Lamlungu, September 14
[Muzitha] kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwera ndi kuzama kwa choonadi.—Aef. 3:18.
Mukafuna kugula nyumba mungafune kudziwa kalikonse kokhudza nyumbayo. Tingachitenso zofanana ndi zimenezi pamene tikuwerenga komanso kuphunzira Baibulo. Ngati mutaliwerenga mofulumira, mukhoza kungodziwa “mfundo zoyambirira za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) Koma mofanana ndi zimene mungachite ndi nyumba ija, muyenera kulowa “mkati” kapena kuti kuliphunzira mosamala kuti mulimvetse. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo ndi kuona mmene mbali zosiyanasiyana za uthenga wake zilili zogwirizana. Muziyesetsa kuti mumvetse, osati mfundo za choonadi zomwe mumakhulupirira zokha, koma chifukwa chakenso mumazikhulupirira. Kuti tizimvetsa bwino Mawu a Mulungu, tiyenera kumaphunzira mosamala mfundo zozama za choonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa abale ndi alongo ake kuti aziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama n’cholinga choti ‘adziwe bwino mulifupi ndi mulitali ndi kukwera ndi kuzama’ kwa choonadi. Iwo akanachita zimenezi, ‘akanazika mizu ndi kukhala okhazikika’ m’chikhulupiriro chawo. (Aef. 3:14-19) Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. w23.10 44:1-3
Lolemba, September 15
Abale, pa nkhani ya kumva zowawa ndi kuleza mtima, tengerani chitsanzo cha aneneri amene analankhula m’dzina la Yehova.—Yak. 5:10.
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Bwanji osakonza zoti mufufuze zitsanzozi pamene mukuphunzira Baibulo panokha? Mwachitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa ali mwana kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli, anafunika kudikira kwa zaka zambiri asanapatsidwe ufumuwo. Simiyoni ndi Anna ankatumikira Yehova mokhulupirika pamene ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaphunzira nkhanizi muzifufuza mayankho a mafunso awa: Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza munthuyu kuti akhale woleza mtima? Kodi kukhala woleza mtima kunamuthandiza bwanji? Kodi ndingamutsanzire bwanji? Mungapindulenso ngati mutaphunzira za anthu omwe sanasonyeze kuleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘Kodi mwina n’chiyani chinachititsa kuti asakhale woleza mtima? Nanga zotsatirapo zake zinali zotani?’ w23.08 35:15
Lachiwiri, September 16
Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera amene Mulungu anamutumiza.—Yoh. 6:69.
Mtumwi Petulo anali wokhulupirika ndipo sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kutsatira Yesu. Iye anasonyeza kukhulupirika kwake pa nthawi ina pamene Yesu analankhula zinthu zimene ophunzira ake sanazimvetse. (Yoh. 6:68) Anthu ambiri anasiya kutsatira Yesu popanda kudikira kuti awafotokozere zimene ankatanthauza. Koma Petulo ankadziwa kuti Yesu yekha, ndi yemwe ali ndi “mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.” Yesu ankadziwa kuti Petulo ndi atumwi ena amusiya yekha. Komabe sankakayikira kuti Petulo adzabwerera n’kukhalabe wokhulupirika. (Luka 22:31, 32) Yesu ankadziwa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38). Choncho ngakhale kuti Petulo anamukana kuti sakumudziwa, iye sanasiye kukonda mtumwi wakeyu. Ataukitsidwa, Yesu anakumana ndi Petulo ndipo zikuoneka kuti Petuloyo anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mtumwiyu, yemwe ankadzimvera chisoni kwambiri. w23.09 40:9-10