Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • es25
  • June

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • June
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Lamlungu, June 1
  • Lolemba, June 2
  • Lachiwiri, June 3
  • Lachitatu, June 4
  • Lachinayi, June 5
  • Lachisanu, June 6
  • Loweruka, June 7
  • Lamlungu, June 8
  • Lolemba, June 9
  • Lachiwiri, June 10
  • Lachitatu, June 11
  • Lachinayi, June 12
  • Lachisanu, June 13
  • Loweruka, June 14
  • Lamlungu, June 15
  • Lolemba, June 16
  • Lachiwiri, June 17
  • Lachitatu, June 18
  • Lachinayi, June 19
  • Lachisanu, June 20
  • Loweruka, June 21
  • Lamlungu, June 22
  • Lolemba, June 23
  • Lachiwiri, June 24
  • Lachitatu, June 25
  • Lachinayi, June 26
  • Lachisanu, June 27
  • Loweruka, June 28
  • Lamlungu, June 29
  • Lolemba, June 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25

June

Lamlungu, June 1

Tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.—Mac. 14:22.

Yehova anadalitsa Akhristu a mu nthawi ya atumwi chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi mmene zinasinthira pa moyo wawo. Nthawi zambiri ankazunzidwa mwinanso pa nthawi yomwe samayembekezera. Taganizirani zimene zinachitikira Baranaba ndi mtumwi Paulo pamene ankalalikira ku Lusitala. Poyamba iwo analandiridwa bwino ndi anthu omwe ankawamvetsera. Koma pambuyo pake otsutsa “anakopa anthuwo” ndipo ena mwa iwo anaponya Paulo miyala n’kumusiya atatsala pang’ono kufa. (Mac. 14:19) Koma Baranaba ndi Paulo anapitiriza kulalikira kudera lina. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iwo anathandiza “anthu angapo kuti akhale ophunzira” ndipo zolankhula komanso chitsanzo chawo chinalimbikitsa Akhristu anzawo. (Mac. 14:21, 22) Ambiri anapindula chifukwa chakuti Baranaba ndi Paulo sanabwerere m’mbuyo ngakhale pamene anazunzidwa mosayembekezereka. Ifenso tidzadalitsidwa ngati sitingasiye kugwira ntchito imene Yehova watiuza kuti tichite. w23.04 17:13-14

Lolemba, June 2

Mvetserani pemphero langa inu Yehova. Ndipo mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo. Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndidzaitana inu, chifukwa inu mudzandiyankha.​—Sal. 86:6, 7.

Mfumu Davide anakumana ndi adani ambiri oopsa pa moyo wake, ndipo nthawi zambiri ankapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Davide ankakhulupirira kuti Yehova amva komanso kuyankha mapemphero ake. Inunso mungamakhulupirire zimenezi. Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova angatipatse nzeru komanso mphamvu zimene timafunikira kuti tipirire. Iye angagwiritse ntchito abale ndi alongo kapenanso anthu omwe panopa sakumutumikira kuti atithandize mwanjira inayake. Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene Yehova angayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera, timadziwa kuti adzatiyankha. Iye adzatipatsa zenizeni zimene tikufunikira komanso pa nthawi yomwe zikufunikira. Choncho pitirizani kupemphera muli ndi chikhulupiriro choti Yehova azikusamalirani panopa komanso kuti ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse’ m’dziko latsopano lomwe likubwera.—Sal. 145:16. w23.05 21:4, 17-18

Lachiwiri, June 3

Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira?​—Sal. 116:12.

Ndi bwino kumaganizira madalitso amene mungapeze chifukwa chokwaniritsa cholinga chanu. Kodi ndi madalitso otani omwe mungaganizire? Ngati cholinga chanu n’chokhudza kuwerenga Baibulo kapena kupemphera, muziganizira mmene kukwaniritsa cholingacho kungakuthandizireni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. (Sal. 145:18, 19) Ngati cholinga chanu n’choti mukhale ndi khalidwe linalake, muziganizira mmene khalidwelo lingakuthandizireni kuti muzigwirizana ndi ena. (Akol. 3:14) Bwanji osalemba penapake zifukwa zonse zimene zikukuchititsani kufuna kukwaniritsa cholinga chanu? Mukatero muzibwereramo pafupipafupi kuti muziona zifukwazo.Komanso muzicheza ndi anthu omwe angamakulimbikitseni. (Miy. 13:20) .Kunena zoona, tonsefe masiku ena timaona kuti sitikufuna kuchita zinazake. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingakwaniritse cholinga chathu? Ayi. Tikhoza kukwaniritsabe cholinga chathucho ngakhale kuti zimenezi sizingakhale zophweka koma zotsatirapo zake zimakhala zabwino kwambiri. w23.05 24:5-8

Lachitatu, June 4

Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.​—Agal. 6:7.

