Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Lachiwiri, November 4

Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?​—Hos. 13:14.

Kodi Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa akufa? N’zosachita kufunsa. Iye anauzira anthu angapo kuti alembe m’Baibulo lonjezo lake lakuti adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Chiv. 20:11-13) Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwaniritsa zomwe walonjezazo. (Yos. 23:14) Ndipotu iye ndi wofunitsitsa kudzaukitsa anthu amene anamwalira. Taganizirani zomwe Yobu analankhula. Iye sankakayikira kuti ngakhale atamwalira, Yehova adzalakalaka kumuonanso ali ndi moyo. (Yobu 14:14, 15) Yehova amafunitsitsanso kudzaukitsa atumiki ake onse amene anamwalira, kuti akhale athanzi komanso osangalala. Nanga bwanji za anthu mabiliyoni omwe anamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Yehova? Mulungu wathu wachikondi amafunanso kudzawaukitsa. (Mac. 24:15) Iye amafuna kuti iwo akhale ndi mwayi wokhala anzake komanso kuti adzakhale ndi mwayi wokhala padzikoli mpaka kalekale.—Yoh. 3:16. w23.04 16:5-6

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachitatu, November 5

Mulungu adzatipatsa mphamvu.​—Sal. 108:13.

Kodi mungatani kuti chiyembekezo chanu chikhale champhamvu? Mwachitsanzo, ngati mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, muziwerenga ndiponso kuganizira zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Paradaiso. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Muziyerekezera muli m’dzikolo. Tikamaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha dziko latsopano, mavuto athu adzaoneka kuti ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.” (2 Akor. 4:17) Chiyembekezo chimene Yehova wakupatsani chingakuthandizeni kuti mupirire mayesero. Iye wapereka kale zinthu zomwe zingatithandize kuti tipeze mphamvu. Choncho ngati tikufuna kuti atithandize kuti tichite bwino utumiki wathu, tipirire mayesero kapena tikhalebe osangalala, tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima ndiponso kufufuza malangizo ake pophunzira Baibulo patokha. Tizilolanso kuti abale ndi alongo atilimbikitse. Nthawi zonse tiziganizira za chiyembekezo chathu. Tikatero tidzalandira ‘mphamvu zazikulu mogwirizana ndi mphamvu zake zochititsa mantha, n’cholinga choti tithe kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe.’—Akol. 1:11. w23.10 43:19-20

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachinayi, November 6

Muzithokoza pa chilichonse.​—1 Ates. 5:18.

Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova m’mapemphero athu. Tingamuyamikire chifukwa cha zabwino zimene tili nazo. Ndipotu mphatso iliyonse yabwino imachokera kwa iye. (Yak. 1:17) Mwachitsanzo, tingamuthokoze chifukwa cha dziko lokongolali komanso zinthu zochititsa chidwi zam’chilengedwe. Tingamuthokozenso chifukwa chotipatsa moyo, banja, anzathu komanso chiyembekezo. Timafunanso kuyamikira Yehova chifukwa chotilola kusangalala ndi ubwenzi wamtengo wapatali womwe tili nawo ndi iye. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tiziganizira zifukwa zomwe zimatichititsa kuti tiziyamikira Yehova. Anthu ambiri m’dzikoli ndi osayamika. Nthawi zambiri iwo amangoganizira zimene akufuna, osati zimene angachite kuti asonyeze kuyamikira zimene ali nazo. Ngati titatengera maganizo amenewa, ndiye kuti mapemphero athu akhoza kukhala omangopempha. Kuti zimenezi zisatichitikire, tiyenera kumayesetsa kukhala ndi mtima woyamikira zonse zimene Yehova amatichitira.—Luka 6:45. w23.05 20:8-9

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani