MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA
Chigawo Chachiwiri Malamulo Olungama a Yehova
Kuphunzira Baibulo kwakuthandizani kudziwa zimene Yehova amafuna kuti muzichita ndiponso mmene mungachitire zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. Pogwiritsa ntchito zimene mwaphunzira, muyenera kuti mwasintha khalidwe lanu komanso mmene mumaonera moyo. Popeza mwasankha kutsatira mfundo zolungama za Yehova, tsopano mungathe kumutumikira m’njira yovomerezeka monga mtumiki wake wolalikira uthenga wabwino.
Kukambirana mafunso otsatirawa kudzakuthandizani kumvetsa bwino malamulo olungama a Yehova ndiponso kukukumbutsani zimene muyenera kuchita kuti mukhale mtumiki wake wovomerezeka. Mafunsowa akuthandizaninso kudziwa kufunika kochita zinthu zonse ndi chikumbumtima chabwino zomwe zimalemekezetsa Yehova.—2 Akor. 1:12; 1 Tim. 1:19; 1 Pet. 3:16, 21.
1. Kodi malamulo achikhristu pa nkhani ya ukwati ndi otani?
“Yesu anayankha kuti: ‘Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, “Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?” Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.’”—Mat. 19:4-6.
“Choncho woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi . . . Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi.”—1 Tim. 3:2, 12.
2. Kodi Malemba amafotokoza kuti n’chiyani chimene chingathetse ukwati kuti munthu athe kukwatiranso kapena kukwatiwanso?
“Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”—Mat. 19:9.
3. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kupatukana?
“Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Maliko 10:9.
“Kwa okwatira ndikupereka malangizo awa, kwenikweni osati ineyo koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna wake. . . . Mwamunanso asasiye mkazi wake.”—1 Akor. 7:10, 11.
Lemba lowonjezera: 1 Akor. 7:4, 5, 12-16.
4. N’chifukwa chiyani mwamuna ndi mkazi omwe akukhala limodzi ngati banja ayenera kukwatirana mwalamulo? Ngati ndinu wokwatira, kodi mumaona kuti ukwati wanu ndi wovomerezeka ndi boma?
“Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndi kumvera maboma ndiponso olamulira. Komanso akhale okonzekera ntchito iliyonse yabwino.”—Tito 3:1.
“Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.”—Aheb. 13:4.
“Chifukwa cha Ambuye, gonjerani dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu: kaya mfumu chifukwa ili ndi udindo waukulu, kapena nduna chifukwa n’zotumidwa ndi mfumuyo kuti zizipereka chilango kwa ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.”—1 Pet. 2:13, 14.—1 Pet. 2:13, 14.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza mphatso ya moyo?
“Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo. Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, tikuona kuwala.”—Sal. 36:9.
“Mulungu amene anapanga dzikoli . . . ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. . . . Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—Mac. 17:24, 25, 28.
“Khristu Yesu . . . anadzipereka kuti akhale dipo lokwanira ndendende m’malo mwa onse.”—1 Tim. 2:5, 6.
“Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.”—Deut. 22:8.
6. Kodi Yehova amakuona bwanji (a) kupha munthu? (b) kuchotsa mimba? (c) kudzipha?
“Koma . . . opha anthu . . . , gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”—Chiv. 21:8.
“Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi wapakati moti mkaziyo n’kubereka mwana koma palibe amene wamwalira, wovulaza mkaziyo azimulipiritsa ndithu malinga ndi zimene mwiniwake wa mkaziyo angagamule. . . . Ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.”—Eks. 21:22, 23.
“Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.”—Ezek. 18:4.
7. Kodi munthu azichita chiyani akakhala kuti ali ndi matenda oopsa opatsirana?
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.”—Mat. 7:12.
“Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afil. 2:4.
8. N’chifukwa chiyani munthu amene ali ndi matenda opatsirana sayenera (a) kusonyeza ena chikondi powakumbatira kapena kuwapsompsona? (b) kukhumudwa ngati ena sakumuitana ku nyumba zawo? (c) N’chifukwa chiyani munthu amene akudzikayikira kuti mwina angakhale ali ndi matenda opatsirana, ayenera kukayezetsa kaye magazi asanayambe kuchita chibwenzi? (d) N’chifukwa chiyani munthu amene ali ndi matenda opatsirana ayenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu asanakabatizidwe?
“Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kusiyapo kukondana, popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa chilamulo. Chifukwa malamulo . . . chidule chake chili m’mawu awa akuti, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake, chotero chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.”—Aroma 13:8-10.
“Chikondi . . . sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa.”—1 Akor. 13:4, 5.
9. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusala magazi, ndipo angachite bwanji zimenezi?
“Koma musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.”—Gen. 9:4.
“Muzipha chiweto chanu ndi kudya nyama yake nthawi iliyonse imene mwafuna. Muzidya nyamayo malinga ndi dalitso limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani . . . Koma musadye magazi ake. Muziwathira panthaka ngati madzi.”—Deut. 12:15, 16.
“Kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola, ndi dama.”—Mac. 15:29.
10. N’chifukwa chiyani Akhristu sayenera kutsatira Chilamulo cha Mose ndi mfundo zake zokhudza nsembe ndi Sabata?
“Pakuti Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo, kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.”—Aroma 10:4.
“Choncho munthu asakuweruzeni pa nkhani ya kudya ndi kumwa kapena chikondwerero chinachake, kapenanso kusunga tsiku lokhala mwezi, ngakhalenso kusunga sabata, pakuti zinthu zimenezo ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni zake zili mwa Khristu.”—Akol. 2:16, 17.
Malemba owonjezera: Agal. 3:24, 25; Akol. 2:13, 14.
11. Kodi ndi khalidwe liti limene liyenera kuonekera kwambiri pakati pathu monga abale ndi alongo?
“Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:34, 35.
“Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—Akol. 3:14.
Lemba lowonjezera: 1 Akor. 13:4-7.
12. Kodi Akhristu ayenera kuchita chiyani okhulupirira anzawo akawalakwira?
“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”—Akol. 3:13.
“Koposa zonse, khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”—1 Pet. 4:8.
Malemba owonjezera: Miy. 17:9; 19:11; Mat. 7:1-5.
13. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati m’bale wanu wakulakwirani kwambiri, mwina wakuchitirani zinthu mwachinyengo kapena kukunenerani miseche?
“Komanso, ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Akapanda kuwamvera amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvera mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”—Mat. 18:15-17.
14. Kodi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndi ati, nanga kukhala ndi makhalidwe amenewa kungatithandize bwanji kuti tizikhala pa ubwenzi wabwino ndi ena?
“Koma makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”—Agal. 5:22, 23.
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa bodza?
“Mdyerekezi . . . sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yoh. 8:44.
“Onse abodza, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”—Chiv. 21:8.
Malemba owonjezera: Eks. 20:16; 2 Akor. 6:4, 7.
16. Kodi Akhristu kuba amakuona bwanji?
“Koma pasakhale wina wa inu wovutika chifukwa cha kupha munthu, kuba.”—1 Pet. 4:15.
“Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.”—Aef. 4:28.
17. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kumwa mowa?
“Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, chifukwa Mulungu woona wakondwera kale ndi ntchito zako.”—Mlal. 9:7.
“Usamangomwa madzi okha, koma uzimwanso vinyo pang’ono, chifukwa cha vuto lako la m’mimba ndi kudwaladwala kwako kuja.”—1 Tim. 5:23.
18. Kodi Mkhristu ayenera kuiona bwanji nkhani ya kumwa mowa kwambiri, ngakhale kuti mwina sangaledzere?
“Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri, ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka.”—Miy. 23:20.
“Nawonso atumiki othandiza akhale opanda chibwana, . . . osakonda kumwa vinyo wambiri.”—1 Tim. 3:8.
Lemba lowonjezera: 1 Pet. 4:3.
19. Kodi Mkhristu ayenera kuona bwanji kuledzera?
“Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, . . . aumbombo, zidakwa . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.
“Choncho woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera, . . . Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa.”—1 Tim. 3:2, 3.
Lemba lowonjezera: 1 Akor. 5:11.
20. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kupewa mtundu uliwonse wa mankhwala osokoneza bongo?
“Chotero ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu abale, kuti mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza. Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—Aroma 12:1, 2.
“Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.”—2 Akor. 7:1.
Malemba owonjezera: 1 Pet. 4:7; Chiv. 21:8.
21. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya dama (por·neiʹa), lomwe limaphatikizapo chigololo, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndi kugonana kwa mtundu uliwonse kosemphana ndi mmene Mulungu anakonzera?
“Tsopano, ntchito za thupi zimaonekera. Ntchitozi ndizo dama, zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira, . . . ndi zina zotero. . . . Anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—Agal. 5:19-21.
“Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.
“Ndiye chifukwa chake Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zamanyazi za kugonana, popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo n’kumachita zosemphana ndi chibadwa. Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi n’kumatenthetsana okhaokha mwachiwawa m’chilakolako choipa, amuna ndi amuna anzawo, kuchitirana zonyansa ndi kulandiriratu mphoto yoyenerera kulakwa kwawo.”—Aroma 1:26, 27.
“Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.”—Aheb. 13:4.
Malemba owonjezera: Maliko 7:20-23; Aef. 5:5; 1 Pet. 4:3; Chiv. 21:8.
22. Kodi muyenera kumvera malangizo ati a m’Baibulo omwe angakuthandizeni kuti mupewe kuchita chiwerewere?
“Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu zapadziko. Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.”—Akol. 3:2, 5.
“Chomalizira abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afil. 4:8.
23. N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kupewa mtundu uliwonse wa juga?
“Koma anthu inu mwamusiya Yehova. Mwaiwala phiri langa loyera. Inu mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi. Mumadzaza chikho ndi vinyo wosakaniza n’kupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.”—Yes. 65:11.
“Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe. . . . Akuba, aumbombo . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.
24. Ngati munthu wachita tchimo lalikulu koma akufuna kuti akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kodi ayenera kuchita chiyani mwamsanga?
“Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.’”—Sal. 32:5.
“Kodi pali aliyense mwa inu amene akumva zowawa? Apitirize kupemphera. Kodi pali wina amene akukondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu. Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.”—Yak. 5:13-15.
Malemba owonjezera: Miy. 28:13; 1 Yoh. 2:1, 2.
25. Kuwonjezera pa kuulula machimo ake, kodi munthu aliyense ali ndi udindo wotani ngati akudziwa kuti ena achita machimo aakulu zomwe zingaipitse mbiri ya mpingo komanso zingachititse kuti mpingo usakhale woyera?
“Tsopano munthu akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo kuti akachitire umboni za wochimwayo koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.”—Lev. 5:1.
26. Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani tikadzudzulidwa mwa Malemba?
“Mwana wanga, usakane malangizo a Yehova ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,”—Miy. 3:11.
“Pakuti lamulolo ndilo nyale, ndipo malangizo ndiwo kuwala, komanso kudzudzula kowongola zolakwa ndiko njira yamoyo”—Miy. 6:23.
27. Kodi mpingo umachita chiyani ngati pali munthu wina mumpingomo yemwe akuswa malamulo a Mulungu koma sakulapa?
“M’kalata yanga ndinakulemberani kuti muleke kuyanjana ndi anthu adama. Sindikutanthauza kuti muzipeweratu adama a m’dzikoli, kapena aumbombo ndi olanda, kapena opembedza mafano ayi. Kuti muchite zimenezo, ndiye mungafunikire kutuluka m’dzikomo. Koma tsopano ndikukulemberani kuti muleke kuyanjana ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi. Nanga kuweruza anthu amene ali kunja ndi ntchito yanga ngati? Kodi inu si paja mumaweruza amene ali mkati, ndipo Mulungu amaweruza amene ali kunja? ‘M’chotseni pakati panu munthu woipayo.’”—1 Akor. 5:9-13.
28. Kodi kulambira mafano n’kutani? Ndipo tchulani mitundu ina ya kulambira mafano.
“Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi. Usaziweramire kapena kuzitumikira, chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha, wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.”—Eks. 20:4, 5.
“Inu ana okondedwa, pewani mafano.”—1 Yoh. 5:21.
Malemba owonjezera: Yes. 42:8; Yer. 10:14, 15.
29. Kodi Mkhristu ayenera kuliona bwanji dziko lotalikirana ndi Mulunguli?
“Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.
“Kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu? Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.”—Yak. 4:4.
30. Kodi Yesu ankaiona bwanji nkhani yolowerera m’zochitika za ndale za m’dzikoli?
“Ndiyeno Mdyerekezi anamutenganso ndi kupita naye paphiri lalitali kwambiri, ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo. Kenako anamuuza kuti: ‘Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.’ Koma Yesu anamuyankha kuti: ‘Choka Satana! Pakuti Malemba amati, “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”’”—Mat. 4:8-10.
“Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.”—Yoh. 6:15.
31. Munthu akasiyana ndi dziko n’kukhala Mkhristu, kodi ayenera kuyembekezera chiyani kuchokera kwa anthu a m’dzikoli?
“Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Koma popeza simuli mbali ya dzikoli, koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu. . . . Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.”—Yoh. 15:19, 20.
“Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.”—2 Tim. 3:12.
“Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.”—1 Pet. 4:4.
32. Kodi kukhala wosiyana ndi dziko kumakhudza bwanji mmene Mkhristu angasankhire mtundu wa ntchito imene ayenera kugwira?
“Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.”—Aef. 4:28.
“Mdyerekezi . . . ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yoh. 8:44.
“Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu ndipo adzakonza zinthu zokhudza anthu ochokera m’mitundu yamphamvu yakutali. Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”—Mika 4:3.
“Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: ‘Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.’”—Chiv. 18:4.
33. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingathandize Mkhristu posankha zosangalatsa?
“Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.
“Abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afil. 4:8.
“Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko. Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.”—1 Yoh. 2:15.
“Yehova . . . amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Sal. 11:5.
“Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu chifukwa masikuwa ndi oipa. Pa chifukwa chimenechi, lekani kukhala opanda nzeru, koma pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova. Ndiponso, musamaledzere naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa, koma khalanibe odzaza ndi mzimu. Mukakhala pakati panu muziimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndiponso nyimbo zauzimu. Muziimba nyimbo zotamanda Yehova m’mitima mwanu, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu. Nthawi zonse muziyamika Mulungu, Atate wathu, pa zinthu zonse.”—Aef. 5:15-20.
“Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, monga mmene anthu oyera amayenera kuchitira.”—Aef. 5:3.
34. N’chifukwa chiyani sikoyenera kuti Akhristu oona azikhala nawo pa zochitika za zipembedzo zina?
“Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: ‘Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake. Pakuti machimo ake aunjikana mpaka kumwamba, ndipo Mulungu wakumbukira zochita zake zopanda chilungamo.’”—Chiv. 18:4, 5.
Malemba owonjezera: Mat. 7:13, 14, 21-23; 1 Akor. 10:20; 2 Akor. 6:14-18.
35. Kodi ndi mwambo uti wachipembedzo umene Akhristu analamulidwa kuti azichita?
“Kenako anatenga mkate. Atayamika anaunyemanyema n’kuwapatsa, ndipo anati: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.’”—Luka 22:19.
Lemba lowonjezera: 1 Akor. 11:23-26.
36. Kodi mungadziwe bwanji ngati mungathe kuchita kapena kusachita nawo zikondwerero zina zimene zimachitika m’dera lanu?
“Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.
“Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”—1 Akor. 10:21.
“Iwo anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina, ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo. Anayamba kutumikira mafano awo, ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.”—Sal. 106:35, 36.
“Pakuti nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Pet. 4:3.
“Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.”—Mlal. 9:5.
37. Kodi ndi zikondwerero ziti zokumbukira tsiku lobadwa zimene zimatchulidwa m’Baibulo? Ndipo zimenezi zikutithandiza bwanji pa nkhani ya mmene tiyenera kuonera kukondwerera tsiku lobadwa?
“Koma tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambiri, mwakuti analonjeza molumbira kuti adzapatsa mtsikanayo chilichonse chimene angapemphe. Tsopano mtsikanayu, mayi wake atachita kum’pangira, anapempha kuti: ‘Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.’ Mfumuyo inamva chisoni, koma poganizira lumbiro lake lija ndi anthu amene anali nawo paphwandolo, analamula kuti mutuwo uperekedwe. Choncho anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende. Kenako anabweretsa mutuwo m’mbale ndi kuupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anapita nawo kwa mayi ake.”—Mat. 14:6-11.
Malemba owonjezera: Gen. 40:20-22; Mlal. 7:1, 8.