Kudziwa kuti timafunika kukumana ndi zotsatira za zimene tasankha, kungatilimbikitse kuti tiulule machimo athu, tikonze zimene talakwitsazo komanso tisadzazibwerezenso. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tipitirize kuthamanga pampikisano wokalandira moyo. Ngati simungathe kusintha zomwe munasankha molakwika, muzivomereza mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa. Musamataye nthawi ndi mphamvu zanu poyesa kudzilungamitsa, kudziimba mlandu kapenanso kumaimba ena mlandu. M’malomwake, muzivomereza zimene munalakwitsa n’kumayesetsa kuchita zimene mungathe kuti zinthu zikhale bwino panopa. Ngati mukudziimba mlandu chifukwa cha zimene munalakwitsa, modzichepetsa muzipemphera kwa Yehova, kuvomereza zimene munalakwitsazo komanso kupempha kuti akukhululukireni. (Sal. 25:11; 51:3, 4) Muzipepesa kwa amene munawalakwira. Muzipemphanso kuti akulu akuthandizeni ngati pakufunika kutero. (Yak. 5:14, 15) Muziphunzira pa zimene munalakwitsa ndipo muziyesetsa kuti musazibwerezenso. Mukamachita zimenezi, mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakuchitirani chifundo komanso adzakuthandizani.—Sal. 103:8-13. w23.08 36:8-9

Lachinayi, June 5

Yehoasi anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova pa nthawi yonse imene wansembe Yehoyada ankamulangiza.—2 Maf. 12:2.

Zochita za Yehoyada zinathandiza Yehoasi kuti akhale mfumu yabwino. Zotsatira zake n’zakuti mfumu yachinyamatayi inkafuna kusangalatsa Yehova. Koma Yehoyada atamwalira, Yehoasi anamvera akalonga ampatuko. (2 Mbiri 24:4, 17, 18) Ngakhale kuti Yehova anakhumudwa ndi zimenezi, “anapitiriza kuwatumizira aneneri kuti awathandize kubwerera kwa iye . . . , koma sanamvere.” Iwo sanamvere ngakhale Zekariya mwana wa Yehoyada, yemwe sikuti anangokhala mneneri ndi wansembe wa Yehova, koma analinso wachibale wa Yehoasi. Ndipotu Mfumu Yehoasi anafika pochititsa kuti Zekariya aphedwe. (2 Mbiri 22:11; 24:19-22) Yehoasi sanapitirize kuopa Yehova. Yehova anali atanena kuti: “Amene akundinyoza, adzanyozedwa.” (1 Sam. 2:30) Pasanapite nthawi, gulu laling’ono lankhondo la ku Siriya linagonjetsa “gulu lalikulu kwambiri la asilikali” la Yehoasi ndipo linamusiya “atavulala kwambiri.” (2 Mbiri 24:23-25) Yehoasi anaphedwa ndi atumiki ake chifukwa chopha Zekariya. w23.06 27:16-17

Lachisanu, June 6

Poyamba munali ngati mdima, koma pano muli ngati kuwala.—Aef. 5:8.

Kwa kanthawi, mtumwi Paulo ankaphunzitsa komanso kulalikira uthenga wabwino ku Efeso. (Mac. 19:1, 8-10; 20:20, 21) Iye ankakonda kwambiri abale akewo ndipo ankafunitsitsa kuwathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova. Akhristu a ku Efeso amene Paulo anawalembera kalata, poyamba ankakhulupirira zinthu zabodza komanso ankachita zamizimu. Anthu ambiri mumzinda wa Efeso anali achiwerewere komanso a khalidwe lopanda manyazi. Nthabwala zotukwana zinkanenedwa m’mabwalo amasewera ngakhalenso pamiyambo yachipembedzo. (Aef. 4:17-19) ‘Sankathanso kuzindikira makhalidwe abwino’ kutanthauza kuti “sankamvanso kupweteka kulikonse.” (Aef. 4:17-19) Asanaphunzire zolondola pa nkhani ya zoyenera ndi zosayenera, chikumbumtima cha Akhristu a ku Efeso sichinkawavutitsa. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti iwo anali “mumdima wa maganizo ndipo anali otalikirana ndi moyo umene umachokera kwa Mulungu.” Koma anthu ena a ku Efeso sanakhalebe mumdima. w24.03 12:2, 4-6

Loweruka, June 7

Anthu amene amayembekezera Yehova adzapezanso mphamvu. Iwo . . . adzayenda koma osatopa.​—Yes. 40:31.

Gidiyoni ankafunika kuchita zinthu mwakhama pa ntchito yake monga woweruza. Amidiyani atathawa usiku pankhondo, iye anawathamangitsa kuchokera kuchigwa cha Yezereeli mpaka kukafika kumtsinje wa Yorodano. (Ower. 7:22) Ndiye kodi Gidiyoni anasiya kuwathamangitsa atafika kumtsinjeko? Ayi. Ngakhale kuti anali atatopa, iye ndi amuna 300 omwe anali nawo anawoloka mtsinjewo n’kupitiriza kuwathamangitsa. Pamapeto pake anawapeza ndipo anawagonjetsa. (Ower. 8:4-12) Gidiyoni ankakhulupirira kuti Yehova amupatsa mphamvu, ndipo sanagwiritsidwe fuwa la moto. (Ower. 6:14, 34) Gidiyoni ndi asilikali ake ankathamangitsa wapansi mafumu awiri a ku Midiyani, omwe mwina anali atakwera ngamila. (Ower. 8:12, 21) Komabe mothandizidwa ndi Mulungu, Aisiraeli akhamawa anapambana pankhondoyo. Mofananamo, akulu angamadalire Yehova yemwe “satopa kapena kufooka.” Iye adzawapatsa mphamvu pamene afooka.—Yes. 40:28, 29. w23.06 25:14, 16

Lamlungu, June 8

[Yehova] sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.​—Deut. 31:6.

Tingathe kukhala ndi mtima wokhazikika ngakhale tikukumana ndi mavuto. Choncho, tizidalira Yehova. Taganizirani mmene kudalira malangizo a Yehova kunathandizira Baraki. Ngakhale kuti m’dziko lawo munalibiretu zishango ndi mikondo, Yehova anamuuza kuti akamenye nkhondo ndi gulu la asilikali a ku Kanani, lotsogoleredwa ndi Sisera, lomwe linali ndi zida zonse zankhondo. (Ower. 5:8) Mneneri wamkazi Debora anauza Baraki kuti atsike m’phiri n’kupita kuchigwa kuti akakumane ndi Sisera, yemwe anali ndi magaleta 900. Baraki anamvera, ngakhale kuti zikanakhala zovuta kumenyana ndi asilikali a Sisera omwe magaleta awo sakanamavutika kuthamanga m’chigwamo. Pamene asilikaliwo ankayamba kutsika m’phiri la Tabori, Yehova anayamba kugwetsa mvula. Zimenezi zinachititsa kuti magaletawa azititimira m’matope, ndipo Yehova anachititsa kuti Baraki apambane pankhondoyi. (Ower. 4:1-7, 10, 13-16) Yehova adzachititsa kuti ifenso zinthu zitiyendere bwino ngati timamudalira komanso kumvera malangizo amene amatipatsa kudzera m’gulu lake. w23.07 31:17-18

Lolemba, June 9

Amene adzapirire mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.​—Mat. 24:13.

Kuleza mtima ndi kofunika kuti tidzapulumuke. Mofanana ndi atumiki okhulupirika akale, timafunika kuyembekezera moleza mtima kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake. (Aheb. 6:11, 12) Baibulo limatiyerekezera ndi mlimi. (Yak. 5:7, 8) Mlimi amachita khama kudzala mbewu komanso kuthirira koma sadziwa kuti zikula liti. Komabe mlimiyo amayembekezera moleza mtima n’kumakhulupirira kuti adzakolola. Mofanana ndi zimenezi, timatanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira, ngakhale kuti ‘sitidziwa tsiku limene Ambuye wathu adzabwere.’ (Mat. 24:42) Timayembekezera moleza mtima n’kumakhulupirira kuti pa nthawi yake Yehova adzakwaniritsa zonse zimene analonjeza. Koma ngati sitingakhale oleza mtima, tikhoza kutopa n’kuyamba kusiya pang’onopang’ono choonadi. Tingayambenso kufunafuna zinthu zimene tikuona kuti zingatibweretsere chimwemwe panopa. Koma tikakhala oleza mtima, tingathe kupirira mpaka pamapeto komanso kudzapulumuka.—Mika 7:7. w23.08 35:7

Lachiwiri, June 10

Zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanikirana ndi dongo.​—Dan. 2:42.

Tikayerekezera ulosi wa pa Danieli 2:41-43 ndi maulosi ena opezeka m’buku la Danieli ndi Chivumbulutso, tinganene kuti mapazi akuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse masiku ano, wa Britain ndi America. Ponena za ulamulirowu, Danieli ananena kuti “ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.” N’chifukwa chiyani pa zinthu zina udzakhale wosalimba? Chifukwa chakuti anthu amene ayerekezeredwa ndi dongo amachititsa kuti ufumuwo uzilephera kuchita zinthu mwamphamvu ngati chitsulo.” Timaphunzira mfundo zofunika zingapo za choonadi pa zimene Danieli anafotokoza zokhudza maloto a chifaniziro. Choyamba, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America wakhala ukusonyeza kuti ndi wamphamvu pa zinthu zina. Mwachitsanzo, mayikowa ndi awiri mwa mayiko amene anapambana pa nkhondo yoyamba komanso yachiwiri yapadziko lonse. Komabe ulamulirowu wakhala uli wofooka pa zinthu zina ndipo ukupitirizabe kukhala wofooka chifukwa choti nzika zake zimakangana zokhazokha komanso ndi boma. Chachiwiri, ulamulirowu udzakhala womaliza, Ufumu wa Mulungu usanathetse maboma onse a anthu. w23.08 34:12-13

Lachitatu, June 11

Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova, ndinapitiriza kufuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake.​—Sal. 18:6.

Nthawi zina Davide ankada nkhawa kwambiri chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. (Sal. 18:4, 5) Koma ankatsitsimulidwa chifukwa Yehova ankamusonyeza chikondi komanso kumusamalira. Pa nthawi imeneyi, Yehova ankatsogolera mnzakeyu kumalo “a msipu wambiri” komanso “kumalo opumira a madzi ambiri.” Zimenezi zinathandiza Davide kupezanso mphamvu ndipo anapitiriza kutumikira Mulungu. (Sal. 18:28-32; 23:2) Masiku anonso Yehova amatisonyeza chikondi chokhulupirika ndipo ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambiri, “sitinatheretu.” (Maliro 3:22; Akol. 1:11) Nthawi zambiri moyo wa Davide unkakhala pangozi ndipo adani ake ankakhala amphamvu. Komabe chikondi cha Yehova chinkamuthandiza kuti azimva kuti ndi wotetezeka. Nthawi zonse Davide ankaona kuti Yehova anali naye ndipo zimenezi zinkamulimbikitsa. Choncho iye anaimba kuti: “[Yehova] anandipulumutsa ku zinthu zonse zomwe zimandichititsa mantha.” (Sal. 34:4) Ngakhale kuti nthawi zina Davide ankachita mantha kwambiri, ankakhalabe wolimba mtima chifukwa chodziwa kuti Yehova amamukonda. w24.01 4:15-17

Lachinayi, June 12

Anthu ochimwa akayesa kukunyengerera, usavomere.—Miy. 1:10.

Muziphunzirapo kanthu pa zimene Yehoasi analakwitsa. Mkulu wa Ansembe Yehoyada atamwalira, Yehoasi ankagwirizana ndi anthu olakwika. (2 Mbiri 24:17, 18) Iye anayamba kumvera akalonga a Yuda omwe sankakonda Yehova. Kodi mukuona kuti iye anachita bwino kugwirizana ndi anthu osokonezawa? Komatu iye ankawaona ngati anzake ndipo ankawamvera. Komanso msuweni wake Zekariya atayesa kumulangiza, Yehoasi analamula kuti aphedwe. (2 Mbiri 24:20, 21; Mat. 23:35) Kumenekutu kunali kuipa mtima komanso kupusa kwambiri. Poyamba Yehoasi anali munthu wabwino koma n’zomvetsa chisoni kuti anasintha n’kukhala wampatuko komanso wakupha. Pamapeto pake atumiki ake anamupha. (2 Mbiri 24:22-25) Zinthu zikanamuyendera bwino ngati akanapitiriza kumvera Yehova komanso anthu amene ankamukonda. w23.09 38:6

Lachisanu, June 13

Usachite mantha.​—Luka 5:10.

Yesu ankadziwa kuti mtumwi Petulo akhoza kupitiriza kukhala wokhulupirika. Choncho, iye anauza Petulo mokoma mtima kuti: “Usachite mantha.” Zimene Yesu anachita posonyeza kuti ankakhulupirira Petulo, zinamuthandiza kwa moyo wake wonse. Pambuyo pake Petulo ndi m’bale wake Andireya, anasiya ntchito yawo yausodzi n’kukhala otsatira a Mesiya, zomwe zinachititsa kuti apeze madalitso ambiri. (Maliko 1:16-18) Petulo anaona zinthu zambiri zosangalatsa chifukwa chokhala wotsatira wa Khristu. Mwachitsanzo, iye anaona Yesu akuchiritsa odwala, kutulutsa ziwanda komanso kuukitsa akufa. (Mat. 8:14-17; Maliko 5:37, 41, 42) Petulo anaonanso masomphenya osonyeza ulemerero womwe Yesu adzakhale nawo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo mosakayikira zimenezi zinamulimbikitsa. (Maliko 9:1-8; 2 Pet. 1:16-18) Petulo akanapanda kutsatira Yesu, sakanaona zinthu zimenezi. Iyetu ayenera kuti anasangalala chifukwa chosalola kuti maganizo ofooketsa amulepheretse kupeza madalitso amenewa. w23.09 40:4-5

Loweruka, June 14

Yesu anamuyankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati maulendo 7 okha ayi, koma mpaka maulendo 77.”​—Mat. 18:22.

M’kalata yake yoyamba, mtumwi Petulo anagwiritsanso ntchito mawu akuti “muzikondana kwambiri.” Chikondi chimenechi chimakwirira osati machimo ochepa chabe koma “machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Mwina Petulo ankakumbukira zimene Yesu anamuphunzitsa zaka zingapo m’mbuyomo pa nkhani yokhululuka. Pa nthawiyo, iye ayenera ankakhulupirira kuti ngati atakhululukira m’bale wake “mpaka nthawi 7,” angasonyeze kuti ndi wokoma mtima. Koma Yesu anaphunzitsa Petulo ndiponso ifeyo kuti tiyenera kukhululuka “mpaka nthawi 77,” kutanthauza kuti popanda malire. (Mat. 18:21) Ngati nthawi ina zinakuvutani kutsatira malangizowa, musataye mtima. Atumiki onse a Yehova poti si angwiro, nthawi zina zimawavuta kukhululuka. Chofunika kwambiri panopa, ndi kuchita zonse zomwe mungathe kuti mukhululukire m’bale wanu ndi kukhalanso naye pamtendere. w23.09 41:12

Lamlungu, June 15

Ndinaitana inu Yehova ndipo munandiyankha.​—Yona 2:2.

