MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA
Chigawo Choyamba Ziphunzitso Zoyambirira za M’Baibulo
Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwakuthandizani kudziwa choonadi. Zimene mwaphunzira zakuthandizani kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso zakupatsani chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha m’tsogolo limodzi ndi madalitso a m’dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. Panopo, mumakhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu ndipo mwapeza madalitso ambiri chifukwa chosonkhana ndi abale mumpingo. Ndiponso mukudziwa mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ake masiku ano.—Zek. 8:23.
Pamene mukukonzekera kubatizidwa, mudzapindula kwambiri pokambirana ndi akulu mfundo zokhudza ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. (Aheb. 6:1-3) Yehova apitirize kukudalitsani pamene mukuyesetsa kuphunzira Mawu ake kuti mumudziwe bwino ndiponso kuti mudzalandire mphotho imene akulonjeza.—Yoh. 17:3.
1. Kodi Mulungu Woona ndi Ndani?
“Inu mukudziwa bwino lero, ndipo muzikumbukira m’mitima yanu, kuti Yehova ndiye Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi. Palibenso wina.”—Deut. 4:39.
“Pakuti ngakhale ilipo yotchedwa ‘milungu,’ kaya kumwamba kapena padziko lapansi, ndipo n’zoona ilipodi ‘milungu’ yambiri ndi ‘ambuye’ ambiri, kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi amene ndi Atate. Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake. Ndipo pali Ambuye mmodzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye, ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.”—1 Akor. 8:5, 6.
Malemba owonjezera: Sal. 83:18; Yes. 43:10-12.
2. Kodi ena mwa makhalidwe apadera a Yehova ndi ati?
“Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yoh. 4:8.
“Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, Njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”—Deut. 32:4.
“Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?”—Aroma 11:33.
“Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu yanu ndi dzanja lanu lotambasula. Nkhaniyi si yovuta kwa inu.”—Yer. 32:17.
3. Kodi Baibulo limatchula Yehova ndi mawu ati otithandiza kudziwa ena a maudindo ake?
“Pakuti Yehova ndiye Woweruza wathu. Yehova ndiye Wotipatsa Malamulo. Yehova ndiye Mfumu yathu. Iye adzatipulumutsa.”—Yes. 33:22.
“Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve? Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale. Iye satopa kapena kufooka. Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.”—Yes. 40:28.
4. Kodi kulambira Yehova mosagawanika kumatanthauza chiyani? Ndipo n’chifukwa chiyani kulambira koteroko kuli koyenera Yehova yekha?
“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.”—Maliko 12:30.
“Poyankha Yesu anamuuza [Satana] kuti: ‘Malemba amati, “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”’”—Luka 4:8.
“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”—Chiv. 4:11.
Malemba owonjezera: Eks. 20:4, 5; Mac. 17:28.
5. Kodi tiziliona bwanji dzina lenileni la Mulungu?
“Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga, Ndipo ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya. Ndidzakutamandani tsiku lonse. Ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.”—Sal. 145:1, 2.
“Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’”—Mat. 6:9.
Lemba lowonjezera: Eks. 20:7.
6. N’chifukwa chiyani kutchula dzina lenileni la Mulungu kuli kofunika polambira?
“Sumeoni wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.”—Mac. 15:14.
“Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13.
Malemba owonjezera: Sal. 91:14; Yow. 2:32.
7. Kodi Yehova Mulungu adzayeretsa bwanji dzina lake? Nanga ifeyo tingatani pothandiza kuyeretsa dzinali?
“Ndidzadzilemekeza, kudziyeretsa ndi kuchititsa kuti mitundu yambiri ya anthu indidziwe, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”—Ezek. 38:23.
“Achite manyazi ndi kusokonezeka nthawi zonse. Athedwe nzeru ndi kutheratu, Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”—Sal. 83:17, 18.
“Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy. 27:11.
Malemba owonjezera: Ezek. 36:16-18; 1 Pet. 2:12.
8. N’chifukwa chiyani kungakhale kulakwa kupanga fano la Mulungu kapena kumulambira pogwiritsa ntchito mafano?
“Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cha m’madzi a pansi pa dziko lapansi. Usaziweramire kapena kuzitumikira, chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha, wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za anthu odana ndi ine.”—Deut. 5:8, 9.
“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense kapena kupereka ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.”—Yes. 42:8.
“Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambira ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”—Yoh. 4:24.
“Tikuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.”—2 Akor. 5:7.
9. Kodi kudzipereka kwa Yehova kumatanthauza chiyani? Nanga inuyo munadzipereka kwa Yehova m’pemphero?
“‘Taonani! Ine ndabwera . . . kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’ . . . ‘Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.’”—Aheb. 10:7, 9.
“Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsatire mosalekeza.’”—Mat. 16:24.
10. Kodi Yesu Khristu ndi ndani?
“Poyankha, Simoni Petulo ananena kuti: ‘Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.’”—Mat. 16:16.
“Iye ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse, chifukwa kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yachifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamuliro. Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzera mwa iye, ndiponso chifukwa cha iye.”—Akol. 1:15, 16.
Malemba owonjezera: Yoh. 1:1, 2, 14; Mac. 2:36.
11. Kodi Yesu ndi wosiyana bwanji ndi Yehova Mulungu, nanga ndi udindo wotani umene Yehova anam’patsa?
“Ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yoh. 14:28.
“Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo. Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande. Sanatero ayi, koma anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo, ndi kukhala wofanana ndi anthu. Kuposanso pamenepo, atakhala munthu, anadzichepetsa ndi kukhala womvera mpaka imfa. Anakhala womvera mpaka imfa ya pamtengo wozunzikirapo. Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.”—Afil. 2:5-11.
Malemba owonjezera: Dan. 7:13, 14; Yoh. 14:10, 11; 1 Akor. 11:3.
12. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?
“Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”—Mat. 20:28.
“Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh. 3:16.
“Anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: ‘Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!’”—Yoh. 1:29.
“Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.”—Yoh. 18:37.
13. N’chifukwa chiyani pankafunikira dipo? Ndipo inuyo mumapindula nalo bwanji?
“Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.”—Aef. 1:7.
“Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse, chifukwatu onsewo anali atafa kale. Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.”—2 Akor. 5:14, 15.
Malemba owonjezera: Aroma 3:23; 1 Yoh. 4:11.
14. Kodi mzimu woyera n’chiyani? Ndipo unagwira ntchito zotani m’mbuyomu?
“Mphamvu ya Mulungu inali kuyendayenda pamwamba pa madzi akuyawo.”—Gen. 1:2.
“Ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu. Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”—2 Pet. 1:20, 21.
“Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana, monga mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.”—Mac. 2:4.
15. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji masiku ano?
“Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Mac. 1:8.
“Mukhale tcheru ndi kuyang’anira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.”—Mac. 20:28.
“Pakuti mwa mzimu wake, Mulungu anaululira ifeyo zinthu zimenezi, chifukwa mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”—1 Akor. 2:10.
“Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa. Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.”—Agal. 5:22, 23.
Malemba owonjezera: Mat. 10:19, 20; Yoh. 14:26.
16. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?
“M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Dan. 2:44.
“Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mat. 6:10.
Malemba owonjezera: Yes. 9:7; Yoh. 18:36.
17. Kodi Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso otani pa dziko lapansi ndi kwa anthu?
“Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chiv. 21:4.
“Mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake kudzenje la njoka yapoizoni. Sizidzavulazana kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera, chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”—Yes. 11:8, 9.
Malemba owonjezera: Yes. 26:9; 65:21, 22.
18. Kodi kufuna Ufumu choyamba kumatanthauza chiyani?
“Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi . . . Koma unjikani chuma chanu kumwamba . . . Kapolo sangatumikire ambuye awiri . . . Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi . . . Choncho musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi.”—Mat. 6:19-32.
“Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo. Komanso ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino. Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali, anapita mwamsanga n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo.”—Mat. 13:44-46.
Malemba owonjezera: Mat. 16:24; 19:27-29.
19. Kodi timadziwa bwanji kuti tili m’masiku otsiriza, komanso kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira?
“Atakhala pansi m’phiri la Maolivi, ophunzira anafika kwa iye mwamseri ndi kunena kuti: ‘Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?’”—Mat. 24:3.
“Koma dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe. Anthu amenewa uwapewe.”—2 Tim. 3:1-5.
Malemba owonjezera: Mat. 24:4-14; Chiv. 6:1-8; 12:1-12.
20. Kodi Satana Mdyerekezi ndi ndani? Nanga iyeyo ndi ziwanda zake anachokera kuti?
“Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chiv. 12:9.
“Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yoh. 8:44.
“Ndiponso angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala, Mulungu anawasunga kosatha m’maunyolo, mu mdima wandiweyani kuti adzaweruzidwe pa tsiku lalikulu.”—Yuda 6.
Malemba owonjezera: Yobu 1:6; 2:1.
21. Kodi Satana anatsutsa bwanji Yehova ndi ulamuliro wake m’munda wa Edeni? Kodi ndi bodza lotani limene Satana anam’neneza Yobu?
“Tsopano njoka inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?’ Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: ‘Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, “Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.”’ Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.’”—Gen. 3:1-5.
“Satana anamuyankha Yehova kuti: ‘Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe? Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo? Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. Mwadalitsa ntchito ya manja ake ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri padziko lapansi. Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!’”—Yobu 1:9-11.
“Satana anamuyankha Yehova kuti: ‘Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake. Tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!’”—Yobu 2:4, 5.
22. Kodi aliyense payekha, angasonyeze bwanji kuti ali ku mbali ya Yehova ndi ulamuliro wake? Ndipo tingasonyeze bwanji kuti zimene Satana ananeneza atumiki a Mulungu n’zabodza?
“Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy. 27:11.
“Inetu sindingayerekeze n’komwe kunena kuti amuna inu ndinu olungama. Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.
Malemba owonjezera: Sal. 26:11; Yak. 4:7.
23. Kodi n’chiyani chidzachitikire Satana ndi ziwanda zake, malinga ndi chiweruzo chimene Yehova anawapatsa?
“Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”—Gen. 3:15.
“Mulungu amene amapatsa mtendere aphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwapa. Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu kukhale ndi inu.”—Aroma 16:20.
“Ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Kenako anagwira chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000.”—Chiv. 20:1, 2.
“Mdyerekezi, amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo ndi mneneri wonyenga uja. Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya.”—Chiv. 20:10.
24. Popeza kukhulupirira mizimu n’koipa, kodi Akhristu ayenera kupewa zinthu ziti?
“Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.”—Deut. 18:10, 11.
“Koma amantha, opanda chikhulupiriro, odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu, adama, ochita zamizimu, opembedza mafano, ndi onse abodza, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”—Chiv. 21:8.
25. Kodi mzimu wa munthu n’chiyani? Nanga kodi umafa?
“Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi, ndipo anauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake, munthuyo n’kukhala wamoyo.”—Gen. 2:7.
“Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.”—Ezek. 18:4.
26. Kodi tchimo n’chiyani? Ndipo zinatheka bwanji kuti tonse tikhale ochimwa?
“Aliyense amene amachita tchimo samvera malamulo, choncho tchimo ndilo kusamvera malamulo.”—1 Yoh. 3:4.
“Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.”—Aroma 5:12.
Lemba lowonjezera: Sal. 51:5.
27. Kodi muyenera kutani ngati mwachita tchimo lalikulu?
“Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.’”—Sal. 32:5.
“Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa. Choncho muululirane machimo anu poyera ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe. Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”—Yak. 5:14-16.
“Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.”—Miy. 28:13.
28. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya tchimo?
“Musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo. Uchimo usakhale mbuye kwa inu, chifukwa simuli pansi pa chilamulo koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu.”—Aroma 6:12, 14.
29. Kodi imfa n’chiyani?
“Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”—Gen. 3:19.
“Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse. Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.”—Mlal. 9:5.
Malemba owonjezera: Sal. 146:4; Mlal. 3:19, 20; 9:10; Yoh. 11:11-14.
30. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amafa?
“Ndiye chifukwa chake monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.”—Aroma 5:12.
“Chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa.”—Aroma 6:23.
31. Kodi pali chiyembekezo chotani kwa amene anamwalira?
“Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu, chimenenso anthu awa ali nacho, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Mac. 24:15.
“Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo. Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.”—Yoh. 5:28, 29.
32. Kodi ndi anthu angati amene adzaukitsidwe kukakhala kumwamba?
“Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo. Iwo anali kuimba nyimbo yokhala ngati yatsopano pamaso pa mpando wachifumu, pamaso pa zamoyo zinayi, ndi pamaso pa akulu. Palibe anatha kuiphunzira nyimboyo, koma 144,000 amene anagulidwa padziko lapansi.”—Chiv. 14:1, 3.
33. Kodi anthu amene adzaukitsidwe kukakhala kumwamba akukachitako chiyani?
“Ndipo munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”—Chiv. 5:10.
“Kenako ndinaona mipando yachifumu ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza. . . . Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000. Wodala ndi woyera ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri ilibe ulamuliro. Koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.”—Chiv. 20:4, 6.
Lemba lowonjezera: Chiv. 22:5.
34. Kodi anthu onse ali ndi chiyembekezo chotani?
“Kenako anapitiriza kunena kuti: ‘Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.’ Pamenepo Yesu anamuuza kuti: ‘Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’”—Luka 23:42, 43.
“Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo. Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.”—Chiv. 20:12, 13.
Lemba lowonjezera: Chiv. 21:1-4.
35. N’chifukwa chiyani n’kofunika kukhulupirira kwambiri kuti akufa adzaukitsidwa?
“Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo, m’malomwake, muziopa iye amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.”—Mat. 10:28.