo. 15 Onyamula Likasawo atangofika pamtsinje wa Yorodano, nʼkuponda madzi a mʼmphepete mwake (mtsinje wa Yorodano unkasefukira+ nyengo yonse yokolola), 16 madzi ochokera kumtunda anaima ngati khoma. Ndipo anakhala ngati damu lomwe linasefukira mpaka kukafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu, mzinda woyandikana ndi mzinda wa Zeretani. Koma madzi akumunsi omwe ankapita kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere,* anaphwa. Choncho, madzi a mtsinjewo anagawikana, ndipo anthuwo anawolokera kutsidya lina, pafupi ndi Yeriko. 17 Ansembe onyamula likasa la pangano la Yehova anaima panthaka youma+ pakati pa mtsinje wa Yorodano. Anaimabe choncho pamene Aisiraeli onse ankawoloka panthaka youmayo,+ mpaka mtundu wonse unawoloka mtsinje wa Yorodano.

4 Mtundu wonse utangomaliza kuwoloka mtsinje wa Yorodano, Yehova anauza Yoswa kuti: 2 “Tenga amuna 12 pakati pa anthuwa, mwamuna mmodzi pa fuko lililonse.+ 3 Uwalamule kuti, ‘Pitani pakati pa mtsinje wa Yorodano, pamene ansembe aima+ ndipo mukatengepo miyala 12 nʼkupita nayo kumene mukagone usiku wa lero.’”+

4 Choncho Yoswa anaitana amuna 12 amene anawasankha pakati pa Aisiraeli, mwamuna mmodzi pa fuko lililonse. 5 Ndipo anawauza kuti: “Dutsani kutsogolo kwa Likasa la Yehova Mulungu wanu, mukafike pakati pa mtsinje wa Yorodano. Aliyense akanyamule mwala umodzi paphewa pake, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Aisiraeli. 6 Miyalayo idzakhala chizindikiro kwa inu. Ana anu* akamadzafunsa mʼtsogolo muno kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 7 Muzidzawauza kuti: ‘Nʼchifukwa chakuti madzi amumtsinje wa Yorodano anagawikana chifukwa cha likasa+ la pangano la Yehova. Likasalo likudutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinjewo anagawikana. Miyalayi ndi yoti izikumbutsa Aisiraeli zimenezo mpaka kalekale.’”+

8 Choncho Aisiraeliwo anachita zimene Yoswa anawalamula. Anapita pakati pa mtsinje wa Yorodano, ndipo anakanyamula miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Aisiraeli, ngati mmene Yehova analamulira Yoswa. Ananyamula miyalayo nʼkupita nayo kumalo amene anagona.

9 Komanso Yoswa anatenga miyala 12 nʼkuisanja pakati pa mtsinje wa Yorodano, pamalo amene ansembe onyamula likasa la pangano anaima.+ Miyalayo ilipo mpaka lero.

10 Ansembe onyamula Likasawo, anaimabe pakati pa mtsinje wa Yorodano, mpaka zonse zimene Yehova analamula Yoswa kuti auze anthuwo zitachitika, mogwirizana ndi zonse zimene Mose analamula Yoswa. Ansembewo ali chiimire choncho, anthuwo anawoloka mtsinjewo mofulumira. 11 Anthu onse atangotha kuwoloka, Likasa la Yehova linawoloka litanyamulidwa ndi ansembewo, anthu onsewo akuona.+ 12 Anthu a fuko la Rubeni, a fuko la Gadi komanso hafu ya fuko la Manase, anawoloka nʼkumayenda patsogolo pa Aisiraeli ena atakonzekera kumenya nkhondo,+ ngati mmene Mose anawalangizira.+ 13 Amuna pafupifupi 40,000 onyamula zida anawoloka nʼkupita kuchipululu cha Yeriko, ndipo Yehova anali nawo.

14 Pa tsikuli, Yehova anachititsa Aisiraeli onse kuona kuti Yoswa ndi mtsogoleri wamkulu,+ ndipo anayamba kumulemekeza* kwambiri masiku onse a moyo wake ngati mmene ankalemekezera Mose.+

15 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: 16 “Lamula ansembe onyamula likasa+ la Umboni kuti achoke mumtsinje wa Yorodano.” 17 Choncho Yoswa analamula ansembewo kuti: “Tulukani mumtsinje wa Yorodano.” 18 Ansembe onyamula likasa+ la pangano la Yehova atachoka pakati pa mtsinje wa Yorodano, komanso mapazi awo atangoponda pamtunda, madzi a mtsinjewo anayambanso kuyenda ndipo anasefukira mbali zonse+ ngati poyamba.

19 Anthuwo anawoloka mtsinje wa Yorodano pa tsiku la 10 la mwezi woyamba ndipo anakamanga msasa ku Giligala,+ kumalire a kumʼmawa kwa Yeriko.

20 Miyala 12 imene anaitenga mumtsinje wa Yorodano ija, Yoswa anaisanja ku Giligala.+ 21 Kenako anauza Aisiraeli kuti: “Mʼtsogolomu ana anu akamadzafunsa abambo awo kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 22 Muzidzauza anawo kuti, ‘Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano panthaka youma.+ 23 Izi zinachitika pamene Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano, mpaka iwo atawoloka. Zinachitika mofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anachita pa Nyanja Yofiira, pamene anaphwetsa madzi a nyanjayo, mpaka onse atawoloka.+ 24 Yehova anachita zimenezi kuti anthu onse apadziko lapansi adziwe kuti dzanja lake ndi lamphamvu,+ ndiponso kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.’”

5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali mʼmbali mwa nyanja, anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano mpaka Aisiraeli onse atawoloka. Atangomva zimenezo, anachita mantha kwambiri,*+ moti analibenso mphamvu chifukwa choopa Aisiraeli.+

2 Pa nthawi imeneyo, Yehova anauza Yoswa kuti: “Panga timipeni tamiyala ndipo udule khungu+ amuna a Chiisiraeli kachiwiri.” 3 Choncho Yoswa anapanga timipeni tamiyala nʼkudula amuna a Chiisiraeli. Zimenezi zinachitikira ku Gibeyati-haaraloti.*+ 4 Yoswa anawadula chifukwa chakuti amuna onse amene anatuluka mu Iguputo, onse otha kupita kunkhondo,* anali atafera mʼchipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo.+ 5 Anthu onse amene anachoka ku Iguputo anali odulidwa. Koma onse amene anabadwira mʼchipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo, anali asanadulidwe. 6 Aisiraeliwo anayenda mʼchipululu zaka 40,+ mpaka anthu onse amene anatuluka mu Iguputo, amene sanamvere mawu a Yehova+ atatha kuphatikizapo amuna onse otha kupita kunkhondo. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 7 Iye analowetsa mʼdzikomo ana awo mʼmalo mwa iwowo.+ Ana amenewa Yoswa anawadula, chifukwa sanadulidwe pa nthawi imene anali pa ulendo.

8 Atamaliza kudula amuna onse, aliyense anakhalabe muhema wake pamsasapo mpaka atachira.

9 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndachititsa kuti Aiguputo asamakunyozeninso.”* Choncho malowo amawatchula kuti Giligala,*+ mpaka lero.

10 Aisiraeliwo anakhalabe ku Giligala ndipo anachita Pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ mʼchipululu cha Yeriko. 11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za mʼdzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda zofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene Aisiraeli anadya zokolola za mʼdzikomo. Kuyambira pamenepo, sipankakhalanso mana oti Aisiraeli azidya.+ Choncho chaka chimenechi nʼchimene iwo anayamba kudya zokolola za mʼdziko la Kanani.+

13 Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima patsogolo pake, atanyamula lupanga mʼmanja.+ Yoswa anamuyandikira nʼkumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” 14 Munthuyo anayankha kuti: “Ayi, ndabwera chifukwa ndine kalonga* wa gulu lankhondo la Yehova.”+ Atatero, Yoswa anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamuuza kuti: “Lankhulani mbuyanga kwa kapolo wanu.” 15 Ndiyeno kalonga wa gulu lankhondo la Yehovayo anauza Yoswa kuti: “Vula nsapato zako, chifukwa malo amene waimawo ndi oyera.” Nthawi yomweyo, Yoswa anavula nsapato zake.+

6 Mzinda wa Yeriko unatsekedwa mwamphamvu chifukwa cha Aisiraeli. Palibe amene ankatuluka kapena kulowa mumzindawo.+

2 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Mzinda wa Yeriko ndaupereka mʼmanja mwako, pamodzi ndi mfumu yake ndi asilikali ake amphamvu.+ 3 Asilikali nonsenu muziguba kuzungulira mzindawu kamodzi pa tsiku, ndipo muchite zimenezi kwa masiku 6. 4 Ansembe 7 aziyenda patsogolo pa Likasa atanyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo. Pa tsiku la 7 mudzagube kuzungulira mzindawo maulendo 7, ansembewo akuliza malipenga.+ 5 Ansembewo akadzaliza malipenga a nyanga za nkhosa pa ulendo wa 7, ndipo inu mukadzamva kulira kwa malipengawo, nonse mudzafuule mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wonse wa mzindawo udzagwa mpaka pansi.+ Pamenepo, nonsenu mudzathamangire kumeneko.”

6 Choncho Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe nʼkuwauza kuti: “Nyamulani likasa la pangano, ndipo ansembe 7 aziyenda patsogolo pa Likasa la Yehovalo. Ansembewo atenge malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo.”+ 7 Anauzanso asilikali kuti: “Nyamukani, mukagube kuzungulira mzindawo. Gulu la asilikali onyamula zida zankhondo+ likhale patsogolo pa Likasa la Yehova.” 8 Monga Yoswa ananenera, ansembe 7 ananyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa pamaso pa Yehova. Iwo anatsogola akuliza malipengawo, ndipo likasa la pangano la Yehova linkabwera pambuyo pawo. 9 Gulu la asilikali onyamula zida linkayenda patsogolo pa ansembe oimba malipenga, pamene gulu lina la asilikali linkabwera pambuyo pa Likasa, uku malipenga aja akuimbidwa mosalekeza.

10 Yoswa analamula asilikaliwo kuti: “Musafuule kapena kulankhula kanthu, ndipo pakamwa panu pasatuluke mawu alionse mpaka tsiku limene ndidzakuuzani kuti, ‘Fuulani!’ Pamenepo mudzafuule.” 11 Choncho iye atalamula, Likasa la Yehova linazungulira mzindawo kamodzi, asilikaliwo akuguba nalo. Kenako iwo anabwerera kumsasa ndipo anakhala kumeneko usiku wonse.

12 Tsiku lotsatira, Yoswa anadzuka mʼmawa kwambiri, ndipo ansembe ananyamula Likasa+ la Yehova. 13 Ansembe 7 onyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa, omwe ankakhala patsogolo pa Likasa la Yehova, ankayenda akuliza malipenga mosalekeza. Patsogolo pawo panali gulu la asilikali onyamula zida, ndipo pambuyo pa Likasa la Yehova pankabwera asilikali ena, uku malipenga akulira mosalekeza. 14 Iwo anagubanso kuzungulira mzindawo kamodzi pa tsiku lachiwirili ndipo atamaliza anabwerera kumsasa. Anachita zimenezi kwa masiku 6.+

15 Pa tsiku la 7, anadzuka mʼmamawa kwambiri ndipo anaguba kuzungulira mzindawo ngati mmene ankachitira. Pa tsikuli anazungulira mzindawo maulendo 7.+ 16 Pa ulendo wa 7, ansembe aja analiza malipenga awo, ndipo Yoswa anauza asilikaliwo kuti: “Fuulani!+ Chifukwa Yehova wakupatsani mzindawu! 17 Mzindawu komanso zinthu zonse zimene zilimo ziyenera kuwonongedwa,+ zonse ndi za Yehova. Rahabi+ yekha, hule uja, musamuphe. Mumusiye pamodzi ndi onse amene ali nawo mʼnyumba mwake, chifukwa iye anabisa anthu amene tinawatuma.+ 18 Koma zinthu zoyenera kuwonongedwa musamale nazo,+ kuopera kuti mungazisirire nʼkuzitenga+ chifukwa mukatero, mudzabweretsa tsoka pamsasa wa Isiraeli ndipo nawonso udzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa.+ 19 Koma siliva yense, golide yense ndiponso zipangizo zonse zamkuwa ndi zachitsulo, nʼzopatulika kwa Yehova.+ Ziyenera kukaikidwa mosungiramo chuma cha Yehova.”+

20 Ansembe aja ataliza malipenga, asilikali nʼkumva kulira kwa malipengawo, asilikaliwo anafuula mwamphamvu+ mfuu yankhondo ndipo mpanda wa mzindawo unagwa mpaka pansi.+ Zitatero, iwo analowa mumzindawo. Aliyense anathamangira kumeneko nʼkulanda mzindawo. 21 Aliyense amene anali mumzindawo anamupha ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, anyamata ndi anthu okalamba omwe. Anaphanso ngʼombe, nkhosa ndi abulu.+

22 Yoswa anauza amuna awiri aja amene anawatuma kukafufuza zokhudza dzikolo, kuti: “Pitani kunyumba kwa hule uja ndipo mukamutulutse limodzi ndi onse amene ali mʼnyumba mwake, mogwirizana ndi zimene munalumbira kwa iye.”+ 23 Choncho, anyamata amene anakafufuza zokhudza dziko aja, anapita kukatulutsa Rahabi limodzi ndi bambo ake, mayi ake, azichimwene ake ndi onse amene anali naye. Anatulutsa achibale ake onse,+ ndipo anayenda nawo bwinobwino kupita nawo kumalo ena kunja kwa msasa wa Isiraeli.

24 Atatero, anatentha mzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo. Koma siliva, golide ndiponso zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, anakaziika mosungiramo chuma cha Yehova.+ 25 Yoswa anangosiya Rahabi hule uja limodzi ndi anthu amʼnyumba ya bambo ake komanso onse amene anali naye.+ Mayiyo akukhalabe ndi Aisiraeli mpaka lero+ chifukwa anabisa anthu amene Yoswa anawatuma kukafufuza zokhudza Yeriko.+

26 Pa nthawiyo Yoswa analumbira* kuti: “Munthu amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu adzakhale wotembereredwa pamaso pa Yehova. Akadzangoyala maziko ake, mwana wake woyamba adzafe, ndipo akadzaika zitseko zapageti, mwana wake wotsiriza adzafe.”+

27 Choncho Yehova anali ndi Yoswa,+ ndipo mbiri yake inamveka padziko lonse.+

7 Kenako Aisiraeli anachita zinthu zosakhulupirika potenga zinthu zoyenera kuwonongedwa. Akani+ mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatenga zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Chifukwa cha zimenezi, Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli.+

2 Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni, kumʼmawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani mukafufuze zokhudza mzindawu.” Amunawo anapita nʼkukafufuza zokhudza mzinda wa Ai. 3 Amunawo atabwerako anauza Yoswa kuti: “Musachite kutumiza anthu onse kumeneko. Amuna pafupifupi 2,000 kapena 3,000, akhoza kugonjetsa Ai. Musatopetse anthu onse kuti apite kumeneko, chifukwa kuli anthu ochepa.”

4 Choncho amuna pafupifupi 3,000 okha anapita ku Ai, koma anathamangitsidwa ndi amuna a kumeneko.+ 5 Ndipo amuna a Chiisiraeli 36 anaphedwa. Anthu a ku Ai anawathamangitsa kuchokera pageti kutsetsereka mpaka kukafika ku Sebarimu. Ndipo ankawapha mʼnjira yonse. Zitatero, Aisiraeli anachita mantha kwambiri.

6 Zimenezi zitachitika, Yoswa anangʼamba zovala zake ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi patsogolo pa Likasa la Yehova, mpaka madzulo. Anachita zimenezi pamodzi ndi akulu a Isiraeli, nʼkumadzithira fumbi kumutu. 7 Ndipo Yoswa anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nʼchifukwa chiyani mwalola kuti anthu ayende mtunda wonsewu mpaka kuwoloka mtsinje wa Yorodano, nʼkudzatipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiphe? Zikanakhala bwino tikanangokhala kutsidya lina lija la Yorodano! 8 Pepanitu Yehova, ndingatinso chiyani nanga, poti Isiraeli wathawa pamaso pa adani ake? 9 Akanani ndi anthu onse a mʼdzikoli adzamva zimenezi, ndipo adzabwera nʼkufafaniza dzina lathu padziko lapansi. Ndiye mudzateteza bwanji dzina lanu lalikulu?”+

10 Yehova anauza Yoswa kuti: “Tadzuka iwe! Nʼchifukwa chiyani wadzigwetsa mpaka nkhope yako pansi? 11 Aisiraeli achimwa ndiponso aphwanya pangano+ limene ndinawalamula kuti alisunge. Iwo atenga zina mwa zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Aba+ zinthuzo ndi kuzibisa pakati pa katundu wawo.+ 12 Choncho Aisiraeli sadzathanso kulimbana ndi adani awo. Iwo azingogonja nʼkumathawa adani awo, chifukwa nawonso akhala zinthu zoyenera kuwonongedwa. Sindikhalanso nanu kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo.+ 13 Dzuka ndipo uyeretse anthuwa.+ Uwauze kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera mawa, chifukwa Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Anthu inu pakati panu pali zinthu zoyenera kuwonongedwa. Simudzathanso kulimbana ndi adani anu, pokhapokha mutachotsa zinthu zoyenera kuwonongedwazo. 14 Mawa mʼmawa, mubwere mafuko onse. Fuko limene Yehova adzasankhe+ lidzabwera patsogolo. Kenako mbumba ndi mbumba, ndipo mbumba imene Yehova adzasankhe idzabwera patsogolo. Kenako banja ndi banja, ndipo banja limene Yehova adzasankhe lidzabwera patsogolo, kenako mwamuna aliyense payekhapayekha. 15 Amene apezeke ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo, adzatenthedwa ndi moto,+ limodzi ndi banja lake komanso zinthu zake zonse. Adzatenthedwa chifukwa waphwanya pangano+ la Yehova ndiponso wachita choipa chochititsa manyazi mu Isiraeli.”’”

16 Ndiyeno Yoswa anadzuka mʼmawa kwambiri, nʼkuuza Aisiraeli kuti afike pamaso pa Mulungu, fuko ndi fuko, ndipo fuko la Yuda linasankhidwa. 17 Kenako anauza mabanja a mʼfuko la Yuda kufika pamaso pa Mulungu, ndipo banja la Zera+ linasankhidwa. Kenako anauza banja la Zera kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense payekhapayekha, ndipo Zabidi anasankhidwa. 18 Potsirizira pake anauza a mʼbanja la Zabidi kufika pamaso pa Mulungu, mwamuna aliyense payekhapayekha. Ndipo Akani mwana wa Karami, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anasankhidwa.+ 19 Tsopano Yoswa anauza Akani kuti: “Mwana wanga, chonde, lemekeza Yehova Mulungu wa Isiraeli, ulula kwa iye. Tandiuza chonde, wachita chiyani? Usandibisire.”

20 Akani anayankha Yoswa kuti: “Ndithudi, ineyo ndi amene ndachimwira Yehova Mulungu wa Isiraeli. Zimene ndinachita ndi izi: 21 Pakati pa zinthu zoyenera kuwonongedwa ndinaonapo chovala chokongola komanso chamtengo wapatali cha ku Sinara,+ masekeli* a siliva 200 komanso mtanda umodzi wa golide wolemera masekeli 50. Nditaziona ndinazisirira ndipo ndinazitenga. Panopa chovalacho ndi ndalamazo ndazikumbira pansi, pakati pa tenti yanga, ndipo ndalamazo zili pansi pa chovalacho.”

22 Nthawi yomweyo Yoswa anatuma anthu, amene anathamangira kutentiko. Iwo anachipezadi chovalacho mʼhema wake, ndipo ndalama zinali pansi pake. 23 Anthuwo anatenga zinthuzo muhemayo ndipo anabwera nazo kwa Yoswa ndi Aisiraeli onse nʼkuziika pansi, pamaso pa Yehova. 24 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anatenga Akani+ mwana wa Zera, limodzi ndi siliva uja, chovala chamtengo wapatali chija, mtanda wa golide uja,+ komanso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu, nkhosa, ndiponso hema wake, ndi chilichonse chomwe chinali chake, nʼkupita nawo kuchigwa cha Akori.+ 25 Ndiyeno Yoswa anati: “Nʼchifukwa chiyani watibweretsera tsoka?*+ Lero Yehova akubweretsera iweyo tsoka.” Atatero, Aisiraeli onse anayamba kuwaponya miyala+ anthuwo ndipo kenako anawatentha ndi moto.+ Umu ndi mmene anawaphera, anawaponya miyala. 26 Pambuyo pake, anaunjika mulu waukulu wa miyala pa iye. Muluwo ulipo mpaka lero. Zitatero, mkwiyo waukulu wa Yehova unatha.+ Nʼchifukwa chake malowo amatchedwa chigwa cha Akori* mpaka lero.

8 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Usaope kapena kuchita mantha.+ Tenga amuna onse ankhondo ndipo upite kukamenyana ndi mzinda wa Ai. Dziwa kuti mfumu ya Ai ndaipereka kwa iwe limodzi ndi anthu ake, mzinda wake komanso dera lake lonse.+ 2 Ukachitire mzinda wa Ai ndi mfumu yake zimene unachitira mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto zamumzindawo mukatenge zikhale zanu. Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”

3 Choncho Yoswa ndi amuna onse ankhondo ananyamuka kupita kukamenyana ndi mzinda wa Ai. Yoswa anasankha asilikali amphamvu ndi olimba mtima okwanira 30,000, nʼkuwatumiza usiku. 4 Anawalamula kuti: “Inu mukabisale kumbuyo kwa mzindawo. Musakakhale patali kwambiri ndi mzindawo, ndipo nonsenu mukakhale okonzeka. 5 Koma ine ndi onse amene ndikakhale nawo, tikafika pafupi kwambiri ndi mzindawo. Iwo akakatuluka kuti adzamenyane nafe ngati poyamba paja,+ tikayamba kuthawa. 6 Akakaona kuti tikuthawa, akatithamangitsa. Tikapitiriza kuthawa kuti tikawatulutse mpaka akafike kutali ndi mzindawo, chifukwa akaganiza kuti, ‘Akuthawa ngati poyamba paja.’+ 7 Zikakatero, inu mukavumbuluke nʼkulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu mʼmanja mwanu. 8 Ndipo mukakangolanda mzindawo, mukauyatse moto.+ Mukachite zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova. Ndakulamulani kuti mukachite zimenezi.”

9 Kenako Yoswa anatumiza amunawo ndipo anapita kukabisala. Iwo anakabisala pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma usiku umenewo Yoswa anagona limodzi ndi asilikali amene anali nawo.

10 Yoswa anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkusonkhanitsa asilikaliwo. Atatero ananyamuka ndipo iye limodzi ndi akulu a Isiraeli anatsogolera asilikaliwo ku Ai. 11 Asilikali onse+ amene anali ndi Yoswa anayenda nʼkukafika pafupi ndi mzindawo, kutsogolo kwake. Atafika anamanga msasa kumpoto kwa Ai, ndipo pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12 Pa nthawiyi anali atatumiza amuna pafupifupi 5,000 ndipo anali atabisala+ pakati pa Beteli+ ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda wa Ai. 13 Choncho asilikali ambiri anamanga msasa wawo kumpoto kwa mzindawo,+ ndipo ochepa anamanga kumadzulo kwa mzindawo.+ Usikuwo Yoswa ananyamuka nʼkupita pakati pa chigwa chija.

14 Tsopano mfumu ya Ai itaona zimenezo, nthawi yomweyo mfumuyo ndi amuna amumzindawo anakonzeka kuti akamenyane ndi Aisiraeli. Anadzuka mʼmamawa kukakumana nawo pamalo ena pomwe ankatha kuona bwino chigwa cha mʼchipululu. Koma mfumuyo sinadziwe kuti asilikali ena anali atabisala kumbuyo kwa mzindawo. 15 Amuna a ku Ai atawaukira, Yoswa ndi Aisiraeli onse anayamba kuthawa kudzera njira yolowera kuchipululu.+ 16 Zitatero, anthu onse amumzindawo anaitanidwa kuti akathamangitse Aisiraeli. Anthuwo anathamangitsa Aisiraeliwo ndi Yoswa, mpaka anafika kutali ndi mzindawo. 17 Panalibe mwamuna ndi mmodzi yemwe amene anatsala ku Ai ndi ku Beteli. Onse anapita kukathamangitsa Aisiraeli, ndipo mageti a mzindawo anangowasiya osatseka.

18 Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Loza mzinda wa Ai ndi nthungo* imene ili mʼmanja mwako,+ chifukwa ndiupereka mʼmanja mwako.”+ Choncho Yoswa analoza mzindawo ndi nthungo imene inali mʼmanja mwake. 19 Atangouloza, asilikali amene anabisala aja anavumbuluka nʼkuthamangira kumzindawo ndipo anaulanda. Nthawi yomweyo anauyatsa moto.+

20 Amuna a ku Ai atatembenuka anangoona utsi uli tolo mumzindawo, ndipo analibiretu mphamvu zoti nʼkuthawira kulikonse. Kenako asilikali a Chiisiraeli amene ankathawira kuchipululu aja, anatembenukira amuna a ku Aiwo. 21 Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye ataona kuti asilikali omwe anabisala aja alanda mzindawo, ndiponso ataona utsi mumzindawo, anatembenukira amuna a ku Ai nʼkuyamba kuwapha. 22 Ndiyeno asilikali amene analanda mzinda aja anatuluka mumzindamo kudzamenyana ndi amuna a ku Aiwo. Choncho amuna a ku Ai anali pakati pa Aisiraeli, ena mbali ino, ena mbali inayo. Aisiraeliwo anapha amuna a ku Ai, moti palibe amene anatsala kapena kuthawa.+ 23 Koma mfumu ya ku Ai+ anaigwira nʼkupita nayo kwa Yoswa.

24 Aisiraeli anapha ndi lupanga amuna onse ankhondo a ku Ai kuchipululu kumene anthu a ku Aiwo anawathamangitsirako. Atatero, Aisiraeliwo anabwerera ku Ai nʼkukapha ndi lupanga ena onse otsala. 25 Anthu onse amene anaphedwa tsikulo, amuna ndi akazi, anakwana 12,000, anthu onse a ku Ai. 26 Ndipo Yoswa sanatsitse mkono wake umene anagwiritsa ntchito poloza mzindawo ndi nthungo+ mpaka anthu onse a ku Ai ataphedwa.+ 27 Koma Aisiraeliwo anatenga ziweto ndi katundu wamumzindawo nʼkukhala zawo, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Yoswa.+

28 Ndiyeno Yoswa anatentha mzinda wa Ai nʼkuusiya uli bwinja loti lidzakhala choncho mpaka kalekale,+ ndipo lilipobe mpaka lero. 29 Mfumu ya Ai anaipachika pamtengo mpaka madzulo. Koma dzuwa litatsala pangʼono kulowa, Yoswa analamula kuti achotse mtembo wa mfumuyo pamtengopo.+ Atauchotsa anakauponya pageti la mzindawo nʼkuunjikapo mulu waukulu wa miyala, ndipo muluwo ulipo mpaka lero.