Ali m’mimba mwa nsomba, Yona sankakayikira kuti Yehova amvetsera pemphero lake losonyeza kudzichepetsa komanso kulapa ndipo amuthandiza. Kenako Yehova anamupulumutsa ndipo iye anali wokonzeka kukagwira ntchito imene anamutuma. (Yona 2:10–3:4) Mukamakumana ndi mayesero, kodi mumakhala ndi nkhawa kwambiri moti mumalephera kupemphera kwa Yehova? Kapena mumafooka kwambiri moti mumalephera kuphunzira panokha? Muzikumbukira kuti Yehova amamvetsa mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Choncho ngakhale mutangopemphera mwachidule, musamakayikire kuti iye akupatsani zimene mukufunikira. (Aef. 3:20) Ngati mukulephera kuwerenga komanso kuphunzira panokha chifukwa cha mavutowo, mungayese kumvetsera zinthu zochita kujambulidwa monga Baibulo kapena mabuku athu ena. Kumvetsera nyimbo kapena kuonera vidiyo pa jw.org kukhozanso kukuthandizani. Mukamapemphera kwa Yehova komanso kugwiritsa ntchito zinthu zimene watipatsa, mumakhala mukumulola kuti akupatseni mphamvu. w23.10 43:6, 9

Lolemba, June 16

Mzimu woyera umatithandiza kumvetsa bwino kuti njira yolowera kumalo oyera inali isanaonekere pamene chihema choyambacho chinalipo.​—Aheb. 9:8.

Zinthu zimene zinkapezeka m’kati mwa chihema zinali zofanana ndi zimene zinkapezeka mu akachisi omwe anadzamangidwa ku Yerusalemu. Mkati mwake munali zipinda ziwiri: “Malo Oyera” ndi “Malo Oyera Koposa.” Zipindazi zinasiyanitsidwa ndi nsalu yopetedwa. (Aheb. 9:2-5; Eks. 26:31-33) Mkati mwa Malo Oyera munali choikapo nyale chagolide, guwa la nsembe la zofukiza ndi tebulo la mkate wachionetsero. “Ansembe odzozedwa” okha ndi amene ankaloledwa kulowa mkati mwa Malo Oyera kukagwira ntchito zawo. (Num. 3:3, 7, 10) M’malo Oyera Koposa munkakhala likasa la pangano lagolide, lomwe linkaimira kukhalapo kwa Yehova. (Eks. 25:21, 22) Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaloledwa kudutsa nsalu yotchinga kupita ku Malo Oyera Koposa pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. (Lev. 16:2, 17) Iye ankalowa ndi magazi a nyama kuti akaphimbe machimo ake komanso a Aisiraeli onse. Pamapeto pake, Yehova anafotokoza tanthauzo la zinthu zomwe zinkapezeka m’chihema.—Aheb. 9:6,7. w23.10 45:12

Lachiwiri, June 17

Muzikondana.​—Yoh. 15:17.

Mawu a Mulungu amatilamula mobwerezabwereza kuti ‘tizikondana.’ (Yoh. 15:12; Aroma 13:8; 1 Ates. 4:9; 1 Pet. 1:22; 1 Yoh. 4:11) Komabe chikondi chimakhala mumtima ndipo palibe munthu amene angaone mumtima mwathu. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda ena? Zolankhula komanso zochita zathu ndi zimene zingasonyeze. Pali njira zosiyanasiyana zomwe tingasonyezere kuti timakonda abale ndi alongo athu. Mwachitsanzo, Malemba amatilimbikitsa kuti: “Muziuzana zoona.” (Zek. 8:16) “Sungani mtendere pakati panu.” (Maliko 9:50) “Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.” (Aroma 12:10) “Muzilandirana.” (Aroma 15:7) “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana.” (Akol. 3:13) “Pitirizani kunyamulirana zinthu zolemera.” (Agal. 6:2) “Pitirizani kulimbikitsana.” (1 Ates. 4:18) “Pitirizani kutonthozana.” (1 Ates. 5:11) ‘Muzipemphererana.’—Yak. 5:16. w23.11 47:7-8

Lachitatu, June 18

Kondwerani chifukwa cha chiyembekezo.​—Aroma 12:12.

Tsiku lililonse timafunika chikhulupiriro cholimba kuti tisankhe zochita pa nkhani zosiyanasiyana monga maphunziro, zosangalatsa, anthu ocheza nawo, banja, ana komanso ntchito. Tingachite bwino kumadzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndimasankha zimasonyeza kuti sindikayikira kuti dziko loipali ndi losakhalitsa ndipo posachedwapa lilowedwa m’malo ndi dziko latsopano la Mulungu? Kapena kodi ndimasankha zinthu mofanana ndi anthu omwe amaona kuti imfa ndi mapeto a zonse?’ (Mat. 6:19, 20; Luka 12:16-21) Tingamasankhe zochita mwanzeru ngati timakhulupirira kuti dziko latsopano lili pafupi kwambiri. Timafunikanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba tikamakumana ndi mayesero. Tikhoza kuzunzidwa, kudwala matenda aakulu kapenanso kukumana ndi zinthu zina zofooketsa. Mwina poyamba tingamaone kuti titha kupirira mavuto athuwo. Koma nthawi zambiri mayesero ngati amenewo amatenga nthawi yaitali. Choncho tingafunike chikhulupiriro cholimba kuti tiwapirire komanso tipitirize kutumikira Yehova mosangalala.—1 Pet. 1:6, 7. w23.04 19:4-5

Lachinayi, June 19

Muzipemphera nthawi zonse.​—1 Ates. 5:17.

Yehova amayembekezera kuti tichita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu. Mwachitsanzo, m’bale angapemphe Yehova kuti amuthandize pamene akupempha abwana ake kuti akapezeke kumsonkhano wachigawo. Kodi Yehova angayankhe bwanji pemphero limeneli? Iye angamuthandize m’baleyo kuti alimbe mtima kukalankhula ndi abwana akewo. Koma m’baleyo ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi pempheroli popita kwa abwana akewo kukapempha. Mwinanso angafunike kupempha abwanawo mobwerezabwereza. Angathenso kupempha mnzake kuntchitoko kuti asinthane nthawi yogwirira ntchitoyo. Nthawi zina angathenso kupempha kuti asapatsidwe ndalama patsiku lomwe sanagwire ntchitolo. Yehova amayembekezera kuti tizipemphera mobwerezabwereza tikakumana ndi mavuto. Zimene Yesu ananena zimasonyeza kuti nthawi zina sitingapatsidwe nthawi yomweyo zimene tapempha. (Luka 11:9) Choncho musamataye mtima. Muzipempherabe mochokera pansi pamtima komanso mobwerezabwereza. (Luka 18:1-7) Tikamachita zimenezi, timamusonyeza Yehova kuti nkhaniyo ndi yofunika kwambiri kwa ife. Timamusonyezanso kuti timakhulupirira kwambiri kuti atithandiza. w23.11 49:10-11

Lachisanu, June 20

Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa.​—Aroma 5:5.

Yehova analonjeza Abulahamu yemwe anali mnzake kuti mitundu yonse ya padziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa mbadwa yake. (Gen. 15:5; 22:18) Popeza Abulahamu ankakhulupirira kwambiri Mulungu, sankakayikira kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa. Ngakhale zinali choncho, Abulahamu anali ndi zaka 100 ndipo mkazi wake zaka 90, koma banja lokhulupirikali linalibe mwana. (Gen. 21:1-7) Koma Baibulo limati: “Abulahamu anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri . . . mogwirizana ndi zimene zinanenedwa.” (Aroma 4:18) Inu mukudziwa kuti zimene Abulahamu ankayembekezerazi zinakwaniritsidwa. Iye anabereka mwana wamwamuna dzina lake Isaki, yemwe anamuyembekezera kwa nthawi yaitali. Kodi n’chiyani chinamuthandiza Abulahamu kuti asamakayikire zimene Mulungu anamulonjeza? Chifukwa chakuti anali pa ubwenzi ndi Yehova, Abulahamu “sankakayikira kuti zimene Mulungu analonjeza,” zidzakwaniritsidwa. (Aroma 4:21) Yehova anasangalala ndi Abulahamu, ndipo anamutchula kuti anali wolungama chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro.—Yak. 2:23. w23.12 51:1-2

Loweruka, June 21

Munthu amene ndi wokhulupirika pa chinthu chaching’ono amakhalanso wokhulupirika pa chinthu chachikulu, ndipo munthu amene ndi wosakhulupirika pa chinthu chaching’ono amakhalanso wosakhulupirika pa chinthu chachikulu.—Luka 16:10.

Wachinyamata wodalirika, amakwaniritsa maudindo ake mokhulupirika. Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Iye sankachita zinthu mosasamala kapena mosaikirapo mtima. M’malomwake anachita zinthu zonse zomwe Yehova anamutuma, ngakhale pamene kuchita zimenezi kunali kovuta. Yesu ankakonda anthu makamaka ophunzira ake, ndipo mofunitsitsa anapereka moyo wake chifukwa cha iwo. (Yoh. 13:1) Potsanzira Yesu, muzigwira mwakhama ntchito iliyonse yomwe mwapatsidwa. Ngati simukudziwa mmene mungachitire zinthu zina, muyenera kukhala odzichepetsa ndi kumapempha abale olimba mwauzimu kuti akuthandizeni. Musamakhutire ndi kungochita zochepa chabe. (Aroma 12:11) M’malomwake, muzimaliza ntchito yonse imene mwapatsidwa ngati “mukuchitira Yehova, osati anthu.” (Akol. 3:23) Komabe, muzikumbukira kuti si inu angwiro choncho muzidziwa malire anu n’kumavomereza zimene mwalakwitsa.—Miy. 11:2. w23.12 53:8

Lamlungu, June 22

Munthu amene amakhulupirira Yehova . . . ndi amene amadalitsidwa.​—Yer. 17:7.

Timasangalala tikabatizidwa n’kukhala m’banja la Yehova. Anthu amene anabatizidwa angagwirizane ndi zimene Davide analemba, pomwe anati: “Wosangalala ndi munthu amene inu Yehova mwamusankha nʼkumubweretsa pafupi ndi inu, kuti akhale mʼmabwalo anu.” (Sal. 65:4) Sikuti Yehova amangolola aliyense kuti alowe m’mabwalo ake. Iye amasankha anthu amene asonyeza kuti akufunitsitsa kukhala naye pa ubwenzi. (Yak. 4:8) Ndiye mukadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, mungakhale otsimikiza kuti ‘adzakukhuthulirani madalitso mpaka simudzasowa kanthu.’ (Mal. 3:10; Yer. 17:8) Kubatizidwa chimangokhala chiyambi chabe. Koma pambuyo pake, mumayenera kuchita zonse zomwe mungathe kuti muzikwaniritsa lonjezo lanu ngakhale pamene mukukumana ndi mayesero. (Mlal. 5:4, 5) Monga wophunzira wa Yesu, mumafunika kutengera chitsanzo chake komanso kumvera malamulo ake mosamala kwambiri.—Mat. 28:19, 20; 1 Pet. 2:21. w24.03 10:1-3

Lolemba, June 23

Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake.​—Gen. 2:24.

Koma bwanji ngati inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu simusangalala kuchitira zinthu limodzi? Ndiye kodi mungatani? Taganizirani za moto. Moto sumangofikira kuyaka mwamphamvu. Umafunika kusonkhezera pang’onopang’ono, kenako n’kumaika nkhuni zazikulu. Mofanana ndi zimenezi, bwanji osayamba ndi kumapeza nthawi yochepa tsiku lililonse yochitira zinthu limodzi? Muzionetsetsa kuti muzichita zinthu zomwe nonse mumasangalala nazo. (Yak. 3:18) Kuyamba mwapang’onopang’ono kungathandize kuti mukulitse chikondi chanu. Kulemekezana n’kofunika kwambiri m’banja. Tingakuyerekezere ndi mpweya, womwe umathandiza kuti moto uziyaka kwambiri. Popanda mpweyawu, moto ukhoza kuzima mofulumira. Mofanana ndi zimenezi, ngati anthu okwatirana sakulemekezana, chikondi chawo chikhoza kuchepa mofulumira. Koma mwamuna ndi mkazi wake akamayesetsa kuti azilemekezana, zimathandiza kuti chikondi chawo chizikula. Muzikumbukira kuti si nkhani yongoti inuyo mumaganiza kuti mumalemekeza mnzanuyo koma kuti iyeyo aziona kuti mumamulemekeza. w23.05 23:9, 14-15

Lachiwiri, June 24

Nkhawa zitandichulukira, munanditonthoza komanso kundisangalatsa.​—Sal. 94:19.

Atumiki ena okhulupirika a Mulungu ananenapo za nthawi imene anada nkhawa kapena kunjenjemera chifukwa cha adani awo kapena mavuto ena. (Sal. 18:4; 55:1, 5) Nafenso tikhoza kutsutsidwa kusukulu, kuntchito, ndi anthu a m’banja lathu kapenanso ndi boma. Apo ayi tikhoza kudwala mwakayakaya. Pa nthawi ngati imeneyi tikhoza kukhala ngati kamwana kamene kakusowa mtengo wogwira. Kodi Yehova amatithandiza bwanji pa nthawi ngati imeneyi? Iye amatitonthoza komanso kutilimbikitsa. Choncho tizilankhula ndi Yehova pafupipafupi popemphera kwa iye komanso kuwerenga Mawu ake. (Sal. 77:1, 12-14) Tikatero, tikadzakumana ndi mavuto, choyambirira kuchita chidzakhala kupemphera kwa Atate wathu wakumwamba. Muzimufotokozera Yehova zimene zikukuchititsani mantha komanso kukudetsani nkhawa. Muzimulola kuti akulankhuleni komanso kukutonthozani kudzera m’Malemba.—Sal. 119:28. w24.01 3:14-16

Lachitatu, June 25

Mulungu ndi amene . . . amakupatsani mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.​—Afil. 2:13.

Timafunika kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuti tikwaniritse zolinga zauzimu. Munthu akakhala ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chake amachita khama. Muzipempha Yehova kuti mukhale ndi mtima wofunitsitsa. Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Yehova angakuthandizeni kukhala mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chanu. Nthawi zina timadziikira cholinga chifukwa timadziwa kuti ndi zimene tiyenera kuchita, ndipotu ndi bwino kuchita zimenezi. Koma mwina sitingakhale ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholingacho. Muziganizira zimene Yehova wakuchitirani. (Sal. 143:5) Mtumwi Paulo anaganizira mozama mmene Yehova anamusonyezera kukoma mtima kwake kwakukulu ndipo izi zinamulimbikitsa kuti azichita khama pomutumikira. (1 Akor. 15:9, 10; 1 Tim. 1:12-14) Mofanana ndi zimenezi, inunso mukamaganizira kwambiri zimene Yehova wakuchitirani, mudzakhala ofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chanu.—Sal. 116:12. w23.05 24:3-5

Lachinayi, June 26

Tamandani dzina la Yehova.​—Sal. 113:1.

Timasangalatsa Atate wathu wakumwamba tikamatamanda dzina lake. (Sal. 119:108) Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu Wamphamvuyonse ali ngati anthu omwe si angwiro, amene amafuna kutamandidwa chifukwa chofuna kuti azidziona kuti ndi ofunika? Ayi. Tikamatamanda Atate wathu wakumwamba timathandiza kutsutsa bodza lomwe Satana ananena, limene limakhudzanso munthu aliyense. Satana amanena kuti palibe munthu amene angakhale wokhulupirika atakumana ndi mayesero pothandiza kuti dzina la Mulungu lisadetsedwe. Iye amanena kuti tingasiye kutumikira Mulungu ngati titaona kuti kuchita zimenezo kungachititse kuti tikumane ndi mavuto. (Yobu 1:9-11; 2:4) Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Nanga bwanji inuyo? Aliyense wa ife ali ndi mwayi wothandiza kuti dzina la Atate wathu lisadetsedwe komanso kumusangalatsa popitirizabe kumutumikira mokhulupirika. (Miy. 27:11) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. w24.02 6:3-5

Lachisanu, June 27

Khulupirirani aneneri ake kuti zinthu zikuyendereni bwino.​—2 Mbiri 20:20.

Mose ndi Yoswa atamwalira, Yehova anasankha oweruza kuti azitsogolera anthu ake. Kenako, m’nthawi ya mafumu, Yehova ankasankha aneneri kuti azipereka malangizo kwa anthu ake. Mafumu okhulupirika ankatsatira malangizo a aneneriwa. Mwachitsanzo, Davide anamvera modzichepetsa atadzudzulidwa ndi mneneri Natani. (2 Sam. 12:7, 13; 1 Mbiri 17:3, 4) Mfumu Yehosafati inkadalira malangizo a mneneri Yahazieli ndipo inalimbikitsa anthu a ku Yuda kuti ‘azikhulupirira aneneri a [Mulungu].’ (2 Mbiri 20:14, 15) Atathedwa nzeru, Mfumu Hezekiya anapempha malangizo kwa mneneri Yesaya. (Yes. 37:1-6) Nthawi zonse mafumu akamatsatira malangizo a Yehova, ankadalitsidwa ndipo mtundu wonse unkakhala wotetezeka. (2 Mbiri 20:29, 30; 32:22) Zinali zoonekeratu kuti Yehova ankagwiritsa ntchito aneneriwo potsogolera anthu ake. w24.02 8:8

Loweruka, June 28

Musamachite zimene iwo amachita.—Aef. 5:7.

Satana amafuna kuti tizigwirizana ndi anthu amene angachititse kuti tisamamvere mfundo za Yehova. Tizikumbukira kuti anthu amene timagwirizana nawo si amene timacheza nawo pamasom’pamaso okha. Anthuwa akuphatikizapo amene timacheza nawo pa intaneti. Tiyenera kupewa maganizo a m’dzikoli akuti khalidwe lachiwerewere si lolakwika. Ifeyo timadziwa kuti maganizo amenewa ndi olakwika. (Aef. 4:19, 20) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kupewa kucheza mosayenera ndi anzanga a kuntchito, kusukulu kapena anthu ena amene salemekeza mfundo zolungama za Yehova? Kodi ndimalolera kutsatira mfundo za Yehova ngakhale ena azindiona kuti ndine wovuta?’ Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 2:20-22, tiyenera kukhalanso osamala pamene tikusankha anzathu mumpingo. Tizikumbukira kuti ena sangatithandize kukhalabe okhulupirika potumikira Yehova. w24.03 12:11-12

Lamlungu, June 29

Yehova ndi wachikondi chachikulu.—Yak. 5:11.

Kodi munayamba mwaganizirapo kuti Yehova ndi wotani? Ngakhale kuti sitingathe kumuona, Baibulo limamufotokoza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Yehova amatchedwa “dzuwa ndiponso chishango” komanso “moto wowononga.” (Sal. 84:11; Aheb. 12:29) Amafotokozedwanso kuti ali ngati mwala wa safiro, chitsulo chowala komanso utawaleza. (Ezek. 1:26-28) Popeza kuti sitingathe kuona Yehova, mwina zingativute kukhulupirira kuti amatikonda. Ena amaganiza kuti Yehova samawakonda chifukwa cha zinthu zoipa zomwe zinawachitikira m’mbuyomu. Yehova amamvetsa mmene timamvera ndipo amadziwa mmene zimenezi zimachititsira kuti zikhale zovuta kuti tikhale naye pa ubwenzi. Choncho pofuna kutithandiza, iye amatifotokozera makhalidwe ake osangalatsa kudzera m’Mawu ake. Mawu amodzi omwe amafotokoza bwino Yehova ndi chikondi. (1 Yoh. 4:8) Baibulo limati Mulungu ndi chikondi. Zilizonse zimene amachita, amazichita chifukwa cha chikondi. Chikondi chake ndi champhamvu kwambiri moti amachisonyeza ngakhale kwa anthu omwe samukonda.—Mat. 5:44, 45. w24.01 4:1-3

Lolemba, June 30

Ankalankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo.​—Sal. 99:7.

Yehova anasankha Mose kuti atsogolere Aisiraeli potuluka ku Iguputo ndipo anawapatsa umboni wooneka, masana ankawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo ndipo usiku pogwiritsa ntchito chipilala cha moto. (Eks. 13:21) Mose ankatsatira chipilalacho chomwe chinatsogolera iyeyo ndi Aisiraeli ku Nyanja Yofiira. Anthuwo anachita mantha kwambiri poganiza kuti asowa kolowera chifukwa kutsogolo kwawo kunali nyanja ndipo kumbuyo kunali asilikali a Iguputo. Koma sikuti Mose analakwitsa. Yehova ndi amene anatsogolera anthu akewo kumeneko pogwiritsa ntchito Mose. (Eks. 14:2) Kenako iye anawapulumutsa m’njira yodabwitsa kwambiri. (Eks. 14:26-28) Pa zaka 40 zotsatira, Mose anapitiriza kudalira chipilala cha mtambo potsogolera anthu a Mulungu m’chipululu. (Eks. 33:7, 9, 10) Yehova ankalankhula ndi Mose kudzera m’chipilalacho ndipo Mose ankapereka malangizo a Yehovawo kwa anthu. Aisiraeli anali ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti Yehova ankagwiritsa ntchito Mose powatsogolera. w24.02 8:4-5

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani