MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzikhala Okhulupirika Mukakumana ndi Mayesero
Onerani vidiyo yakuti Muzikhala Okhulupirika Ngati mmene Yesu Analili—Pamene Mukuyesedwa (imapezeka pamene palembedwa kuti BAIBULO), kenako yankhani mafunso otsatirawa:
- Kodi Segi anakumana ndi mayesero otani amene akanamuchititsa kuti asakhale wokhulupirika kwa Mulungu? 
- Kodi n’chiyani chinathandiza Segi kuti akhalebe wokhulupirika? 
- Kodi kukhulupirika kwake kunathandiza bwanji kuti Yehova alemekezedwe?