30 Nthawi imeneyi ndi imene Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Isiraeli guwa lansembe pa Phiri la Ebala.+ 31 Anamanga guwalo mogwirizana ndi zimene Mose mtumiki wa Yehova analamula Aisiraeli, mogwirizananso ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la Chilamulo+ cha Mose kuti: “Guwa lansembe la miyala yathunthu ndiponso yosasema ndi chipangizo chachitsulo.”+ Ndipo iwo anaperekapo kwa Yehova nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano.+

32 Kenako Yoswa analemba pamiyala Chilamulo+ chimene Mose analembera Aisiraeli.+ 33 Aisiraeli onse, atsogoleri awo, akapitawo awo, ndi oweruza awo anasonkhanitsidwa pamodzi. Panalinso alendo ndi nzika.+ Ena anaima mbali iyi ya Likasa, ena anaima mbali inayo, pamaso pa Alevi omwe anali ansembe amene ananyamula likasa la pangano la Yehova. Hafu ya anthuwo inaima mʼphiri la Gerizimu, ndipo hafu ina inaima mʼphiri la Ebala,+ (ngati mmene Mose mtumiki wa Yehova analamulira),+ kuti Aisiraeliwo adalitsidwe. 34 Zimenezi zitatha, Yoswa anawerenga mokweza mawu onse a Chilamulo,+ madalitso+ ndi matemberero,+ mogwirizana ndi zonse zolembedwa mʼbuku la Chilamulo. 35 Panalibe ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene Mose analamula, amene Yoswa sanawawerenge mokweza pamaso pa mpingo wonse wa Aisiraeli.+ Panalinso akazi ndi ana, komanso alendo+ okhala pakati pawo.+

9 Mafumu onse amene anali kumadzulo kwa Yorodano+ anamva zimene zinachitika. Amenewa anali mafumu a Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ Iwo ankakhala kudera lamapiri, ku Sefela ndiponso mʼmbali monse mwa Nyanja Yaikulu*+ komanso pafupi ndi Lebanoni. Mafumuwa atangomva zimene zinachitikazo, 2 anapanga mgwirizano kuti amenyane ndi Yoswa ndi Isiraeli.+

3 Nawonso anthu a ku Gibiyoni+ anamva zimene Yoswa anachita ku Yeriko+ ndi ku Ai.+ 4 Choncho anachita zinthu mwanzeru. Anaika chakudya mʼmatumba akutha nʼkukweza pa abulu. Ananyamulanso vinyo mʼmatumba achikopa akutha, atawasoka mongʼambika. 5 Anavalanso nsapato zakutha atazisokasoka ndiponso zovala zakutha. Mkate wonse umene anatenga unali wouma ndipo unkangoyoyoka. 6 Kenako anapita kwa Yoswa kumsasa ku Giligala,+ ndipo anamuuza iyeyo ndi amuna a Chiisiraeli kuti: “Tachokera kudziko lakutali kwambiri. Chonde muchite nafe pangano.” 7 Koma amuna a Chiisiraeli anayankha Ahiviwo+ kuti: “Mwina mumakhala chakonkuno. Ndiye tingachite nanu bwanji pangano?”+ 8 Iwo anayankha Yoswa kuti: “Ndife akapolo* anu.”

Ndiyeno Yoswa anawafunsa kuti: “Koma ndinu ndani, ndipo mwachokera kuti?” 9 Iwo anamuyankha kuti: “Akapolo anufe tachokera kudziko lakutali kwambiri.+ Tabwera chifukwa tamva za dzina la Mulungu wanu, Yehova. Tamva mbiri yake ndi zonse zimene anachita ku Iguputo.+ 10 Tamvanso zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kutsidya lina* la Yorodano, omwe ndi Mfumu Sihoni+ ya ku Hesiboni ndi Mfumu Ogi+ ya ku Basana, imene inali ku Asitaroti. 11 Choncho akulu akwathu ndi anthu onse amʼdziko lathu anatiuza kuti, ‘Tengani chakudya cha pa ulendo ndipo mupite kukakumana nawo. Mukawauze kuti: “Ife ndife akapolo anu.+ Chonde muchite nafe pangano.”’+ 12 Pamene tinkanyamuka kubwera kuno, mkate wathuwu unali wotentha. Koma mutha kuona kuti wauma ndipo ukungoyoyoka.+ 13 Ndipo matumba achikopa a vinyowa anali atsopano pamene timathiramo vinyo, koma tsopano angʼambika.+ Onaninso zovala ndi nsapato zathuzi, zangʼambika chifukwa cha kutalika kwa ulendo.”

14 Ndiyeno amuna a Chiisiraeli anatengako zakudyazo nʼkuziyangʼanitsitsa, koma sanafunsire kwa Yehova.+ 15 Choncho Yoswa anagwirizana nawo za mtendere,+ ndipo anachita nawo pangano kuti sawapha. Zitatero, atsogoleri a Isiraeli analumbira kwa anthuwo.+

16 Koma patapita masiku atatu atachita nawo panganolo, anamva kuti anthuwo ankakhala pafupi, mʼdera lomwelo. 17 Aisiraeliwo ananyamuka nʼkukafika kumizinda ya anthuwo pa tsiku lachitatu. Mizindayo inali Gibiyoni,+ Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-yearimu.+ 18 Koma Aisiraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalumbirira anthuwo mʼdzina la Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli. Choncho gulu lonse linayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi atsogoleriwo. 19 Ndiyeno atsogoleri onse anauza gululo kuti: “Ife tinawalumbirira mʼdzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndiye sitingawaphe. 20 Tipanga chonchi: Tiwasiya kuti akhale ndi moyo, kuti Mulungu asatikwiyire popeza tinawalumbirira.”+ 21 Atsogoleriwo ananenanso kuti: “Asaphedwe, koma azitola nkhuni ndiponso kutungira madzi gulu lonse la Aisiraeli.” Izi ndi zimene atsogoleriwo anawalonjeza.

22 Kenako Yoswa anaitana anthuwo nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani munatipusitsa nʼkumanena kuti ‘Timakhala kutali kwambiri ndi inu,’ chonsecho mumakhala pafupi?+ 23 Tsopano mukhala anthu otembereredwa.+ Mukhala akapolo ndipo muzitola nkhuni ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.” 24 Anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Akapolo anufe tinauzidwa mosapita mʼmbali kuti Yehova Mulungu wanu analamula mtumiki wake Mose kuti akupatseni dziko lonseli ndiponso muphe anthu onse okhalamo.+ Choncho tinachita mantha kuti mutipha.+ Nʼchifukwa chake tinachita zimenezi.+ 25 Tsopano tili mʼmanja mwanu. Tichiteni chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino ndi choyenera.” 26 Yoswa anavomereza zimenezo. Anawalanditsa kwa Aisiraeli ndipo sanawaphe. 27 Koma pa tsikuli, Yoswa anawalamula kuti azitunga madzi ndi kutola nkhuni za Aisiraeli onse+ ndiponso zapaguwa lansembe la Yehova, pamalo alionse amene Mulungu wasankha.+ Iwo akhala akuchita zimenezi mpaka lero.+

10 Adoni-zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva zoti Yoswa walanda mzinda wa Ai nʼkuuwononga. Anamva kuti wawononga mzindawo ndi kupha mfumu yake+ ngati mmene anachitira ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake.+ Anamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni agwirizana za mtendere ndi Aisiraeli+ ndipo akukhala pakati pawo. Atangomva zimenezi, 2 anachita mantha kwambiri+ chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu ngati mzinda wolamulidwa ndi mfumu. Komanso mzindawo unali waukulu kuposa mzinda wa Ai,+ ndipo amuna onse akumeneko anali asilikali. 3 Choncho Adoni-zedeki mfumu ya ku Yerusalemu anatumiza uthenga kwa Hohamu mfumu ya ku Heburoni,+ Piramu mfumu ya ku Yarimuti, Yafiya mfumu ya ku Lakisi ndi Debiri mfumu ya ku Egiloni.+ Uthengawo unali wakuti: 4 “Bwerani mudzandithandize. Tiyeni tikamenyane ndi Agibiyoni, chifukwa agwirizana ndi Yoswa ndi Aisiraeli.”+ 5 Choncho mafumu 5 a Aamoriwo,+ limodzi ndi magulu awo ankhondo, anasonkhana pamodzi ndipo anakamanga msasa pafupi ndi anthu a ku Gibiyoni nʼcholinga choti amenyane nawo. Mafumuwo anali mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.

6 Zitatero, amuna a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa kumsasa ku Giligala,+ kuti: “Bwerani msanga mudzatithandize ndi kutipulumutsa. Mafumu onse a Aamori okhala kudera lamapiri asonkhana kuti amenyane nafe. Musatisiye tokha ife akapolo anu.”+ 7 Choncho Yoswa ananyamuka ku Giligala limodzi ndi amuna onse ankhondo ndiponso asilikali amphamvu.+

8 Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa ndawapereka mʼmanja mwako.+ Ndipo palibe aliyense amene adzatha kulimbana nawe.”+ 9 Yoswa anayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, ndipo anafika kwa adaniwo modzidzimutsa. 10 Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndipo Aisiraeli anapha adani ambirimbiri ku Gibiyoni. Anawathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka ndi ku Makeda. 11 Atafika pamalo otsetsereka otchedwa Beti-horoni pothawa Aisiraeli, Yehova anayamba kuwagwetsera matalala akuluakulu mpaka kukafika ku Azeka ndipo adaniwo ankafa. Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene Aisiraeli anawapha ndi lupanga.

12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori kwa Aisiraeli, mʼpamene Yoswa analankhula ndi Yehova pamaso pa Aisiraeli kuti:

“Dzuwa, ima+ pamwamba pa Gibiyoni,+

Ndipo mwezi, uime pamwamba pa chigwa cha Aijaloni.”

13 Choncho dzuwa linaimadi, ndiponso mwezi sunayende mpaka mtunduwo utalanga adani ake. Kodi sizinalembedwe mʼbuku la Yasari?+ Dzuwa linaima kumwamba pakatikati, ndipo linaimabe choncho pafupifupi maola 24.* 14 Palibe tsiku ngati limeneli, kaya pambuyo pake kapena patsogolo pake, limene Yehova anamvera mawu a munthu mʼnjira imeneyi,+ popeza Yehova anamenyera nkhondo Isiraeli.+

15 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse anabwerera kumsasa ku Giligala.+

16 Koma mafumu 5 aja anathawa nʼkukabisala kuphanga la ku Makeda.+ 17 Ndiyeno Yoswa analandira uthenga wakuti: “Mafumu 5 aja apezeka atabisala kuphanga la ku Makeda.”+ 18 Choncho Yoswa anati: “Gubuduzirani miyala ikuluikulu pakhomo pa phangalo ndipo musankhe amuna oti azilonderapo. 19 Koma enanu musangoima. Thamangitsani adani anu ndipo mukapeza aliyense muzimupha.+ Musawalole kuti akalowe mʼmizinda yawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.”

20 Yoswa ndi Aisiraeli atamaliza kupha adani awo onse, kupatulapo amene anathawa nʼkukalowa mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, 21 Aisiraeli onse anabwerera bwinobwino kwa Yoswa kumsasa, ku Makeda. Ndipo palibe munthu amene ananena zamtopola kwa Aisiraeliwo. 22 Ndiyeno Yoswa anati: “Tsegulani phangali munditulutsire mafumu 5 amene ali mmenemowo.” 23 Iwo anatseguladi phangalo nʼkutulutsa mafumu 5 aja: Mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.+ 24 Atapita nawo kwa Yoswa, iye anaitana amuna onse a Isiraeli amene anapita naye kunkhondoko nʼkuuza atsogoleri awo kuti: “Bwerani apa muponde kumbuyo kwa makosi a mafumuwa.” Iwo anapita nʼkupondadi kumbuyo kwa makosi a mafumuwo.+ 25 Ndiyeno Yoswa anawauza kuti: “Musaope kapena kuchita mantha.+ Khalani olimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu, chifukwa zimenezi ndi zimene Yehova azichitira adani anu onse amene muzimenyana nawo.”+

26 Kenako Yoswa anawapha nʼkuwapachika pamitengo 5, ndipo anakhala pamenepo mpaka madzulo. 27 Dzuwa likulowa, Yoswa analamula kuti awatsitse pamitengoyo+ nʼkuwaponyera mʼphanga limene anabisalamo lija. Kenako anaika miyala ikuluikulu pakhomo la phangalo, ndipo ilipobe mpaka lero.

28 Tsiku limenelo, Yoswa analanda mzinda wa Makeda+ ndipo anapha anthu amumzindawo ndi lupanga. Anapha mfumu ya mzindawo ndi anthu ake onse, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Mfumu ya ku Makeda+ anaichita zofanana ndi zomwe anaichita mfumu ya ku Yeriko.

29 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Makeda nʼkupita kukamenyana ndi anthu a ku Libina.+ 30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Isiraeli.+ Choncho Aisiraeli anapha anthu onse amumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anaichita mfumu ya ku Yeriko.+

31 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Libina nʼkupita ku Lakisi.+ Atafika anamanga msasa nʼkuyamba kumenyana ndi anthu akumeneko. 32 Yehova anapereka Lakisi mʼmanja mwa Isiraeli, moti analanda mzindawo pa tsiku lachiwiri. Anapha ndi lupanga anthu onse amumzindawo,+ ngati mmene anachitira ku Libina.

33 Zitatero Horamu mfumu ya ku Gezeri+ anapita kukathandiza anthu a ku Lakisi. Koma Yoswa anapha Horamu ndi anthu ake onse, moti sipanatsale wopulumuka.

34 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Lakisi nʼkupita ku Egiloni.+ Kumeneko anamanga msasa nʼkuyamba kumenyana ndi anthu amumzindawo. 35 Analanda mzindawo tsiku lomwelo nʼkupha ndi lupanga anthu onse mumzindawo ngati mmene anachitira ku Lakisi.+

36 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Egiloni nʼkupita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Heburoni.+ 37 Analanda mzindawo ndipo anapha ndi lupanga mfumu yake, anthu ake onse komanso anthu amʼmidzi yake yonse. Anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Choncho anawononga mzindawo ndi aliyense amene anali mmenemo ngati mmene anachitira ku Egiloni.

38 Pomaliza, Yoswa ndi Aisiraeli onse anapita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Debiri.+ 39 Analanda mzindawo ndi midzi yake yonse nʼkugwiranso mfumu yake. Ndiyeno anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mmenemo+ ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Anachitira mzinda wa Debiri ndi mfumu yake zimene anachitira mzinda wa Heburoni komanso mzinda wa Libina ndi mfumu yake.

40 Choncho Yoswa anagonjetsa anthu amʼdera lonse lamapiri, anthu a ku Negebu, a ku Sefela,+ ndi amʼmadera otsetsereka pamodzi ndi mafumu awo onse. Anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka ndipo anapha chamoyo chilichonse*+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamula.+ 41 Yoswa anagonjetsa anthuwa kuchokera ku Kadesi-barinea+ mpaka ku Gaza+ ndi dera lonse la Goseni+ mpaka ku Gibiyoni.+ 42 Yoswa anagonjetsa mafumu onsewa nʼkulanda malo awo pa nthawi imodzi, chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi amene ankawamenyera nkhondo.+ 43 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anabwerera kumsasa ku Giligala.+

11 Yabini mfumu ya ku Hazori atangomva zimenezi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni,+ mfumu ya ku Simironi ndi mfumu ya ku Akasafu.+ 2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amʼdera lamapiri kumpoto, mafumu amʼchigwa* chakumʼmwera kwa Kinereti, mafumu a ku Sefela ndiponso mafumu okhala mʼmapiri a Dori+ kumadzulo. 3 Anaitanitsanso Akanani+ omwe ankakhala kumʼmawa ndi kumadzulo, ndiponso Aamori,+ Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi akudera lamapiri. Komanso anaitanitsa Ahivi+ omwe ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni+ ku Mizipa. 4 Choncho mafumuwo pamodzi ndi magulu awo onse ankhondo anabwera. Anali ambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ndipo anali ndi mahatchi* komanso magaleta* ankhondo ambirimbiri. 5 Mafumu onsewa anagwirizana kuti akumane pamodzi, ndipo anakamanga msasa pafupi ndi madzi a ku Meromu kuti amenyane ndi Aisiraeli.

6 Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino, ndidzawapereka onsewo kuti aphedwe ndi Aisiraeli. Mahatchi awo udzawapundule*+ ndipo magaleta awo udzawatenthe.” 7 Ndiyeno Yoswa ndi asilikali ake onse anafika modzidzimutsa pafupi ndi madzi a Meromu nʼkuyamba kupha adaniwo. 8 Yehova anapereka adaniwo mʼmanja mwa Aisiraeli.+ Choncho anayamba kuwagonjetsa ndipo anawathamangitsa mpaka kukafika kumzinda waukulu wa Sidoni,+ ku Misirepotu-maimu+ ndi kuchigwa cha Mizipe kumʼmawa. Anapitiriza kuwapha moti panalibe amene anapulumuka.+ 9 Kenako Yoswa anachita zimene Yehova anamuuza. Mahatchi awo anawapundula ndipo magaleta awo anawatentha.+

10 Komanso Yoswa anabwerera nʼkukalanda mzinda wa Hazori ndipo anapha mfumu yake ndi lupanga,+ chifukwa poyamba mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa. 11 Aisiraeliwo anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mumzindawo. Panalibe chamoyo chilichonse chimene chinatsala,+ ndipo Yoswa anatentha mzinda wa Hazori. 12 Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumuwa, nʼkupha mafumu ake onse ndi lupanga+ mogwirizana ndi zimene Mose, mtumiki wa Yehova, analamula. 13 Komabe mizinda yonse imene inamangidwa pamalo okwera, Aisiraeli sanaitenthe. Mzinda wa Hazori wokha ndi umene Yoswa anautentha. 14 Aisiraeli anatenga katundu yense wa mʼmizindayi ndi ziweto zomwe.+ Koma anthu onse anawapha ndi lupanga.+ Sanasiye munthu aliyense wamoyo.+ 15 Zimene Yehova analamula mtumiki wake Mose, Mose analamula Yoswa+ ndipo Yoswayo anachitadi zonse. Palibe chilichonse chimene Yoswa sanachite pa zonse zimene Yehova analamula Mose.+

16 Yoswa analanda dziko lonselo, dera lamapiri, dera lonse la Negebu,+ dziko lonse la Goseni, ku Sefela,+ ku Araba+ ndiponso dera lamapiri la Isiraeli ndi zigwa zake. 17 Analandanso dera lochokera kuphiri la Halaki lomwe lili moyangʼanizana ndi Seiri mpaka kukafika ku Baala-gadi,+ kuchigwa cha Lebanoni mʼmunsi mwa phiri la Herimoni.+ Yoswa anagonjetsa mafumu awo onse nʼkuwapha. 18 Iye anamenyana ndi mafumu onsewa kwa nthawi ndithu. 19 Panalibe mzinda winanso umene unagwirizana za mtendere ndi Aisiraeli, kupatulapo Ahivi a ku Gibiyoni.+ Aisiraeli anamenyana ndi mizinda ina yonse nʼkuigonjetsa.+ 20 Yehova ndi amene analola kuti anthuwa aumitse mitima yawo+ kuti amenyane ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndipo asawamvere chisoni,+ koma awatheretu mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.+

21 Pa nthawiyo Yoswa anapita nʼkukapha Aanaki+ onse kudera lamapiri, ku Heburoni, ku Debiri, ku Anabi, kudera lonse lamapiri la Yuda ndiponso kudera lonse lamapiri la Isiraeli. Yoswa anapha Aanaki onsewo nʼkuwononga mizinda yawo.+ 22 Palibe Aanaki amene anatsala mʼdziko la Aisiraeli, kupatulapo+ amene ankakhala ku Gaza,+ ku Gati+ ndi ku Asidodi.+ 23 Choncho Yoswa analanda dziko lonse mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Mose.+ Kenako Yoswa anagawa dzikolo kwa Aisiraeli kuti likhale cholowa chawo, mogwirizana ndi mafuko awo.+ Ndipo mʼdziko lonselo munalibenso nkhondo.+

12 Awa ndi mafumu amene Aisiraeli anagonjetsa nʼkulanda madera awo kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera kuchigwa cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba konse, chakumʼmawa:+ 2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni. 3 Ankalamuliranso ku Araba mpaka kunyanja ya Kinereti*+ chakumʼmawa kwa nyanjayi, mpaka kukafika kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.* Komanso ankalamulira kumʼmawa, cha ku Beti-yesimoti ndiponso chakumʼmwera, kumunsi kwa Pisiga.+

4 Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi wa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti ndi ku Edirei. 5 Ankalamulira kuphiri la Herimoni, ku Saleka ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri ndi Amaakati.+ Ankalamuliranso hafu ya Giliyadi mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni, mfumu ya Hesiboni, ankalamulira.+

6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumuwa.+ Kenako Mose mtumiki wa Yehova anapereka maderawa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti akhale awo.+

7 Yoswa ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumu akudera lakumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera ku Baala-gadi+ kuchigwa cha Lebanoni+ mpaka kuphiri la Halaki,+ limene lili moyangʼanizana ndi Seiri.+ Atawagonjetsa, Yoswa anapereka dzikolo kwa mafuko a Isiraeli poligawa mʼmagawomagawo.+ 8 Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa:

 9 Mfumu ya Yeriko,+ imodzi. Mfumu ya Ai+ pafupi ndi Beteli, imodzi.

10 Mfumu ya Yerusalemu, imodzi. Mfumu ya Heburoni,+ imodzi.

11 Mfumu ya Yarimuti, imodzi. Mfumu ya Lakisi, imodzi.

12 Mfumu ya Egiloni, imodzi. Mfumu ya Gezeri,+ imodzi.

13 Mfumu ya Debiri,+ imodzi. Mfumu ya Gederi, imodzi.

14 Mfumu ya Horima, imodzi. Mfumu ya Aradi, imodzi.

15 Mfumu ya Libina,+ imodzi. Mfumu ya Adulamu, imodzi.

16 Mfumu ya Makeda,+ imodzi. Mfumu ya Beteli,+ imodzi.

17 Mfumu ya Tapuwa, imodzi. Mfumu ya Heferi, imodzi.

18 Mfumu ya Afeki, imodzi. Mfumu ya Lasaroni, imodzi.

19 Mfumu ya Madoni, imodzi. Mfumu ya Hazori,+ imodzi.

20 Mfumu ya Simironi-meroni, imodzi. Mfumu ya Akasafu, imodzi.

21 Mfumu ya Taanaki, imodzi. Mfumu ya Megido, imodzi.

22 Mfumu ya Kadesi, imodzi. Mfumu ya Yokineamu+ ku Karimeli, imodzi.

23 Mfumu ya Dori kumapiri a Dori,+ imodzi. Mfumu ya Goimu ku Giligala, imodzi.

24 Mfumu ya Tiriza, imodzi. Mafumu onse analipo 31.

13 Tsopano Yoswa anali atakalamba, ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Choncho Yehova anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba ndipo uli ndi zaka zambiri, koma madera oti alandidwe adakali ambiri. 2 Madera amene atsala ndi awa:+ Madera onse a Afilisiti ndi madera onse a Agesuri.+ 3 (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo* kumʼmawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi, lomwe linkaonedwa kuti ndi la Akanani.)+ Komanso madera a olamulira 5 a Afilisiti+ omwe ndi Gaza, Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ ndiponso dera la Aavimu.+ 4 Kumʼmwera kwatsala dera lonse la Akanani. Patsalanso mzinda wa Asidoni+ wotchedwa Meara, mpaka kukafika ku Afeki kumalire a Aamori, 5 dera la Agebala+ ndiponso dera lonse la Lebanoni chakumʼmawa, kuyambira ku Baala-gadi mʼmunsi mwa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo-hamati.*+ 6 Ine ndidzathamangitsa pamaso pa Aisiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu+ komanso Asidoni+ onse. Iweyo ungopereka maderawa kwa Aisiraeli+ kuti akhale cholowa chawo mogwirizana ndi zimene ndinakulamula.+ 7 Maderawa uwagawe kwa mafuko 9 ndiponso kwa hafu ya fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”+

8 Mose mtumiki wa Yehova anapereka cholowa kwa hafu ina ya fuko la Manase, kwa fuko la Rubeni ndi kwa fuko la Gadi, kutsidya lakumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano.+ 9 Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwera a Medeba mpaka kukafika ku Diboni. 10 Anawapatsanso mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori imene inkalamulira ku Hesiboni, mpaka kumalire ndi Aamoni.+ 11 Anapatsidwanso Giliyadi, dera la Agesuri, la Amaakati,+ phiri lonse la Herimoni ndi dera lonse la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12 Mafukowa anapatsidwanso dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi mfumu ya Basana, imene inali kulamulira ku Asitaroti ndi ku Edirei. (Mfumu Ogi inali mmodzi mwa Arefai otsala.)+ Mose anagonjetsa anthu onsewa nʼkuwathamangitsa.+ 13 Koma Aisiraeli sanathamangitse+ Agesuri ndi Amaakati, ndipo iwo akukhalabe pakati pawo mpaka lero.

14 Fuko la Levi lokha ndi limene sanalipatse malo monga cholowa chawo.+ Cholowa chawo ndi nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+

15 Kenako Mose anagawira cholowa fuko la Rubeni motsatira mabanja awo. 16 Dera lawo linayambira ku Aroweli, mzinda umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho komanso malo onse okwera a Medeba. 17 Linafikanso ku Hesiboni ndi midzi yake yonse+ imene inali mʼmalo okwera, ku Diboni, ku Bamoti-baala komanso ku Beti-baala-meoni.+ 18 Linaphatikizaponso Yahazi,+ Kademoti,+ Mefaata,+ 19 Kiriyataimu, Sibima,+ Zereti-sahara, malo amene anali mʼphiri la kuchigwa, 20 Beti-peori, dera lotsetsereka la ku Pisiga,+ Beti-yesimoti,+ 21 mizinda yonse ya mʼmalo okwera ndiponso dziko lonse la Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ili ku Hesiboni.+ Mfumu imeneyi Mose anaigonjetsa+ limodzi ndi atsogoleri a ku Midiyani, Evi, Rekemu, Zuri, Hura, ndi Reba.+ Amenewa anali mafumu omwe anali pansi pa ulamuliro wa Sihoni ndipo ankakhala mʼdzikolo. 22 Balamu+ mwana wa Beori, wolosera zamʼtsogolo uja,+ anali mmodzi mwa anthu amene Aisiraeli anawapha ndi lupanga. 23 Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodano. Dera limeneli linali cholowa cha anthu a fuko la Rubeni chimene anapatsidwa motsatira mabanja awo. Iwo anapatsidwa derali limodzi ndi mizinda komanso midzi ya kumeneko.

24 Komanso Mose anagawira cholowa fuko la Gadi motsatira mabanja awo. 25 Dera lawo linali mzinda wa Yazeri,+ mizinda yonse ya ku Giliyadi komanso hafu ya dziko la Aamoni,+ mpaka kukafika ku Aroweli kufupi ndi Raba.+ 26 Kuchokera ku Hesiboni+ linakafika ku Ramati-mizipe ndi ku Betonimu, ndiponso kuchokera ku Mahanaimu+ mpaka kumalire ndi Debiri. 27 Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya mʼchigwa ya Beti-harana, Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni ndi dera lotsala la dziko la Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndi umene unali malire awo kuchokera kumunsi kwa nyanja ya Kinereti,*+ kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano. 28 Dera limeneli linali cholowa cha anthu a fuko la Gadi chimene anapatsidwa motsatira mabanja awo. Iwo anapatsidwa derali limodzi ndi mizinda komanso midzi ya kumeneko.

29 Komanso Mose anapereka cholowa kwa hafu ya fuko la Manase motsatira mabanja awo.+ 30 Dera lawo linayambira ku Mahanaimu,+ dera lonse la Basana, dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Mfumu Ogi ya Basana ndiponso midzi yonse yaingʼono ya Yairi+ ku Basana. Dera lawoli linali ndi matauni 60. 31 Mose anapereka hafu ya dera la Giliyadi, Asitaroti, Edirei+ ndi mizinda ya ufumu wa Ogi mʼdziko la Basana kwa ana a Makiri,+ mwana wa Manase. Anapereka dzikoli kwa hafu ya ana a Makiri motsatira mabanja awo.

32 Chimenechi ndi cholowa chimene Mose anawapatsa kuti chikhale chawo, pamene anali mʼchipululu cha Mowabu, kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano, chakumʼmawa kwa Yeriko.+

33 Koma fuko la Alevi, Mose sanalipatse cholowa.+ Chifukwa cholowa chawo ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli, mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+

14 Aisiraeli anatenga cholowa chawo mʼdziko la Kanani. Wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri a mafuko a makolo a Aisiraeli ndi amene anawagawira cholowachi.+ 2 Pogawa cholowacho kwa mafuko 9 ndi hafu,+ anachita maere+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose. 3 Mose anali atagawira kale cholowa mafuko awiri ndi hafu kutsidya lina la Yorodano.*+ Koma Alevi sanawagawire cholowacho.+ 4 Ana a Yosefe anali mafuko awiri,+ la Manase ndi la Efuraimu.+ Alevi sanapatsidwe cholowa cha malo koma anangowapatsa mizinda+ yoti azikhalamo komanso malo odyetserako ziweto ndi osungirako katundu wawo.+ 5 Choncho Aisiraeli anagawana dzikolo mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

6 Tsopano amuna a ku Yuda anapita kwa Yoswa ku Giligala.+ Ndipo Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, anauza Yoswa kuti: “Inu mukudziwa bwino zimene Yehova anauza+ Mose, munthu wa Mulungu woona,+ ku Kadesi-barinea zokhudza ine ndi inu.+ 7 Ndinali ndi zaka 40 pamene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kudzafufuza zokhudza dzikoli,+ kuchokera ku Kadesi-barinea. Nditabwerako ndinamuuza moona mtima zonse zimene ndinaona.+ 8 Ngakhale kuti abale anga amene ndinali nawo, anapangitsa anthu kuchita mantha kwambiri,* ine ndinatsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.+ 9 Mose anandilumbirira tsiku limenelo kuti: ‘Dziko limene wakaliponda ndi mapazi ako lidzakhala cholowa chako ndi cha ana ako mpaka kalekale, chifukwa watsatira Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’+ 10 Yehova wandisunga ndi moyo+ mogwirizana ndi zimene analonjeza.+ Tsopano padutsa zaka 45 kuchokera pamene Yehova analonjeza Mose pa nthawi imene Aisiraeli anali mʼchipululu.+ Lero ndili ndi zaka 85. 11 Ndipo ndine wamphamvu ngati mmene ndinalili tsiku limene Mose anandituma. Mphamvu zanga zidakali mmene zinalili pa nthawiyo, moti ndikhoza kupita kunkhondo komanso kuchita zinthu zina. 12 Choncho ndipatseni dera lamapiri ili limene Yehova anandilonjeza tsiku limene lija. Ngakhale kuti pa tsikulo, munamva kuti kumeneko kuli Aanaki+ komanso mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ sindikukayikira kuti Yehova adzakhala nane,+ ndipo ndikawathamangitsa ndithu ngati mmene Yehova analonjezera.”+

13 Choncho Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune ndipo anamʼpatsa mzinda wa Heburoni kuti ukhale cholowa chake.+ 14 Nʼchifukwa chake mzinda wa Heburoni unakhala cholowa cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi, mpaka lero, chifukwa iye anatsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.+ 15 Poyamba mzinda wa Heburoni unkatchedwa Kiriyati-ariba.+ (Ariba anali munthu wamphamvu pakati pa Aanaki.) Kenako mʼdzikolo munakhala mopanda nkhondo.+

15 Gawo limene linaperekedwa+ ku fuko la Yuda kuti ligawidwe kwa mabanja awo linkafika kumalire a Edomu+ ndi kuchipululu cha Zini, mpaka kumapeto kwa Negebu, kumʼmwera. 2 Malire awo akumʼmwera ankayambira kumapeto kwa Nyanja Yamchere,*+ kugombe lake lakumʼmwera. 3 Malirewo analowera kumʼmwera kuchitunda cha Akirabimu+ nʼkukafika ku Zini. Kenako anakwera kuchokera kumʼmwera kupita ku Kadesi-barinea,+ nʼkukafika ku Hezironi mpaka ku Adara, nʼkuzungulira kukafika cha ku Karika. 4 Ndiyeno anapitirira kukafika ku Azimoni+ mpaka kuchigwa cha Iguputo+ nʼkukathera ku Nyanja.* Amenewa anali malire awo akumʼmwera.

5 Malire akumʼmawa anali Nyanja Yamchere* mpaka pamene mtsinje wa Yorodano umathira mʼnyanjayi. Malire akumpoto anakhota pagombe pamene mtsinje wa Yorodano umathirira mʼnyanjayi.+ 6 Malirewo anapitirira mpaka ku Beti-hogila+ nʼkukadutsa kumpoto kwa Beti-araba,+ kukafika kumwala wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 7 Anakafika ku Debiri kuchigwa cha Akori+ nʼkukhotera kumpoto cha ku Giligala,+ patsogolo pa chitunda cha Adumi, kumʼmwera kwa chigwa cha mtsinje. Malirewo anapitirira nʼkukafika kumadzi a Eni-semesi,+ nʼkukathera ku Eni-rogeli.+ 8 Kuchokera pamenepo, anapitirira mpaka kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ kumalo otsetsereka otchedwa Yebusi+ kumʼmwera, kutanthauza Yerusalemu.+ Anapitirirabe mpaka pamwamba pa phiri loyangʼanizana ndi chigwa cha Hinomu, limene lili kumadzulo kwa chigwacho. Phirilo lili kumpoto kwa chigwa cha Arefai, kumapeto kwa chigwacho. 9 Kuchokera pamwamba pa phirilo, malirewo anakafika kukasupe wa madzi a Nafitoa,+ nʼkupitirira mpaka kumizinda ya mʼmbali mwa phiri la Efuroni. Anapitirirabe mpaka ku Baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu.+ 10 Kuchokera ku Baala, malirewo anazungulira chakumadzulo kulowera kuphiri la Seiri, nʼkukadutsa pamalo otsetsereka a phiri la Yearimu kumpoto, kutanthauza Kesaloni. Ndiyeno anatsetserekera ku Beti-semesi,+ nʼkukafika ku Timuna.+ 11 Malirewo anakafika kumalo otsetsereka otchedwa Ekironi+ kumpoto, nʼkukadutsa ku Sikeroni. Anapitirira mpaka kuphiri la Baala kukafika ku Yabineeli, nʼkukathera kunyanja.

12 Malire akumadzulo anali Nyanja Yaikulu*+ ndi gombe lake. Amenewa anali malire a ana a Yuda a mbali zonse motsatira mabanja awo.

13 Kalebe+ mwana wa Yefune anamʼpatsa gawo lake pakati pa ana a Yuda pomvera lamulo la Yehova kwa Yoswa. Anamʼpatsa Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni. (Ariba anali bambo wa Anaki.)+ 14 Choncho Kalebe anathamangitsa mbadwa za ana atatu a Anaki+ kuderalo. Anawo anali Sesai, Ahimani ndi Talimai.+ 15 Kenako anapita kukamenyana ndi anthu a mumzinda wa Debiri.+ (Poyamba dzina la mzinda wa Debiri linali Kiriyati-seferi.) 16 Kenako Kalebe anati: “Aliyense amene agonjetse mzinda wa Kiriyati-seferi nʼkuulanda, ndidzamʼpatsa mwana wanga Akisa, kuti akhale mkazi wake.” 17 Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ mʼbale wake wa Kalebe, analanda mzindawo. Choncho Kalebe anamʼpatsa Akisa,+ mwana wake, kuti akhale mkazi wake. 18 Pamene Akisa ankapita kunyumba, anauza Otiniyeli kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo ake. Kenako Akisa anatsika pabulu.* Atatero Kalebe anamʼfunsa kuti: “Ukufuna chiyani?”+ 19 Iye anapempha kuti: “Ndidalitseni, poti mwandipatsa malo akumʼmwera* mundipatsenso Guloti-maimu.”* Atatero, Kalebe anamʼpatsa Guloti Wakumtunda ndi Guloti Wakumunsi.

20 Ichi chinali cholowa cha fuko la Yuda, motsatira mabanja awo.

21 Mizinda ya kumapeto kwa gawo la fuko la Yuda, chakumalire ndi Edomu+ kumʼmwera, inali Kabizeeli, Ederi, Yaguri, 22 Kina, Dimona, Adada, 23 Kedesi, Hazori, Itinani, 24 Zifi, Telemu, Bealoti, 25 Hazori-hadata, Kerioti-hezironi, kutanthauza Hazori, 26 Amamu, Sema, Molada,+ 27 Hazara-gada, Hesimoni, Beti-peleti,+ 28 Hazara-suali, Beere-seba,+ Bizioti, 29 Baala, Iimu, Ezemu, 30 Elitoladi, Kesili, Horima,+ 31 Zikilaga,+ Madimana, Sanasana, 32 Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni.+ Mizinda 29 pamodzi ndi midzi yake.

33 Ku Sefela+ kunali Esitaoli, Zora,+ Asina, 34 Zanowa, Eni-ganimu, Tapuwa, Enamu, 35 Yarimuti, Adulamu,+ Soko, Azeka,+ 36 Saaraimu,+ Aditaimu, Gedera ndi Gederotaimu.* Mizinda 14 ndi midzi yake.

37 Zenani, Hadasha, Migidala-gadi, 38 Dilani, Mizipe, Yokiteeli, 39 Lakisi,+ Bozikati, Egiloni, 40 Kaboni, Lamamu, Kitilisi, 41 Gederoti, Beti-dagoni, Naama ndi Makeda.+ Mizinda 16 ndi midzi yake.

42 Libina,+ Eteri, Asani,+ 43 Ifita, Asina, Nezibi, 44 Keila, Akizibu ndi Maresha. Mizinda 9 ndi midzi yake.

45 Ekironi pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ingʼonoingʼono yomwe. 46 Kuchokera ku Ekironi kulowera chakumadzulo, malo onse amene ali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake.

47 Asidodi+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ingʼonoingʼono yomwe, Gaza+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ingʼonoingʼono yomwe, mpaka kukafika kuchigwa cha Iguputo ndi ku Nyanja Yaikulu* pamodzi ndi dera la mʼmbali mwa nyanjayi.+

48 Kudera lamapiri kunali Samiri, Yatiri,+ Soko, 49 Dana, Kiriyati-sana, kutanthauza Debiri, 50 Anabi, Esitemo,+ Animu, 51 Goseni,+ Holoni ndi Gilo.+ Mizinda 11 ndi midzi yake.

52 Arabu, Duma, Esana, 53 Yanimu, Beti-tapuwa, Apeka, 54 Humita, Kiriyati-ariba kutanthauza Heburoni,+ ndi Ziori. Mizinda 9 ndi midzi yake.

55 Maoni,+ Karimeli, Zifi,+ Yuta, 56 Yezereeli, Yokideamu, Zanowa, 57 Kayini, Gibea ndi Timuna.+ Mizinda 10 ndi midzi yake.

58 Haluli, Beti-zuri, Gedori, 59 Maaratu, Beti-anotu ndi Elitekoni. Mizinda 6 ndi midzi yake.

60 Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu+ ndi Raba. Mizinda iwiri ndi midzi yake.

61 Kuchipululu kunali Beti-araba,+ Midini, Sekaka, 62 Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni-gedi.+ Mizinda 6 ndi midzi yake.

63 Amuna a fuko la Yuda analephera kuthamangitsa Ayebusi+ a ku Yerusalemu,+ moti Ayebusi+ akukhalabe limodzi ndi Ayuda ku Yerusalemu mpaka lero.

16 Gawo limene ana a Yosefe+ anapatsidwa+ linayambira kumtsinje wa Yorodano kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi akumʼmawa kwa Yeriko, kudutsa kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+ 2 Kuchokera ku Beteli wa ku Luzi, malire ake anakadutsa kumalire a Aareki ku Ataroti. 3 Kenako anatsetserekera kumadzulo kumalire a Ayafeleti, mpaka kukafika kumalire a Beti-horoni Wakumunsi+ kupita ku Gezeri,+ nʼkukathera kunyanja.

4 Choncho mbadwa za Yosefe,+ omwe ndi Manase ndi Efuraimu, analandira gawo lawo.+ 5 Malire akumʼmawa a gawo la ana a Efuraimu motsatira mabanja awo anali awa: Kuchokera ku Ataroti-adara+ mpaka kukafika ku Beti-horoni Wakumtunda+ 6 nʼkukathera kunyanja. Kumpoto kwake kunali Mikametatu,+ ndipo malirewo anazungulira chakumʼmawa kukafika ku Taanatu-silo, nʼkupitirirabe chakumʼmawa mpaka ku Yanoa. 7 Ndiyeno anatsetsereka kuchokera ku Yanoa kukafika ku Ataroti ndi ku Naara mpaka ku Yeriko,+ nʼkupitirirabe mpaka ku Yorodano. 8 Kuchokera ku Tapuwa,+ malirewo analowera chakumadzulo kuchigwa cha Kana nʼkukathera kunyanja.+ Chimenechi ndi cholowa cha fuko la Efuraimu motsatira mabanja awo. 9 Cholowa cha ana a Efuraimu chinaphatikizapo mizinda imene inali mkati mwa cholowa cha Manase,+ mizinda yonse ndi midzi yake.

10 Koma Aefuraimu sanathamangitse Akanani amene ankakhala ku Gezeri.+ Choncho Akananiwo akukhalabe pakati pa Aefuraimu mpaka lero,+ ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo.+

17 Kenako fuko la Manase,+ mwana woyamba wa Yosefe,+ linapatsidwa gawo lake.+ Makiri+ mwana woyamba wa Manase, bambo wake wa Giliyadi, anali msilikali wamphamvu, choncho anapatsidwa dera la Giliyadi ndi Basana.+ 2 Ana a Manase otsalawo anapatsidwa gawo lawo motsatira mabanja awo. Gawolo linaperekedwa kwa ana a Abi-ezeri,+ ana a Heleki, ana a Asiriyeli, ana a Sekemu, ana a Heferi ndi ana a Semida. Amenewa anali ana aamuna a Manase mwana wa Yosefe, motsatira mabanja awo.+ 3 Tselofekadi+ mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana aamuna, koma aakazi okhaokha. Mayina a anawo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 4 Iwo anapita kwa wansembe Eliezara,+ Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri, nʼkuwauza kuti: “Yehova ndi amene analamula Mose kuti atipatse cholowa pakati pa abale athu.”+ Choncho anawapatsa cholowa pakati pa azichimwene a bambo awo, pomvera lamulo la Yehova.+

5 Fuko la Manase linapatsidwa magawo 10, kuwonjezera pa dera la Giliyadi ndi Basana lomwe linali kutsidya lina* la Yorodano.+ 6 Ana aakazi a fuko la Manase anapatsidwa cholowa pakati pa ana aamuna a fukolo, ndipo dera la Giliyadi linakhala cholowa cha ana otsala a fukolo.

7 Malire a gawo la fuko la Manase anayambira ku Aseri kukafika ku Mikametatu,+ patsogolo pa Sekemu.+ Malirewo analowera kumʼmwera* kukafika kwa anthu okhala ku Eni-Tapuwa. 8 Dera la Tapuwa+ linakhala la Manase, koma mzinda wa Tapuwa umene unali mʼmalire a Manase, unali wa ana a Efuraimu. 9 Malire a gawolo anatsetserekera kuchigwa cha Kana kenako analowera kumʼmwera kwa chigwachi. Pakati pa mizinda ya Manase panali mizinda ya Efuraimu+ ndipo malire a fuko la Manasewo anali kumpoto kwa chigwachi, ndipo anakathera kunyanja.+ 10 Kumʼmwera kwa malirewo linali gawo la Efuraimu, ndipo kumpoto linali gawo la Manase lomwe linakathera kunyanja.+ Kumpoto, gawo la Manase linakakumana ndi la Aseri, ndipo kumʼmawa linakakumana ndi la Isakara.

11 Mizinda yotsatirayi ya mʼgawo la Isakara ndi Aseri, pamodzi ndi anthu ake ndi midzi yake yozungulira, inali ya Manase: Beti-seani, Ibuleamu,+ Dori,+ Eni-dori,+ Taanaki,+ Megido komanso madera atatu amapiri.

12 Koma ana a Manase analephera kulanda mizindayi, moti Akanani anakakamira kukhalabe mʼderali.+ 13 Aisiraeli atakula mphamvu, anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ koma sanathe kuwathamangitsiratu.+

14 Ana a Yosefe anafunsa Yoswa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwatipatsa gawo limodzi lokha+ kuti likhale cholowa chathu, pomwe tilipo anthu ambiri popeza Yehova akutidalitsabe mpaka pano?”+ 15 Yoswa anawayankha kuti: “Ngati mulipo ambiri pitani kumtunda kunkhalango ya Aperezi+ ndi ya Arefai,+ mukagwetse mitengo nʼkutenga deralo, poti dera lamapiri la Efuraimu+ lakucheperani.” 16 Kenako ana a Yosefe anati: “Dera lamapiri silitikwanira, ndiponso Akanani akuchigwa, a ku Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira ndiponso akuchigwa cha Yezereeli+ ali ndi magaleta ankhondo+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa.” 17 Poyankha, Yoswa anauza anthu a fuko la Yosefe, omwe ndi ana a Efuraimu ndi Manase, kuti: “Ndinu ambiri ndipo ndinu amphamvu kwambiri. Simuyenera kukhala ndi gawo limodzi lokha,+ 18 koma mutengenso dera lamapiri.+ Ngakhale kuti ndi lankhalango, mudzagwetsamo mitengo ndipo gawo lanu likathera kumeneko. Mudzathamangitsa Akanani ngakhale kuti ndi amphamvu ndipo ali ndi magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa.”+

18 Kenako gulu lonse la Aisiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamanga chihema chokumanako,+ popeza pa nthawiyo nʼkuti atagonjetsa dzikolo.+ 2 Koma panali mafuko 7 a Aisiraeli amene anali asanagawiridwebe cholowa. 3 Choncho Yoswa anafunsa Aisiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+ 4 Sankhani amuna atatu pa fuko lililonse oti ndiwatume. Akayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili kuti lidzagawidwe mogwirizana ndi cholowa cha mafuko awo. Akatero adzabwerere kwa ine. 5 Ndiyeno adzagawe dzikolo mʼzigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kumʼmwera,+ ndipo a mʼbanja la Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+ 6 Koma inuyo mukagawe dzikolo mʼzigawo 7 ndipo mukazilembe. Kenako mukabwere nazo kuno kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu. 7 Koma Alevi sadzapatsidwa gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya lakumʼmawa la Yorodano.”

8 Choncho amuna aja anakonzeka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula kuti: “Pitani mukayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili. Mukatero mukabwere kuno, ndipo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova ku Silo kuno.”+ 9 Amunawo anapitadi kukayendera dzikolo ndipo analigawa mʼzigawo 7 potsatira mizinda yake nʼkulemba mʼbuku. Atamaliza anabwerera kwa Yoswa kumsasa ku Silo. 10 Kenako Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova ku Silo+ ndipo anagawira Aisiraeli dzikolo moti fuko lililonse analipatsa gawo limodzi.+

11 Maere oyamba anagwera fuko la Benjamini motsatira mabanja awo, ndipo anapatsidwa dera limene linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+ 12 Kumpoto, malire a gawo lawo anayambira ku Yorodano nʼkupitirira kukafika kumalo otsetsereka akumpoto kwa Yeriko,+ nʼkukwera phiri chakumadzulo, nʼkukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+ 13 Malirewo anapitirira kukafika kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, kutanthauza Beteli.+ Kuchokera ku Luzi anatsetserekera ku Ataroti-adara,+ nʼkukadutsa paphiri lakumʼmwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+ 14 Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kumʼmwera, paphiri loyangʼanizana ndi kumʼmwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa Yuda. Amenewa ndi malire akumadzulo a gawo la Benjamini.

15 Malire akumʼmwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, nʼkulowera chakumadzulo, nʼkupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+ 16 Malirewo anakafika kumapeto kwa phiri loyangʼanizana ndi chigwa cha Mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi+ mpaka kukafika ku Eni-rogeli.+ 17 Analowera chakumpoto nʼkukafika ku Eni-semesi mpaka kumzinda wa Gelilotu, womwe uli kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 18 Anapitirira nʼkukafika kumalo otsetsereka akumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, nʼkutsetsereka kukafika ku Araba. 19 Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka akumpoto kwa Beti-hogila,+ nʼkukathera kugombe lakumpoto kwa Nyanja Yamchere,*+ kumapeto kwa mtsinje wa Yorodano mbali yakumʼmwera. Awa anali malire akumʼmwera a gawo la Benjamini. 20 Kumʼmawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse.

21 Mizinda ya fuko la Benjamini motsatira mabanja awo inali Yeriko, Beti-hogila, Emeki-kezizi, 22 Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+ 23 Aavi, Para, Ofira, 24 Kefara-amoni, Ofini ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake.

25 Kunalinso Gibiyoni,+ Rama, Beeroti, 26 Mizipe, Kefira, Moza, 27 Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28 Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake.

Chimenechi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo.

19 Maere achiwiri+ anagwera Simiyoni, kutanthauza fuko la Simiyoni,+ motsatira mabanja awo. Cholowa chawo chinali pakati pa cholowa cha Yuda.+ 2 Cholowa chawocho chinali Beere-seba+ kuphatikizapo Sheba, Molada,+ 3 Hazara-suali,+ Bala, Ezemu,+ 4 Elitoladi,+ Betuli, Horima, 5 Zikilaga,+ Beti-marikaboti, Hazara-susa, 6 Beti-lebaoti+ ndi Saruheni. Mizinda 13 ndi midzi yake. 7 Chinalinso Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani.+ Mizinda 4 ndi midzi yake 8 ndiponso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka kukafika ku Baalati-beere, komwe ndi ku Rama wakumʼmwera. Ichi chinali cholowa cha fuko la Simiyoni motsatira mabanja awo. 9 Cholowa cha ana a Simiyoni chinatengedwa mʼgawo la Yuda chifukwa ana a Yuda gawo lawo linkawakulira. Choncho ana a Simiyoni anapatsidwa malo pakati pa cholowa chawo.+

10 Maere achitatu+ anagwera ana a Zebuloni+ motsatira mabanja awo. Malire a cholowa chawo anakafika ku Saridi. 11 Malirewa analowera chakumadzulo, kukafika ku Marala ndipo anapitirira mpaka ku Dabeseti komanso kuchigwa chimene chili kutsogolo kwa Yokineamu. 12 Kuchokera ku Saridi analowera kumʼmawa mpaka kumalire a Kisilotu-tabori. Ndiyeno anapitirira kukafika ku Daberati+ mpaka ku Yafiya. 13 Kuchokera kumeneko, malirewo analowera chakumʼmawa nʼkukafika ku Gati-heferi,+ ku Eti-kazini ndi ku Rimoni mpaka ku Nea. 14 Malirewo anazungulira kumpoto kwa Nea kukafika ku Hanatoni, nʼkukathera kuchigwa cha Ifita-eli 15 komanso ku Katati, Nahalala, Simironi,+ Idala ndi ku Betelehemu.+ Mizinda 12 ndi midzi yake. 16 Chimenechi chinali cholowa cha ana a Zebuloni motsatira mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.

17 Maere a 4+ anagwera Isakara,+ kapena kuti ana a Isakara motsatira mabanja awo. 18 Malire a gawo lawo anakafika ku Yezereeli,+ Kesulotu, Sunemu,+ 19 Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20 Rabiti, Kisioni, Ebezi, 21 Remeti, Eni-ganimu,+ Eni-hada ndi Beti-pazezi. 22 Malirewo anakafikanso ku Tabori,+ ku Sahazuma ndi ku Beti-semesi nʼkukathera ku Yorodano. Mizinda 16 ndi midzi yake. 23 Ichi chinali cholowa cha fuko la Isakara motsatira mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.

24 Maere a 5+ anagwera fuko la Aseri+ motsatira mabanja awo. 25 Malire a gawo lawo anadutsa ku Helikati,+ Hali, Beteni, Akasafu, 26 Alameleki, Amadi ndi Misali. Analowera kumadzulo nʼkukafika ku Karimeli+ ndi ku Sihori-libanati. 27 Kenako anabwerera kulowera kumʼmawa ku Beti-dagoni, nʼkukafika ku Zebuloni ndi kumpoto kwa chigwa cha Ifita-eli. Anakafikanso ku Beti-emeki ndi ku Nehieli nʼkupitirira mpaka ku Kabulu chakumanzere. 28 Anapitirira mpaka ku Eburoni, Rehobu, Hamoni ndi Kana mpaka kumzinda waukulu wa Sidoni.+ 29 Malirewo anabwerera ku Rama, mpaka kukafika kumzinda wa Turo+ wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako anabwereranso ku Hosa nʼkukathera kunyanja mʼchigawo cha Akizibu. 30 Anakafikanso ku Uma, Afeki+ ndi Rehobu.+ Mizinda 22 ndi midzi yake. 31 Ichi chinali cholowa cha fuko la Aseri motsatira mabanja awo+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.

32 Maere a 6+ anagwera ana a Nafitali motsatira mabanja awo. 33 Malire a gawo lawo anayambira ku Helefi, kumtengo waukulu wa ku Zaananimu,+ ku Adami-nekebi ndi ku Yabineeli mpaka kukafika ku Lakumu nʼkukathera ku Yorodano. 34 Malirewo anabwerera kumadzulo ku Azinotu-tabori, nʼkupitirira mpaka ku Hukoku nʼkukafika ku Zebuloni kumʼmwera. Anakafikanso ku Aseri kumadzulo ndi ku Yuda chakumʼmawa, kumtsinje wa Yorodano. 35 Mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri inali Zidimu, Zere, Hamati,+ Rakati, Kinereti, 36 Adama, Rama, Hazori,+ 37 Kedesi,+ Edirei, Eni-hazori, 38 Yironi, Migidala-eli, Horemu, Beti-anati ndi Beti-semesi.+ Mizinda 19 ndi midzi yake. 39 Chimenechi chinali cholowa cha fuko la Nafitali motsatira mabanja awo,+ ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.

40 Maere a 7+ anagwera fuko la Dani+ motsatira mabanja awo. 41 Malire a gawo la cholowa chawo anadutsa ku Zora,+ Esitaoli, Iri-semesi, 42 Saalabini,+ Aijaloni,+ Itila, 43 Eloni, Timuna,+ Ekironi,+ 44 Eliteke, Gebetoni,+ Baalati, 45 Yehuda, Bene-beraki, Gati-rimoni,+ 46 Me-jarikoni ndi Rakoni, nʼkukafika kumalire amene ali kutsogolo kwa Yopa.+ 47 Koma fuko la Dani gawo lawo linkawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo nʼkupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga nʼkuyamba kukhalamo ndipo anausintha dzina loti Lesemu nʼkuupatsa dzina loti Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+ 48 Ichi chinali cholowa cha fuko la Dani motsatira mabanja awo, ndipo imeneyi inali mizinda yawo ndi midzi yake.

49 Choncho anamaliza kugawa dzikolo ndipo fuko lililonse linali ndi cholowa chake. Kenako Aisiraeli anamʼpatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa chake pakati pawo. 50 Molamulidwa ndi Yehova, anamʼpatsa mzinda umene anapempha wa Timinati-sera,+ mʼdera lamapiri la Efuraimu ndipo iye anamanga mzindawo nʼkumakhalamo.

51 Zimenezi zinali zigawo za cholowa chimene wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri a mafuko a Isiraeli anagawira anthu.+ Anagawa dzikolo pochita maere ku Silo+ pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ Choncho anamaliza kugawa dzikolo.

20 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako+ imene ndinakuuzani kudzera mwa Mose, 3 kuti wopha munthu mwangozi* azithawirako pothawa wobwezera magazi.+ 4 Azithawira kumzinda umodzi mwa mizindayi.+ Akatero azikaima pageti+ nʼkufotokoza nkhani yake kwa akulu a mzindawo. Akuluwo azimulandira nʼkumupatsa malo mumzindamo ndipo azikhala nawo limodzi. 5 Ngati wobwezera magazi amene akumuthamangitsa wafika, akuluwo asamapereke wopha munthuyo kwa wobwezera magaziyo, chifukwa iye sanaphe munthuyo mwadala ndipo sankadana naye.+ 6 Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,*+ ndipo azikhalabe komweko mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Zikatero, wopha munthuyo akhoza kubwerera nʼkukalowa mumzinda wa kwawo komwe anathawa kuja, nʼkumakhala mʼnyumba mwake.’”+

7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya mʼdera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ mʼdera lamapiri la Efuraimu komanso Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, mʼdera lamapiri la Yuda. 8 Kuchigawo cha Yorodano, kumʼmawa kwa Yeriko, anasankha Bezeri,+ mʼchipululu cha mʼdera lokwererapo la fuko la Rubeni. Anasankhanso Ramoti+ ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi komanso Golani+ ku Basana mʼdera la fuko la Manase.+

9 Imeneyi inali mizinda imene inasankhidwa kuti Aisiraeli onse ndi alendo okhala pakati pawo, azithawirako akapha munthu mwangozi,+ kuti asaphedwe ndi wobwezera magazi asanakaonekere pamaso pa oweruza.*+

21 Tsopano atsogoleri a mabanja a Alevi, anapita kwa wansembe Eliezara,+ Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri a mafuko a Isiraeli. 2 Analankhula nawo ku Silo+ mʼdziko la Kanani, kuti: “Kudzera mwa Mose, Yehova analamula kuti tipatsidwe mizinda yoti tizikhalamo komanso malo oti tizidyetserako ziweto zathu.”+ 3 Choncho Aisiraeli anamvera lamulo la Yehova nʼkupatsa Alevi mizindayo+ ndi malo ake odyetserako ziweto, kuchokera pa cholowa chawo.+

4 Atachita maere, maerewo anagwera mabanja a Akohati.+ Ndipo Alevi, omwe anali ana a wansembe Aroni, anapatsidwa mizinda 13 kuchokera mʼmafuko a Yuda,+ Simiyoni+ ndi Benjamini.+

5 Anachita maere ena, ndipo Akohati amene anatsala anawapatsa mizinda 10 yochokera mʼmabanja a fuko la Efuraimu,+ la Dani ndi hafu ya fuko la Manase.+

6 Anachitanso maere, ndipo ana a Gerisoni+ anapatsidwa mizinda 13 yochokera mʼmabanja a fuko la Isakara, la Aseri, la Nafitali ndi hafu ya fuko la Manase ku Basana.+

7 Anthu a mʼbanja la Merari+ anapatsidwa mizinda 12 yochokera mʼfuko la Rubeni, la Gadi ndi la Zebuloni,+ motsatira mabanja awo.

8 Choncho Aisiraeli anachita maere nʼkupatsa Alevi mizinda imeneyi ndi malo ake odyetserako ziweto, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.+

9 Aisiraeli anapereka mizinda yotsatirayi kuchokera ku fuko la Yuda ndi la Simiyoni+ 10 kuti ikhale ya ana a Aroni ochokera mʼmabanja a Akohati, omwe anali Alevi, chifukwa maere oyamba anagwera iwowa. 11 Anawapatsa Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali bambo wa Anaki.) Mzindawu pamodzi ndi malo ouzungulira odyetserako ziweto unali mʼdera lamapiri la Yuda. 12 Koma malo ena onse amumzindawo komanso midzi yake, anawapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune kuti akhale ake.+

13 Ana a wansembe Aroni anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Heburoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 14 Yatiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 15 Holoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 16 Aini+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yuta+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beti-semesi ndi malo ake odyetserako ziweto. Panali mizinda 9 kuchokera mʼmafuko awiri amenewa.

17 Kuchokera mʼfuko la Benjamini, anawapatsa Gibiyoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Geba ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 18 Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Alimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

19 Mizinda yonse imene anapereka kwa ansembe, ana a Aroni, inalipo 13 ndi malo ake odyetserako ziweto.+

20 Mabanja a ana a Kohati, kapena kuti Alevi otsala, anapatsidwa mizinda yochokera mʼfuko la Efuraimu pambuyo pochita maere. 21 Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto mʼdera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 22 Kibizaimu ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

23 Kuchokera mʼfuko la Dani, anawapatsa Eliteke ndi malo ake odyetserako ziweto, Gibitoni ndi malo ake odyetserako ziweto, 24 Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Gati-rimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

25 Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anawapatsa Taanaki+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Gati-rimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri.

26 Mizinda yonse ndi malo ake odyetserako ziweto, imene mabanja a ana otsala a Kohati anapatsidwa, inalipo 10.

27 Ana a Gerisoni+ a mʼmabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda kuchokera ku hafu ya fuko la Manase. Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Golani+ ku Basana ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beesitera ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri.

28 Kuchokera mʼfuko la Isakara,+ anawapatsa Kisioni ndi malo ake odyetserako ziweto, Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 29 Yarimuti ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Eni-ganimu ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4

30 Kuchokera mʼfuko la Aseri,+ anawapatsa Misali ndi malo ake odyetserako ziweto, Abidoni ndi malo ake odyetserako ziweto, 31 Helikati+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

32 Kuchokera mʼfuko la Nafitali, anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake, wa Kedesi+ ku Galileya ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Hamoti-dori ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Karitani ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda itatu.

33 Mizinda yonse ya Agerisoni motsatira mabanja awo inalipo 13 ndi malo ake odyetserako ziweto.

34 Kuchokera mʼfuko la Zebuloni,+ mabanja a Amerari,+ amene ndi Alevi otsala, anapatsidwa Yokineamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Karita ndi malo ake odyetserako ziweto, 35 Dimena ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Nahalala+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

36 Kuchokera mʼfuko la Rubeni, anawapatsa Bezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yahazi ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 37 Kademoti ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Mefaata ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

38 Kuchokera mʼfuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 39 Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda 4.

40 Amerari omwe anatsala pa mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda yokwana 12 motsatira mabanja awo, pochita maere.

41 Mizinda yonse ya Alevi mʼdziko limene Aisiraeli anapatsidwa inalipo 48, pamodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 42 Mzinda uliwonse unali ndi malo odyetserako ziweto. Ndi mmene mizinda yonseyi inalili.

43 Choncho Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbira kuti adzapatsa makolo awo,+ ndipo iwo analanda dzikolo nʼkumakhalamo.+ 44 Yehova anachititsa kuti azikhala mwamtendere mʼdzikolo, mogwirizana ndi zonse zimene analumbirira makolo awo.+ Panalibe mdani aliyense amene anatha kulimbana nawo.+ Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo.+ 45 Palibe lonjezo* limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.+

22 Kenako Yoswa anaitana anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, 2 nʼkuwauza kuti: “Mwachita zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani,+ ndiponso mwamvera zonse zimene ine ndinakulamulani.+ 3 Simunawasiye abale anu nthawi yonseyi mpaka lero+ ndipo mwasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu.+ 4 Panopa Yehova Mulungu wanu wapatsa abale anu mpumulo mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+ Choncho bwererani, mupite kumatenti anu kudera limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, kutsidya lina* la Yorodano.+ 5 Koma mukaonetsetse kuti mukutsatira Chilamulo ndiponso malamulo amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani.+ Muzikakonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake zonse,+ kumvera malamulo ake,+ kumʼmamatira+ ndiponso kumʼtumikira+ ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.”+

6 Kenako Yoswa anawadalitsa nʼkuwauza kuti azipita ndipo anapita kumatenti awo. 7 Mose anali atapatsa hafu ya fuko la Manase cholowa chawo ku Basana.+ Hafu ina ya fukolo, Yoswa anaipatsa cholowa pamodzi ndi abale awo kutsidya lina la Yorodano kumadzulo.+ Komanso pamene Yoswa ankawauza kuti azipita kumatenti awo, anawadalitsa. 8 Anawauza kuti: “Bwererani kumatenti anu ndi chuma chambiri, ziweto zambiri, siliva, golide, kopa, zitsulo ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munakatenga+ kwa adani anu ndipo mukagawane ndi abale anu.”

9 Zitatero, anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, anachoka ku Silo kumene kunali Aisiraeli mʼdziko la Kanani. Anabwerera ku Giliyadi,+ kudera limene Mose anawapatsa molamulidwa ndi Yehova kuti azikhalako.+ 10 Atafika kuchigawo cha Yorodano chimene chinali mʼdziko la Kanani, anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase anamanga guwa lansembe mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano, ndipo guwalo linali lalikulu komanso logometsa. 11 Kenako Aisiraeli ena anamva+ anthu akunena kuti: “Eti anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a dziko la Kanani, mʼchigawo cha Yorodano kumbali ya Aisiraeli.” 12 Aisiraeli atamva zimenezi, gulu lawo lonse linasonkhana ku Silo+ kuti apite kukamenyana nawo.

13 Kenako Aisiraeli anatumiza Pinihasi+ mwana wa wansembe Eleazara, kwa anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, ku Giliyadi. 14 Anamʼtumiza pamodzi ndi atsogoleri 10. Fuko lililonse la Isiraeli linatumiza mtsogoleri mmodzi woimira nyumba ya makolo ake. Mtsogoleri aliyense anali woimira nyumba ya bambo ake pakati pa Aisiraeli masauzande.+ 15 Atafika kwa anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi, anawauza kuti:

16 “Anthu onse a Yehova anena kuti: ‘Nʼchifukwa chiyani mwachita zosakhulupirika+ kwa Mulungu wa Isiraeli? Lero mwasiya kutsatira Yehova pomanga guwa lanu lansembe kuti mupandukire Yehova.+ 17 Kodi zoipa zimene tinachita ku Peori zatichepera? Sitinadziyeretsebe ku tchimo limene lija mpaka lero, ngakhale kuti mliri unagwera anthu a Yehova.+ 18 Kodi inuyo tsopano mukufuna kusiya kutsatira Yehova? Mukapandukira Yehova lero, ndiye kuti mawa adzakwiyira gulu lonse la Aisiraeli.+ 19 Ngati chili chifukwa choti dziko lanu ndi lodetsedwa, wolokerani kudziko la Yehova+ kumene kuli tenti yopatulika ya Yehova*+ ndipo muzikakhala nafe. Koma musapandukire Yehova, ndipo musachititse ifeyo kupanduka chifukwa cha guwa lansembe limene mwamangali, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu.+ 20 Akani+ mwana wa Zera atachita zosakhulupirika potenga zinthu zoyenera kuwonongedwa, kodi mkwiyo sunagwere gulu lonse la Aisiraeli?+ Ndipo iye sanafe yekha chifukwa cha cholakwa chakecho.’”+

21 Atamva zimenezi, anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase anayankha atsogoleri a masauzande a Aisiraeliwo, kuti:+ 22 “Yehova, Mulungu wa milungu! Yehova, Mulungu wa milungu!+ Iye akudziwa ndipo nawonso Aisiraeli adziwa. Ngati tachita zimenezi chifukwa chopanduka ndiponso chifukwa choti ndife osakhulupirika kwa Yehova, musatisiye amoyo lero. 23 Ngati tadzimangira guwa lansembe kuti tisiye kutsatira Yehova ndiponso ngati timafuna kuti tiziperekerapo nsembe zopsereza ndi nsembe zambewu komanso nsembe zachiyanjano, Yehova apereka yekha chilango.+ 24 Koma ife tinamanga guwa lansembeli chifukwa choda nkhawa kuti, ‘Mʼtsogolo muno ana anu adzauza ana athu kuti: “Mulibe ufulu woti muzilambira Yehova Mulungu wa Isiraeli. 25 Yehova anaika malire pakati pa ife ndi inuyo a fuko la Rubeni ndi la Gadi. Malire ake ndi mtsinje wa Yorodano. Inuyo zolambira Yehova sizikukukhudzani.” Ndipo ana anu adzalepheretsa ana athu kulambira* Yehova.’

26 Nʼchifukwa chake tinati: ‘Tiyeni timange guwa, osati loperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina, 27 koma kuti ukhale umboni pakati pa ife ndi inu+ komanso ana athu,* wakuti tidzatumikira Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, nsembe zachiyanjano ndi nsembe zina,+ kuti mʼtsogolo ana anu asadzauze ana athu kuti: “Inuyo zolambira Yehova sizikukukhudzani.”’ 28 Choncho tinati, ‘Akadzatiuza zimenezi ifeyo kapena ana athu mʼtsogolo, tidzawauza kuti: “Onani guwa lansembe limene makolo athu anamanga lofanana ndi guwa la Yehova, osati kuti aziperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina, koma kuti likhale umboni pakati pa inu ndi ife.”’ 29 Nʼzosatheka kuti ife lero tipandukire Yehova, nʼkusiya kutsatira Yehova+ pomanga guwa lansembe loti tiziperekerapo nsembe zopsereza, zambewu ndi nsembe zina, kusiya guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, limene lili patsogolo pa tenti yake yopatulika!”+

30 Wansembe Pinihasi, atsogoleri a gulu la Aisiraeli ndiponso atsogoleri a masauzande a Aisiraeli amene anali naye, atamva mawu amene ana a Rubeni, a Gadi ndi a Manase ananena, anakhutira.+ 31 Ndiyeno Pinihasi mwana wa wansembe Eliezara, anauza ana a Rubeni, a Gadi ndi a Manase, kuti: “Lero tadziwa kuti Yehova ali pakati pathu chifukwa simunachite zosakhulupirika kwa Yehova. Apatu mwapulumutsa Aisiraeli mʼdzanja la Yehova.”

32 Kenako Pinihasi mwana wa wansembe Eliezara ndi atsogoleri aja, anachoka kwa anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ku Giliyadi, nʼkubwerera kwa Aisiraeli ena ku Kanani. Ndipo anawafotokozera zimene anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ananena. 33 Aisiraeliwo atamva zimenezi anakhutira ndipo anatamanda Mulungu. Sananenenso zopita kukamenyana ndi fuko la Rubeni ndi la Gadi kapena kukawononga dera limene ankakhala.

34 Choncho anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi analitcha dzina guwalo,* chifukwa anati, “Guwali ndi mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu woona.”

23 Tsopano Yoswa anali atakalamba ndiponso anali ndi zaka zambiri.+ Apa nʼkuti patapita masiku ambiri kuchokera pamene Yehova anapatsa Aisiraeli mpumulo+ powapulumutsa kwa adani awo onse owazungulira. 2 Yoswa anaitana Aisiraeli onse,+ akulu awo, atsogoleri, oweruza ndi akapitawo+ nʼkuwauza kuti: “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri. 3 Inuyo mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu anachitira mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Yehova Mulungu wanu ndi amene ankakumenyerani nkhondo.+ 4 Ndinakupatsani malo a mitundu yonse imene yatsalayi pochita maere.+ Ndinakupatsaninso malo a mitundu imene ndinaiwononga+ kuchokera kumtsinje wa Yorodano mpaka ku Nyanja Yaikulu* chakumadzulo,* kuti akhale cholowa cha mafuko anu.+ 5 Yehova Mulungu wanu ndi amene ankawachotsa pamaso panu,+ ndipo anawathamangitsa chifukwa cha inu. Inu munatenga malo awo mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani.+

6 Tsopano limbani mtima kwambiri kuti muzitsatira zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la Chilamulo+ cha Mose, ndipo musapite kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 7 Ndiponso muzipewa kugwirizana* ndi mitundu+ imene yatsala pakati panu. Musamatchule nʼkomwe mayina a milungu yawo+ kapena kulumbira pa milunguyo, ndipo musamaitumikire kapena kuigwadira.+ 8 Koma muyenera kumamatira Yehova Mulungu wanu+ ngati mmene mwakhala mukuchitira mpaka lero. 9 Yehova adzathamangitsa mitundu ikuluikulu ndiponso yamphamvu kuichotsa kwa inu+ chifukwa mpaka pano, palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene wakwanitsa kulimbana nanu.+ 10 Munthu mmodzi yekha wa inu adzathamangitsa anthu 1,000,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukumenyerani nkhondo+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.+ 11 Choncho muzikonda Yehova Mulungu wanu+ ndipo mukamachita zimenezi, mudzateteza miyoyo yanu nthawi zonse.+

12 Koma mukasiya Mulungu nʼkumamatira anthu a mitundu ina, amene atsala pakati panuwa+ nʼkumakwatirana nawo+ komanso kumagwirizana nawo, 13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzasiya kuwathamangitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu. Adzakhalanso ngati zikwapu kumsana kwanu+ komanso ngati zitsotso mʼmaso mwanu, mpaka mutatheratu mʼdziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.

14 Tsopano ine ndatsala pangʼono kufa. Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti palibe mawu ngakhale amodzi pa malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena, omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+ 15 Koma mofanana ndi malonjezo onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena omwe akwaniritsidwa pa inu,+ Yehova adzakwaniritsanso pa inu masoka onse* amene ananena, ndipo adzakufafanizani padziko labwino limene Yehova Mulungu wanu wakupatsanili.+ 16 Mukadzaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, Yehova adzakukwiyirani kwambiri+ ndipo simudzachedwa kutha padziko labwino limene iye anakupatsani.”+

24 Kenako Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Isiraeli ku Sekemu. Iye anaitanitsa akulu a Isiraeli, atsogoleri, oweruza ndi akapitawo+ ndipo onse anaima pamaso pa Mulungu woona. 2 Yoswa anauza anthuwo kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Kale makolo anu,+ kuphatikizapo Tera, bambo ake a Abulahamu ndi Nahori, ankakhala kutsidya lina la Mtsinje,*+ ndipo ankatumikira milungu ina.+

3 Patapita nthawi, ndinatenga kholo lanu Abulahamu+ kuchokera kutsidya lina la Mtsinje.* Ndinamuyendetsa mʼdziko lonse la Kanani ndipo ndinachulukitsa mbadwa zake.*+ Ndinamʼpatsa Isaki+ 4 ndipo Isaki ndinamʼpatsa Yakobo ndi Esau.+ Pambuyo pake Esau ndinamʼpatsa phiri la Seiri kuti likhale lake.+ Kenako Yakobo ndi ana ake anapita ku Iguputo.+ 5 Patapita nthawi ndinatumiza Mose ndi Aroni+ ndipo ndinachititsa kuti ku Iguputo kugwe miliri.+ Kenako ndinakutulutsani ku Iguputoko. 6 Pamene ndinkatulutsa makolo anu ku Iguputo,+ atatsala pangʼono kufika kunyanja, Aiguputo anawathamangira ndi magaleta ankhondo ndiponso amuna okwera pamahatchi, mpaka ku Nyanja Yofiira.+ 7 Iwo anayamba kufuulira Yehova.+ Choncho ndinaika mdima pakati pa iwo ndi Aiguputuwo, ndipo ndinawamiza ndi madzi amʼnyanja.+ Munaona ndi maso anu zimene ndinachita ku Iguputo.+ Kenako inu munakhala mʼchipululu zaka zambiri.*+

8 Ndipo ndinakufikitsani kudziko la Aamori amene ankakhala kutsidya lina* la Yorodano. Iwo anayamba kumenyana nanu+ koma ndinawapereka mʼmanja mwanu kuti mutenge dziko lawo kukhala lanu moti ndinawafafaniza pamaso panu.+ 9 Kenako Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ananyamuka kukamenyana ndi Aisiraeli. Iye anaitanitsa Balamu, mwana wa Beori kuti akutemberereni.+ 10 Koma ine sindinafune kumvera Balamu.+ Choncho iye anakudalitsani mobwerezabwereza+ ndipo ndinakulanditsani mʼmanja mwake.+

11 Kenako munawoloka Yorodano+ nʼkufika ku Yeriko.+ Atsogoleri a* ku Yeriko, omwe ndi Aamori, Aperezi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi, anayamba kumenyana nanu, koma ine ndinawapereka mʼmanja mwanu.+ 12 Ndinawachititsa mantha inu musanafike, choncho anakuthawani+ ngati mmene anachitira mafumu awiri a Aamori. Iwo sanathawe chifukwa cha lupanga lanu kapena chifukwa cha uta wanu.+ 13 Ndinakupatsani dziko limene simunalikhetsere thukuta komanso mizinda imene simunaimange,+ ndipo munayamba kukhalamo. Mukudyanso zipatso za mitengo ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale.’+

14 Choncho muziopa Yehova ndi kumʼtumikira ndi mtima wathunthu* komanso mokhulupirika.*+ Chotsani milungu imene makolo anu ankatumikira kutsidya lina la Mtsinje* ndi ku Iguputo,+ ndipo muzitumikira Yehova. 15 Ngati kutumikira Yehova kukukunyansani, sankhani lero amene mukufuna kumʼtumikira,+ kaya milungu imene makolo anu ankaitumikira kutsidya lina la Mtsinje,*+ kapena milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.+ Koma ine ndi banja langa tizitumikira Yehova.”

16 Anthuwo anayankha kuti: “Sitingayerekeze kusiya Yehova nʼkumatumikira milungu ina. 17 Yehova Mulungu wathu ndi amene anatitulutsa mʼdziko la Iguputo pamodzi ndi makolo athu,+ kutichotsa kudziko lomwe tinali akapolo.+ Iye anachita zizindikiro zazikulu pamaso pathu+ ndi kutiteteza njira yonse. Anatitetezanso kwa anthu onse amene tinadutsa pakati pawo.+ 18 Yehova anathamangitsa mitundu yonse ya anthu pamaso pathu, kuphatikizapo Aamori amene ankakhala mʼdzikoli. Choncho nafenso tipitiriza kutumikira Yehova chifukwa iye ndi Mulungu wathu.”

19 Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Sadzakhululuka zolakwa zanu* ndi machimo anu.+ 20 Mukasiya Yehova nʼkuyamba kutumikira milungu yachilendo, iyenso adzakutembenukirani nʼkukuchitirani zoipa ndi kukufafanizani pambuyo pokuchitirani zabwino.”+

21 Koma anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Ayi! Ife tizitumikira Yehova.”+ 22 Choncho Yoswa anauza anthuwo kuti: “Mukudzichitira umboni wotsimikizira kuti mwasankha nokha kutumikira Yehova.”+ Ndiyeno anthuwo anati: “Inde! Ndife mboni.”

23 “Choncho chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu ndipo perekani mitima yanu kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.” 24 Anthuwo anayankha Yoswa kuti: “Tizitumikira Yehova Mulungu wathu komanso kumumvera.”

25 Ndiyeno Yoswa anachita pangano ndi anthuwo ndipo anapereka lamulo ndi chigamulo ku Sekemu. 26 Kenako Yoswa analemba mawu amenewa mʼbuku la Chilamulo cha Mulungu.+ Atatero anatenga mwala waukulu+ ndi kuuika pansi pa mtengo waukulu kwambiri umene uli pafupi ndi malo opatulika a Yehova.

27 Yoswa anauza anthu onsewo kuti: “Mwauona mwalawu? Mwala umenewu ukhala mboni yathu,+ chifukwa wamva mawu onse amene Yehova watiuza, ndipo ukhala mboni yanu kuti musadzakane Mulungu wanu.” 28 Atatero, Yoswa anauza anthuwo kuti azipita, aliyense kucholowa chake.+

29 Patapita nthawi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110.+ 30 Kenako anamuika mʼmanda mʼgawo la cholowa chake ku Timinati-sera,+ kudera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. 31 Aisiraeli anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse amene Yoswa anali ndi moyo komanso masiku onse a akulu amene anakhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira, omwe ankadziwa zinthu zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli.+

32 Mafupa a Yosefe,+ amene Aisiraeli anabweretsa kuchokera ku Iguputo anawaika mʼmanda ku Sekemu, pamalo amene Yakobo anagula kwa ana a Hamori,+ bambo wa Sekemu. Malowo anawagula ndi ndalama zasiliva zokwana 100,+ ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.+

33 Nayenso Eleazara mwana wa Aroni anamwalira.+ Choncho anamuika mʼmanda mʼphiri la Pinihasi mwana wake,+ limene anapatsidwa mʼdera lamapiri la Efuraimu.

Kapena kuti, “Yehoswa,” kutanthauza kuti “Yehova ndi Chipulumutso.”

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.

Kapena kuti, “Uziliwerenga ndi kusinkhasinkha.”

Fulakesi ndi mbewu imene inkalimidwa ku Iguputo. Ankaigwiritsa ntchito popanga ulusi wopangira nsalu.

Kumeneku ndi kumʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mitima yathu inasungunuka.”

Kapena kuti, “chikondi chokhulupirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira: “ana a Isiraeli.”

Umenewu ndi mtunda wa mamita 890. Onani Zakumapeto B14.

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana anu aamuna.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumuopa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mitima yawo inasungunuka.”

Kutanthauza “Phiri la Makungu Akunsonga.”

Kapena kuti, “onse azaka zoyenera kukhala asilikali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa ife.”

Kapena kuti, “Ndachotsa chitonzo cha Iguputo pa inu.”

Kutanthauza “Kuchotsa.”

Kapena kuti, “ndine mtsogoleri.”

Mabaibulo ena amati, “analumbiritsa anthu.”

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “watibweretsera mavuto; wachititsa kuti tinyanyalidwe.”

Kutanthauza, “Tsoka; Kunyanyalidwa.”

Tikati “nthungo” tikutanthauza mkondo waungʼono, wopepukirako.

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.

Kapena kuti, “Ndife antchito.”

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.

Kapena kuti, “pafupifupi kwa tsiku lonse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chilichonse chopuma.”

Kapena kuti, “mafumu a ku Araba.”

Ena amati “mahosi.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ankawapundula powadula mtsempha wakuseri kwa mwendo wakumbuyo.

Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti yomwe inkadziwikanso kuti nyanja ya Galileya.

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Kapena kuti, “loyambira ku Sihori.”

Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”

Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti yomwe inkadziwikanso kuti nyanja ya Galileya.

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anachititsa mitima ya anthu kusungunuka.”

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.

Mabaibulo ena amati, “anawomba mʼmanja ali pabulu.”

Kapena kuti, “mwandipatsa Negebu.”

Kutanthauza “Mabeseni a Madzi.”

Mabaibulo ena amati, “Gedala komanso makola ake a nkhosa.”

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja.”

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Kapena kuti, “mosadziwa.”

Kapena kuti, “pamaso pa mpingo.”

Kapena kuti, “mpingo.”

Kapena kuti, “liwu.”

Imeneyi ndi mbali yakumʼmawa.

Kapena kuti, “chihema chopatulika cha Yehova.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuopa.”

Kapena kuti, “komanso mibadwo yobwera pambuyo pathu.”

Guwalo ayenera kuti analitcha dzina lakuti, “Mboni.”

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.

Kapena kuti, “kolowera dzuwa.”

Kapena kuti, “muzipewa kusakanikirana.”

Kapena kuti, “mawu oipa onse.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti, “mbewu yake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”

Imeneyi ndi mbali yakumʼmwawa.

Mabaibulo ena amati, “Nzika za.”

Kapena kuti, “mosalakwitsa.”

Kapena kuti, “mʼchoonadi.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti, “Sadzakhululuka kugalukira kwanu.”

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani