Lachiwiri, October 28
[Yehova] adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.—Yes. 33:6.
Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupirika a Yehova, mofanana ndi anthu onse, timakumana ndi mavuto komanso matenda. Nthawi zinanso timatsutsidwa kapena kuzunzidwa ndi anthu odana ndi anthu a Mulungu. Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mavuto, koma amatilonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Iye akatithandiza timapitirizabe kukhala osangalala, timasankha zinthu mwanzeru komanso timakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale pamene zili zovuta kutero. Yehova amatilonjeza kuti atipatsa “mtendere [wake]” wotchulidwa m’Baibulo. (Afil. 4:6, 7) Munthu akakhala ndi mtendere umenewu, mtima ndi maganizo ake zimakhala m’malo chifukwa choti ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mtenderewu ndi woti “anthu sangathe kuumvetsa” ndipo ndi wodabwitsa kuposa mmene tingaganizire. Kodi inunso mtima wanu unayamba wakhalapo m’malo mutapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima? Munamva choncho chifukwa cha “mtendere wa Mulungu.” w24.01 3:2, 4
Lachitatu, October 29
Moyo wanga utamande Yehova. Chilichonse cha mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.—Sal. 103:1.
Kukonda Mulungu kumachititsa anthu okhulupirika kuti azitamanda dzina lake ndi mtima wonse. Mfumu Davide ankadziwa kuti kutamanda dzina la Yehova kumatanthauza kutamanda Yehovayo. Choncho tikamva dzinali timaganizira makhalidwe ake abwino komanso ntchito zake zodabwitsa. Davide ankafuna aziona kuti dzina la Atate wake ndi loyera komanso kumalitamanda. Iye ankafuna azichita zimenezo ndi “chilichonse cha mkati [mwake]” kapena kuti ndi mtima wonse. Mofanana ndi Davide, Alevi nawonso ankatsogolera potamanda Yehova. Modzichepetsa, iwo anavomereza kuti mawu awo sakanatha kufotokoza mokwanira ulemerero umene dzina loyera la Yehova liyenera kulandira. (Neh. 9:5) Mosakayikira, Yehova anasangalala ndi kudzichepetsa komanso kumutamanda kochokera pansi pamtima kumeneku. w24.02 6:6
Lachinayi, October 30
Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.—Afil. 3:16.
Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephera chifukwa simunakwaniritse cholinga chimene simukanatha kuchikwaniritsa. (2 Akor. 8:12) Muziphunzirapo kathu mukakumana ndi zolepheretsa. Muziganizira zomwe mwakwanitsa kale kuchita. Baibulo limanena kuti “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.” (Aheb. 6:10) Choncho inunso musamaiwale zomwe mwachita. Muziganizira zolinga zomwe mwazikwaniritsa kale kaya ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, kuuza ena zokhudza iye kapena kubatizidwa. Monga mmene mwakhala mukukwaniritsira zolinga zanu m’mbuyomu, mungapitirizenso kukwaniritsa cholinga chanu panopa. Mothandizidwa ndi Yehova, inunso mungathe kukwaniritsa cholinga chanu mofanana ndi woyendetsa boti yemwe amasangalala akafika kumene akupita. Koma kumbukirani kuti oyendetsa boti ambiri amasangalalanso ndi ulendo wawo. Inunso mukayesetsa kuti mukwaniritse cholinga chanu chauzimu, muzisangalala ndi mmene Yehova akukuthandizirani komanso kukudalitsirani. (2 Akor. 4:7) Ndipo ngati simungafooke mudzapeza madalitso ambiri.—Agal. 6:9. w23.05 24:16-18