Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachinayi, October 30

Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.​—Afil. 3:16.

Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephera chifukwa simunakwaniritse cholinga chimene simukanatha kuchikwaniritsa. (2 Akor. 8:12) Muziphunzirapo kathu mukakumana ndi zolepheretsa. Muziganizira zomwe mwakwanitsa kale kuchita. Baibulo limanena kuti “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.” (Aheb. 6:10) Choncho inunso musamaiwale zomwe mwachita. Muziganizira zolinga zomwe mwazikwaniritsa kale kaya ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, kuuza ena zokhudza iye kapena kubatizidwa. Monga mmene mwakhala mukukwaniritsira zolinga zanu m’mbuyomu, mungapitirizenso kukwaniritsa cholinga chanu panopa. Mothandizidwa ndi Yehova, inunso mungathe kukwaniritsa cholinga chanu mofanana ndi woyendetsa boti yemwe amasangalala akafika kumene akupita. Koma kumbukirani kuti oyendetsa boti ambiri amasangalalanso ndi ulendo wawo. Inunso mukayesetsa kuti mukwaniritse cholinga chanu chauzimu, muzisangalala ndi mmene Yehova akukuthandizirani komanso kukudalitsirani. (2 Akor. 4:7) Ndipo ngati simungafooke mudzapeza madalitso ambiri.—Agal. 6:9. w23.05 24:16-18

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachisanu, October 31

Atatewo amakukondani chifukwa munandikonda ndipo mwakhulupirira kuti ine ndinabwera monga nthumwi ya Mulungu.​—Yoh. 16:27.

Yehova amafunitsitsa kuuza anthu omwe amawakonda kuti amasangalala nawo. Malemba amatchula nthawi ziwiri pomwe iye anauza Yesu kuti ndi Mwana wake wokondedwa ndipo amasangalala naye. (Mat. 3:17; 17:5) Kodi mungakonde kumva Yehova akukutsimikizirani kuti amasangalala nanu? Iye salankhula nafe mwachindunji koma amatilankhula kudzera m’Mawu ake. ‘Tingamve’ mawu a Yehova onena kuti amasangalala nafe tikamawerenga mawu a Yesu m’mabuku a Uthenga Wabwino. Yesu ankatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake. Choncho tikamawerenga kuti Yesu ankasangalala ndi otsatira ake okhulupirika, omwe sanali angwiro, timadziwa kuti Yehova amasangalalanso ndi ifeyo. (Yoh. 15:9, 15) Tikakumana ndi mavuto sizitanthauza kuti Mulungu sakusangalala nafe. M’malomwake, zimenezi zimatipatsa mwayi wosonyeza kuti timakonda kwambiri Mulungu ndipo timamukhulupirira.—Yak. 1:12. w24.03 13:10-11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Loweruka, November 1

Mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda.​—Mat. 21:16.

Ngati ndinu makolo, muzithandiza ana anu kukonzekera ndemanga zogwirizana ndi msinkhu wawo. Nthawi zina pamisonkhano timaphunzira nkhani zikuluzikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena makhalidwe. Komabe pangathe kukhala ndime imodzi kapena ziwiri zomwe mwana akhoza kuyankhapo. Komanso muzithandiza ana anu kumvetsa chifukwa chake sangalozedwe nthawi iliyonse yomwe akweza dzanja. Kuwafotokozera zimenezi kungawathandize kuti asamakhumudwe ena akalozedwa m’malo mwa iwowo. (1 Tim. 6:18) Tonsefe tingakonzekere ndemanga zomwe zingalemekeze Yehova komanso zingalimbikitse Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafotokoze mwachidule zimene zinatichitikirapo, tizipewa kulankhula kwambiri zokhudza ifeyo. (Miy. 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malomwake, tiziyesetsa kuganizira kwambiri zokhudza Yehova, Mawu ake komanso anthu ake monga gulu. w23.04 18:17-18

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani