Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachitatu, November 5

Mulungu adzatipatsa mphamvu.​—Sal. 108:13.

Kodi mungatani kuti chiyembekezo chanu chikhale champhamvu? Mwachitsanzo, ngati mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, muziwerenga ndiponso kuganizira zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Paradaiso. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Muziyerekezera muli m’dzikolo. Tikamaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha dziko latsopano, mavuto athu adzaoneka kuti ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.” (2 Akor. 4:17) Chiyembekezo chimene Yehova wakupatsani chingakuthandizeni kuti mupirire mayesero. Iye wapereka kale zinthu zomwe zingatithandize kuti tipeze mphamvu. Choncho ngati tikufuna kuti atithandize kuti tichite bwino utumiki wathu, tipirire mayesero kapena tikhalebe osangalala, tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima ndiponso kufufuza malangizo ake pophunzira Baibulo patokha. Tizilolanso kuti abale ndi alongo atilimbikitse. Nthawi zonse tiziganizira za chiyembekezo chathu. Tikatero tidzalandira ‘mphamvu zazikulu mogwirizana ndi mphamvu zake zochititsa mantha, n’cholinga choti tithe kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe.’—Akol. 1:11. w23.10 43:19-20

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachinayi, November 6

Muzithokoza pa chilichonse.​—1 Ates. 5:18.

Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova m’mapemphero athu. Tingamuyamikire chifukwa cha zabwino zimene tili nazo. Ndipotu mphatso iliyonse yabwino imachokera kwa iye. (Yak. 1:17) Mwachitsanzo, tingamuthokoze chifukwa cha dziko lokongolali komanso zinthu zochititsa chidwi zam’chilengedwe. Tingamuthokozenso chifukwa chotipatsa moyo, banja, anzathu komanso chiyembekezo. Timafunanso kuyamikira Yehova chifukwa chotilola kusangalala ndi ubwenzi wamtengo wapatali womwe tili nawo ndi iye. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tiziganizira zifukwa zomwe zimatichititsa kuti tiziyamikira Yehova. Anthu ambiri m’dzikoli ndi osayamika. Nthawi zambiri iwo amangoganizira zimene akufuna, osati zimene angachite kuti asonyeze kuyamikira zimene ali nazo. Ngati titatengera maganizo amenewa, ndiye kuti mapemphero athu akhoza kukhala omangopempha. Kuti zimenezi zisatichitikire, tiyenera kumayesetsa kukhala ndi mtima woyamikira zonse zimene Yehova amatichitira.—Luka 6:45. w23.05 20:8-9

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachisanu, November 7

Azipempha ndi chikhulupiriro, asamakayikire ngakhale pang’ono.​—Yak. 1:6.

Yehova ndi Bambo wathu wachikondi ndipo sasangalala kutiona tikuvutika. (Yes. 63:9) Komabe iye satiteteza ku mavuto onse amene timakumana nawo, omwe ali ngati mitsinje kapena malawi a moto. (Yes. 43:2) Ngakhale zili choncho, iye amatilonjeza kuti angatithandize ‘kudutsa,’ kapena kuti kupirira zinthu ngati zimenezi. Iye sadzalola kuti mavuto atilepheretse kukhalabe okhulupirika kwa iye. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu kuti utithandize kupirira. (Luka 11:13; Afil. 4:13) Choncho sitikayikira kuti tidzakhala ndi zonse zomwe timafunikira kuti tipirire komanso tikhalebe okhulupirika kwa iye. Yehova amayembekezera kuti tizimudalira. (Aheb. 11:6) Nthawi zina mavuto athu angaoneke aakulu moti sitingathe kuwapirira. Mwinanso tingakayikire ngati Yehova angatithandize. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti ndi mphamvu za Mulungu, ‘tingakwere khoma.’ (Sal. 18:29) Choncho m’malo mokayikira, tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro chonse kuti ayankha mapemphero athu.—Yak. 1:6, 7. w23.11 49:8-9

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani