September
Lolemba, September 1
Kuwala kwam’mawa kudzatifikira kuchokera kumwamba.—Luka 1:78.
Mulungu wapatsa Yesu mphamvu zothetsa mavuto onse a anthu. Pochita zozizwitsa, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zothetsera mavuto omwe sitingathe kuwathetsa patokha. Mwachitsanzo, iye ali ndi mphamvu yotipulumutsa ku zimene zinayambitsa mavuto a anthu, zomwe ndi uchimo umene tinatengera komanso zotsatirapo zake monga matenda ndi imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zomwe anachita, zimasonyeza kuti iye angathe kuchiritsa “matenda amtundu uliwonse” ngakhalenso kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Alinso ndi mphamvu yotha kuletsa mphepo zamkuntho komanso kugonjetsa mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova wapatsa Mwana wake mphamvu zochitira zimenezi. Sitikayikira kuti malonjezo omwe tikuyembekezera mu Ufumu wa Mulungu adzakwaniritsidwa. Zozizwitsa zimene Yesu anachita ali munthu padzikoli, zimatiphunzitsa kuti monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzachita zambiri m’tsogolomu. w23.04 15:5-7
Lachiwiri, September 2
Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.—1 Akor. 2:10.
N’kutheka kuti abale ndi alongo ambiri amakonda kuyankha pamisonkhano moti nthawi zambiri mukakweza dzanja sakulozani. Choncho mungaganize kuti bola kungosiya kuyankha. Koma simuyenera kusiya kuyesetsa kuti muyankhe pamisonkhano. Mungachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo pamsonkhano uliwonse. Choncho ngati simunalozedwe kuti muyankhe kumayambiriro kwa phunziro, mungakhalebe ndi mwayi woyankha mkati mwa misonkhanoyo. Mukamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, muziganizira mmene ndime iliyonse ikugwirizanirana ndi mutu wa nkhaniyo. Mukamachita zimenezo mungakhale ndi mfundo zoti muyankhe m’phunziro lonselo. Mungakonzekere kuti mukayankhe pa ndime zimene zikufotokoza mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi zovuta kuzifotokoza. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwina pangakhale anthu ochepa oimika manja kuti ayankhe pa mbali imeneyi. Koma bwanji ngati pamisonkhano ingapo mwaonabe kuti simunapatsidwe mwayi woyankha? Misonkhano isanayambe mungauze amene akuchititsa phunzirolo funso limene mukufuna kuyankha. w23.04 18:9-10
Lachitatu, September 3
Yosefe anadzuka n’kuchita mogwirizana ndi zimene mngelo wa Yehova anamuuza. Anatenga mkazi wake n’kupita naye kunyumba.—Mat. 1:24.
Yosefe ankakhala wokonzeka kutsatira malangizo a Yehova ndipo izi zinachititsa kuti akhale mwamuna wabwino. Pa nthawi zosachepera zitatu, analandira malangizo ochokera kwa Mulungu okhudza banja lake. Pa nthawi zonsezi ankamvera ndi mtima wonse, ngakhale pamene zinali zovuta kutero. (Mat. 1:20, 24; 2:13-15, 19-21) Chifukwa chotsatira malangizo a Mulungu, Yosefe anateteza, kuthandiza komanso kusamalira Mariya. Taganizirani mmene zochita za Yosefe zinathandizira Mariya kuti azimukonda komanso azimulemekeza kwambiri. Amuna, mungatsanzire Yosefe pofufuza ndi kutsatira malangizo a m’Baibulo okhudza mmene mungasamalire banja lanu. Mukamatsatira malangizowa, ngakhale kuti mungafunike kusintha zinthu zina, mumasonyeza kuti mumakonda mkazi wanu komanso mumalimbitsa banja lanu. Mlongo wina wa ku Vanuatu, yemwe wakhala pabanja kwa zaka zoposa 20, anati: “Mwamuna wanga akamafufuza komanso kutsatira malangizo a Yehova, ndimamulemekeza kwambiri. Ndimadzimva kukhala wotetezeka komanso sindikayikira zimene wasankha.” w23.05 23:5
Lachinayi, September 4
Kumeneko kudzakhala msewu waukulu. Inde msewu umene udzatchedwe Msewu Wopatulika.—Yes. 35:8.
Ayuda obwerera kwawo kuchokera ku Babulo akanakhala “anthu oyera” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe zimenezi sizinkatanthauza kuti iwo sankafunika kusintha zinthu zina kuti azisangalatsa Yehova. Ambiri mwa Ayuda omwe anabadwira ku Babulo ankatsatira kaganizidwe ndi mfundo za anthu akumeneko. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene Ayuda oyambirira anabwerera ku Isiraeli, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa atapeza kuti ana ena omwe anabadwira ku Isiraeli, sankadziwa chilankhulo cha Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Kodi ana amenewa akanaphunzira bwanji kukonda komanso kulambira Yehova ngati sankadziwa Chiheberi, chilankhulo chomwe chinagwiritsidwa ntchito polemba Mawu a Mulungu? (Ezara 10:3, 44) Choncho panali zinthu zambiri zomwe Ayuda ankafunika kusintha. Koma zikanakhala zosavuta kusintha ngati akanakhala ku Isiraeli kumene kulambira koona kunkabwezeretsedwa pang’onopang’ono.—Neh. 8:8, 9. w23.05 22:6-7
Lachisanu, September 5
Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pang’ono kugwa ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.—Sal. 145:14.
Ngakhale titayesetsa kukhala odziletsa kapena kukhala ndi mtima wofunitsitsa, tingakumanebe ndi zolepheretsa. Mwachitsanzo, “zinthu zosayembekezereka” zingatiwonongere nthawi yomwe timafunika kukwaniritsa cholinga chathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane ndi vuto lomwe lingachititse kuti tifooke komanso tisakhale ndi mphamvu. (Miy. 24:10) Popeza ndife ochimwa, nthawi zina tingachite zinthu zimene sizingatithandize kukwaniritsa cholinga chathu. (Aroma 7:23) Kapenanso mwina tingamadzimve kuti tatopa. (Mat. 26:43) Ndiye n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi zolepheretsa? Tizikumbukira kuti tikakumana ndi zolepheretsa sizitanthauza kuti ndife olephera. Baibulo limanena kuti tingakumane ndi mavuto mobwerezabwereza. Komabe limafotokoza momveka bwino kuti tingathe kukwaniritsa cholinga chathu.. Mukamayesetsa kuti mukwaniritse zolinga zanu ngakhale pali zolepheretsa, mumamusonyeza Yehova kuti mukufuna kumamusangalatsa. Iye amasangalala akaona kuti mukupitirizabe kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chanu. w23.05 24:14-15
Loweruka, September 6
Muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.—1 Pet. 5:3.
Upainiya umathandiza wachinyamata kuti azitha kugwira bwino ntchito ndi anthu osiyanasiyana. Umathandizanso munthu kuti azipanga bajeti yabwino n’kumaitsatira. (Afil. 4:11-13) Upainiya wothandiza ndi poyambira pabwino kuti munthu achite utumiki wa nthawi zonse ndipo ungamuthandize kuti akonzekere kudzachita upainiya wokhazikika. Upainiya umapatsa munthu mwayi wochita mautumiki wosiyanasiyana a nthawi zonse, monga kugwira nawo ntchito zomangamanga kapena kutumikira pa Beteli. Amuna a Chikhristu ayenera kukhala ndi cholinga choti ayenerere kutumikira abale ndi alongo awo mumpingo ngati akulu. Baibulo limanena kuti amuna amene akuyesetsa kuti akhale ndi udindo umenewu “akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Choyamba, m’bale amafunika akhale kaye mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njira zambiri. Akulu ndi atumiki othandiza amatumikira abale ndi alongo awo modzichepetsa ndiponso amagwira nawo ntchito yolalikira mwakhama. w23.12 53:14-16
Lamlungu, September 7
Akadali mnyamata, Yosiya anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.—2 Mbiri 34:3.
Mfumu Yosiya anayamba kufunafuna Yehova ali wachinyamata. Ankafuna kuphunzira za Yehova n’kumachita chifuniro chake. Komabe zinthu sizinali zophweka kwa mfumu yachinyamatayi. Iye ankafunika kusankha kukhala kumbali ya kulambira koona pa nthawi imene anthu ambiri ankalambira milungu yabodza. Ndipo iye anachitadi zimenezo. Asanakwanitse zaka 20, Yosiya anayamba kuthetsa kulambira kwabodza. (2 Mbiri 34:1, 2) Ngakhale kuti ndinu wamng’ono mungathe kusankha kuti muzitsanzira Yosiya pofunafuna Yehova komanso kuphunzira makhalidwe ake. Kuchita zimenezi kudzakulimbikitsani kuti mudzipereke kwa iye. Kodi kudzipereka kumeneko kudzakhudza bwanji moyo wanu? Luke yemwe anabatizidwa ali ndi zaka 14 ananena kuti, “Kuyambira tsopano, ndiziika kutumikira Yehova pamalo oyamba ndipo ndiziyesetsa kuti ndizimusangalatsa.” (Maliko 12:30) Ngati inunso mutachita zimenezi Yehova adzakudalitsani. w23.09 38:12-13
Lolemba, September 8
Muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye komanso kukulangizani.—1 Ates. 5:12.
Pamene mtumwi Paulo ankalemba kalatayi, panali pasanathe chaka kuchokera pamene mpingo wa ku Tesalonika unakhazikitsidwa. Abale amene ankatsogolera, ayenera kuti anali asakudziwa zambiri komanso mwina ankalakwitsa zinthu zina. Komabe, iwo ankafunika kulemekezedwa. Kuposa kale lonse, pamene chisautso chachikulu chizidzayamba, tidzafunika kudalira kwambiri malangizo omwe akulu m’mipingo yathu angadzatipatse. Mwina pa nthawiyo sitingadzathe kulandira malangizo kuchokera kulikulu kapena ku ofesi ya nthambi, choncho n’zofunika kuphunzira kukonda komanso kulemekeza akulu panopa. Kaya zinthu zidzakhala bwanji, tiyeni tipitirize kukhala oganiza bwino, osamaganizira zimene iwo amalakwitsa koma tiziganizira mfundo yakuti Yehova kudzera mwa Khristu, akutsogolera amuna okhulupirikawa. Monga mmene chisoti chimatetezera mutu wa msilikali, chiyembekezo chathu chachipulumutso chimateteza maganizo athu. Timadziwa kuti zimene dzikoli limapereka, n’zachabechabe. (Afil. 3:8) Chiyembekezo chathu chimatithandiza kukhala odekha komanso osatekeseka. w23.06 26:11-12
Lachiwiri, September 9
Mkazi wopusa amakhala wolongolola. Iye ndi woperewera nzeru.—Miy. 9:13.
Amene amamva kuitana kwa “mkazi wopusa” amafunika kusankha, kaya kuvomera kupita kapena kukana. Pali zifukwa zomveka zotichititsa kupewa zachiwerewere. “Mkazi wopusa” akufotokozedwa ngati akunena kuti: “Madzi akuba amatsekemera.” (Miy. 9:17) Kodi “madzi akuba” akutchulidwawa ndi chiyani? Baibulo limayerekezera kugonana pakati pa anthu okwatirana ndi madzi otsitsimula. (Miy. 5:15-18) Mwamuna ndi mkazi okwatirana mwalamulo ndi amene amaloledwa kuti azigonana. Ndiye kodi zimenezi zikusiyana bwanji ndi “madzi akuba.” Madziwa ndi zachiwerewere zomwe n’zosaloleka. Nthawi zambiri zoterezi zimachitika mwachinsinsi, ngati mmene zimakhalira ndi wakuba. “Madzi akuba” angamaoneke ngati otsekemera makamaka ngati anthu ochita zachiwerewerewo akuona kuti sakukumana ndi vuto lililonse chifukwa cha zoipa zomwe akuchitazo. Kumenekutu n’kudzinamiza chifukwa Yehova amaona zonse. Palibe chinthu chowawa kwambiri kuposa kusiya kukondedwa ndi Yehova, ndipo sipakhala chilichonse “chotsekemera” kapena kuti chosangalatsa munthu akataya mwayi wamtengo wapataliwu.—1 Akor. 6:9, 10. w23.06 28:7-9
Lachitatu, September 10
Ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.—1 Akor. 9:17.
Kodi mungatani ngati mwayamba kuona kuti mapemphero anu si ochokeranso mumtima kapenanso simukusangalala ndi ntchito yolalikira ngati kale? Musamaganize kuti Yehova wasiya kukuthandizani ndi mzimu wake. Monga munthu yemwe si wangwiro, nthawi ndi nthawi mungamasinthe mmene mumamvera. Ngati mwayamba kuona kuti simukuchitanso khama muziganizira chitsanzo cha mtumwi Paulo. Ngakhale kuti ankayesetsa kutsanzira Yesu, ankadziwa kuti si nthawi zonse pomwe angachite zimene akulakalaka. Paulo anali wotsimikiza kukwaniritsa utumiki wake posatengera mmene akumvera. Mofanana ndi zimenezi, inunso musamalole kuti muzisankha zochita potengera mmene mukumvera. Muzitsimikiza kuchita zoyenera ngakhale kuti si zimene mungakonde kuchita. Mukamachita zoyenera nthawi zonse mungayambe kusintha mmene mumamvera.—1 Akor. 9:16. w24.03 10:12-13
Lachinayi, September 11
Asonyezeni kuti mumawakonda.—2 Akor. 8:24.
Tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu powalola kuti akhale anzathu. (2 Akor. 6:11-13) Ambirife tili m’mipingo imene muli abale ndi alongo omwe ndi osiyana pa zinthu zambiri komanso makhalidwe. Kuganizira makhalidwe awo abwino kungatithandize kuti tiziwakonda kwambiri. Tikamaphunzira kuona anthu mmene Yehova amawaonera, timasonyeza kuti timawakonda. Chikondi chidzakhala chofunika kwambiri pa chisautso chachikulu. Kodi n’kuti komwe tidzapeze chitetezo chisautsochi chikadzayamba? Taganizirani malangizo amene Yehova anapereka kwa anthu ake pamene Ababulo ankawaukira. Iye anati: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Zikuoneka kuti malangizo amenewa akugwiranso ntchito kwa ife amene tikuyembekezera chisautso chachikulu. w23.07 29:14-16
Lachisanu, September 12
Zochitika zapadzikoli zikusintha.—1 Akor. 7:31.
Muzidziwika ndi mbiri yoti ndinu ololera. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndine wololera kapena amandiona kuti ndine wokhwimitsa zinthu, wovuta kapena womva zake zokha? Kodi ndimamvetsera maganizo a ena komanso kuchita zimene akufuna ngati zili zoyenera kutero?’ Zimene timachita pa nkhani ya kulolera zingasonyeze ngati timatsanzira kwambiri Yehova ndi Yesu kapena ayi. Kulolera kumaphatikizapo kukhala okonzeka kusintha zinthu zikasintha pa moyo wathu. Nthawi zina kusintha kungachititse kuti tikumane ndi mavuto osayembekezereka. Mwadzidzidzi, tingakumane ndi mavuto okhudza thanzi lathu. Mwinanso kusintha pa nkhani zachuma kapena zandale kungasokoneze kwambiri moyo wathu. (Mlal. 9:11) Chikhulupiriro chathu chingayesedwenso pamene utumiki wathu wasintha. Komabe tikhoza kuzolowera kusintha komwe kwachitika ngati titachita zinthu 4 zotsatirazi: (1) kuvomereza mmene zinthu zilili, (2) kuganizira zam’tsogolo, (3) kuganizira zabwino zimene zikuchitika komanso (4) kuthandiza ena. w23.07 32:7-8
Loweruka, September 13
Ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.—Dan. 9:23.
Mneneri Danieli anali wachinyamata pamene Ababulo anamugwira monga kapolo n’kupita naye kudziko lakutali ndi kwawo. Anthuwo ayenera kuti anachita naye chidwi. Iwo anaona “zooneka ndi maso,” monga zakuti Danieli “analibe chilema chilichonse” ndiponso ankachokera m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulo anamuphunzitsa kuti azikatumikira kunyumba yachifumu. (Dan. 1:3, 4, 6) Yehova ankakonda Danieli chifukwa cha zimene mnyamatayu anasankha kuti azichita pa moyo wake. Ndipotu n’kutheka kuti iye anali ndi zaka pafupifupi 20 zokha, pamene Yehova anamutchula pamodzi ndi Nowa komanso Yobu, amuna amene anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; Ezek. 14:14) Danieli anakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali ndipo Yehova anapitiriza kumukonda kwa moyo wake wonse munthu wokhulupirikayu.—Dan. 10:11, 19. w23.08 33:1-2
Lamlungu, September 14
[Muzitha] kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwera ndi kuzama kwa choonadi.—Aef. 3:18.
Mukafuna kugula nyumba mungafune kudziwa kalikonse kokhudza nyumbayo. Tingachitenso zofanana ndi zimenezi pamene tikuwerenga komanso kuphunzira Baibulo. Ngati mutaliwerenga mofulumira, mukhoza kungodziwa “mfundo zoyambirira za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) Koma mofanana ndi zimene mungachite ndi nyumba ija, muyenera kulowa “mkati” kapena kuti kuliphunzira mosamala kuti mulimvetse. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo ndi kuona mmene mbali zosiyanasiyana za uthenga wake zilili zogwirizana. Muziyesetsa kuti mumvetse, osati mfundo za choonadi zomwe mumakhulupirira zokha, koma chifukwa chakenso mumazikhulupirira. Kuti tizimvetsa bwino Mawu a Mulungu, tiyenera kumaphunzira mosamala mfundo zozama za choonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa abale ndi alongo ake kuti aziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama n’cholinga choti ‘adziwe bwino mulifupi ndi mulitali ndi kukwera ndi kuzama’ kwa choonadi. Iwo akanachita zimenezi, ‘akanazika mizu ndi kukhala okhazikika’ m’chikhulupiriro chawo. (Aef. 3:14-19) Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. w23.10 44:1-3
Lolemba, September 15
Abale, pa nkhani ya kumva zowawa ndi kuleza mtima, tengerani chitsanzo cha aneneri amene analankhula m’dzina la Yehova.—Yak. 5:10.
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Bwanji osakonza zoti mufufuze zitsanzozi pamene mukuphunzira Baibulo panokha? Mwachitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa ali mwana kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli, anafunika kudikira kwa zaka zambiri asanapatsidwe ufumuwo. Simiyoni ndi Anna ankatumikira Yehova mokhulupirika pamene ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaphunzira nkhanizi muzifufuza mayankho a mafunso awa: Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza munthuyu kuti akhale woleza mtima? Kodi kukhala woleza mtima kunamuthandiza bwanji? Kodi ndingamutsanzire bwanji? Mungapindulenso ngati mutaphunzira za anthu omwe sanasonyeze kuleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘Kodi mwina n’chiyani chinachititsa kuti asakhale woleza mtima? Nanga zotsatirapo zake zinali zotani?’ w23.08 35:15
Lachiwiri, September 16
Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera amene Mulungu anamutumiza.—Yoh. 6:69.
Mtumwi Petulo anali wokhulupirika ndipo sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kutsatira Yesu. Iye anasonyeza kukhulupirika kwake pa nthawi ina pamene Yesu analankhula zinthu zimene ophunzira ake sanazimvetse. (Yoh. 6:68) Anthu ambiri anasiya kutsatira Yesu popanda kudikira kuti awafotokozere zimene ankatanthauza. Koma Petulo ankadziwa kuti Yesu yekha, ndi yemwe ali ndi “mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.” Yesu ankadziwa kuti Petulo ndi atumwi ena amusiya yekha. Komabe sankakayikira kuti Petulo adzabwerera n’kukhalabe wokhulupirika. (Luka 22:31, 32) Yesu ankadziwa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38). Choncho ngakhale kuti Petulo anamukana kuti sakumudziwa, iye sanasiye kukonda mtumwi wakeyu. Ataukitsidwa, Yesu anakumana ndi Petulo ndipo zikuoneka kuti Petuloyo anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa mtumwiyu, yemwe ankadzimvera chisoni kwambiri. w23.09 40:9-10
Lachitatu, September 17
Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.—Aroma 4:7.
Mulungu amakhululuka kapena kuphimba machimo a anthu omwe amamukhulupirira. Iye amawakhululukira kotheratu moti sawerengeranso machimo awo. (Sal. 32:1, 2) Amawaona kuti ndi opanda cholakwa komanso olungama chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti Abulahamu, Davide ndi atumiki ena okhulupirika ankaonedwa kuti ndi olungama, iwo anali adakali ochimwa. Koma chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Mulungu ankawaona kuti ndi opanda cholakwa poyerekezera ndi anthu omwe sankamutumikira. (Aef. 2:12) Mtumwi Paulo anafotokoza bwino m’kalata yake zoti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Ndi mmenenso zinalili ndi Abulahamu ndi Davide. Choncho ifenso chikhulupiriro chingatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. w23.12 50:6-7
Lachinayi, September 18
Nthawi zonse tizitamanda Mulungu. . . . Kuchita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupereka kwa Mulungu ndipo timagwiritsa ntchito milomo yathu polengeza dzina lake.—Aheb. 13:15.
Masiku ano Akhristu onse ali ndi mwayi wopereka nsembe kwa Yehova pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso zinthu zawo pomutumikira. Tingasonyeze kuti timayamikira mwayi wathu wolambira Yehova poyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Mtumwi Paulo anatchula zinthu zosiyanasiyana zokhudza kulambira kwathu zimene sitiyenera kuzinyalanyaza. (Aheb. 10:22-25) Zinthu zake zikuphatikizapo kupemphera kwa Yehova, kulengeza poyera chiyembekezo chathu, kusonkhana pamodzi ngati mpingo ndiponso kulimbikitsana, ‘makamaka panopa pamene tikuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikira.’ Pofuna kutsindika, chakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova ananena kawiri kuti: “Lambira Mulungu.” (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse mfundo zozama za choonadi zokhudza kachisi wamkulu wauzimu ndipo tiziyamikira mwayi wolambira Mulungu wathu wamkulu, Yehova. w23.10 45:17-18
Lachisanu, September 19
Tiyeni tipitirize kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Tonsefe tiyenera ‘kupitiriza kukondana.’ Koma tiyenera kukumbukira kuti Yesu anachenjeza kuti “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mat. 24:12) Yesu sankatanthauza kuti chikondi cha ophunzira ake ambiri chidzachepa. Ngakhale zili choncho, tiyenera kukhala osamala kuti tisatengere mtima wopanda chikondi womwe ndi wofala m’dzikoli. Poganizira mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane funso lina lofunika. Kodi pali njira yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu? Njira imodzi yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu ndi kuona zimene timachita pa moyo wathu. (2 Akor. 8:8) Mtumwi Petulo anatchula chimodzi mwa zinthuzi pomwe anati: “Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Choncho zimene timachita abale athu akalakwitsa zinthu, zingasonyeze ngati timawakonda kwambiri kapena ayi. w23.11 47:12-13
Loweruka, September 20
Muzikondana.—Yoh. 13:34.
Sitingamvere lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mumpingo n’kumalephera kukonda ena. N’zoona kuti tingamagwirizane kwambiri ndi ena kuposa ena, ngati mmenenso Yesu ankachitira. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma mtumwi Petulo akutikumbutsa kuti tiyenera kuyesetsa kuti ‘tizikonda abale’ onse ngati anthu a m’banja lathu. (1 Pet. 2:17) Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikondana kwambiri kuchokera mumtima.’ (1 Pet. 1:22) Apa mawu akuti ‘kukondana kwambiri’ akutanthauza kukonda winawake ngakhale pamene zili zovuta kutero. Mwachitsanzo, bwanji ngati m’bale watikhumudwitsa m’njira inayake? Mwachibadwa timafuna kumubwezera osati kumusonyeza chikondi. Komatu Petulo anaphunzira kwa Yesu kuti kubwezera sikusangalatsa Mulungu. (Yoh. 18:10, 11) Iye analemba kuti: “Munthu akakuchitirani choipa musamabwezere ndi choipa, akakuchitirani chipongwe musamabwezere ndi chipongwe. M’malomwake muziwachitira zabwino.” (1 Pet. 3:9) Muzilola kuti kukonda kwambiri ena, kuzikulimbikitsani kuti muzikomera mtima komanso kuganizira ena. w23.09 41:9-11
Lamlungu, September 21
Nawonso akazi akhale . . . ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse.—1 Tim. 3:11.
Timadabwa kuona mmene mwana amakulira mofulumira kwambiri n’kukhala munthu wamkulu. Zimaoneka kuti kukula kumeneku kumangochitika pakokha. Koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti munthu akule mwauzimu amafunika kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timafunikanso mzimu woyera kuti utithandize kukhala ndi makhalidwe abwino, kukhala ndi luso lochitira zinthu bwino komanso kukonzekera maudindo athu am’tsogolo. (Miy. 1:5) Polenga anthu, Yehova anawalenga mwamuna ndi mkazi. (Gen. 1:27) Mwamuna ndi mkazi amaoneka mosiyana komanso amakhala osiyana m’njira zina. Mwachitsanzo, Yehova analenga amuna ndi akazi kuti azikwaniritsa maudindo osiyana. Choncho iwo amafunika kukhala ndi makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwaniritsa bwino maudindo awowo.—Gen. 2:18. w23.12 52:1-2
Lolemba, September 22
Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza mʼdzina la Atate, [ndi] la Mwana.—Mat. 28:19.
Kodi Yesu amafuna kuti enanso azigwiritsa ntchito dzina lenileni la Atate wake? Inde. Atsogoleri ena achipembedzo pa nthawiyo, ankakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi lopatulika kwambiri ndipo si ulemu kumalitchula. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosagwirizana ndi Malembayi imulepheretse kulemekeza dzina la Atate wake. Taganizirani zimene zinachitika atachiritsa munthu wina wogwidwa ndi ziwanda, m’dera la Agerasa. Anthu akumeneko anachita mantha ndipo anapempha Yesu kuti achoke m’deralo, ndipo anachokadi. (Maliko 5:16, 17) Komabe, Yesu ankafuna kuti anthu akumeneko adziwe dzina la Yehova. Choncho analamula munthu amene anamuchiritsayo kuti aziuza anthu, osati zimene Yesu anamuchitira, koma zimene Yehova anamuchitira. (Maliko 5:19) Masiku anonso, iye amafuna kuti tizidziwitsa anthu padziko lonse dzina la Atate wake. (Mat. 24:14; 28:20) Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu. w24.02 6:10
Lachiwiri, September 23
Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa.—Chiv. 2:3.
Ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu la Yehova masiku otsiriza ovutawa. Pamene zinthu zikuipiraipira m’dzikoli, Yehova watipatsa banja lauzimu logwirizana la abale ndi alongo. (Sal. 133:1) Amatithandizanso kuti tizikhala ndi mabanja olimba. (Aef. 5:33–6:1) Komanso amatipatsa nzeru kuti tizikhala ndi mtendere wa mumtima. Koma tiyenera kuchita khama kuti tipitirizebe kutumikira Yehova mokhulupirika. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa nthawi zina tikhoza kukhumudwa ndi zinthu zimene ena alakwitsa. Tikhozanso kumakhumudwa ngati timalakwitsa zinthu zinazake mobwerezabwereza. Tiyenera kupitiriza kutumikira Yehova ngakhale (1) Mkhristu mnzathu akatilakwira, (2) mwamuna kapena mkazi wathu akatikhumudwitsa, ndiponso (3) tikakhumudwa ndi zimene timalakwitsa. w24.03 11:1-2
Lachitatu, September 24
Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.—Afil. 3:16.
Nthawi zambiri muzimva zimene zachitikira abale ndi alongo anu omwe ayesetsa kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Mwina iwo analowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu kapenanso anasamukira kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Inunso mungathe kudziikira zolinga ngati zimenezi. Anthu a Yehova amafunitsitsa kuti azichita zambiri pomutumikira. (Mac. 16:9) Koma bwanji ngati inuyo simungakwanitse kuchita zimenezi panopa? Musamaganize kuti ndinu olephera poyerekezera ndi amene akwanitsa kuchita zimenezo. Chofunika kwambiri n’chakuti mukupitirizabe kutumikira Mulungu. (Mat. 10:22) Musamayiwale kuti Yehova amasangalala ndi zimene mumachita pomutumikira mogwirizana ndi luso lanu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Imeneyi ndi njira yofunika kwambiri yomwe mungapitirizire kutsatira Yesu pambuyo pobatizidwa.—Sal. 26:1. w24.03 10:11
Lachinayi, September 25
Mokoma mtima anatikhululukira machimo athu onse.—Akol. 2:13.
Atate wathu wakumwamba amatilonjeza kuti azitikhululukira tikalapa. (Sal. 86:5) Choncho tikamadzimvera chisoni chifukwa cha machimo amene tinachita tisamakayikire zimene Yehova wanena kuti watikhululukira. Tizikumbukira kuti Yehova amatimvetsa ndipo ndi wololera. Iye samayembekezera kuti tichita zimene sitingakwanitse. Ndipo amayamikira zilizonse zimene timayesetsa kuchita. Komanso muziganizira zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anatumikira Yehova ndi mtima wawo wonse. Mwachitsanzo, taganizirani za mtumwi Paulo. Iye anagwira ntchito mwakhama kwa zaka zambiri, kuyenda maulendo ataliatali komanso kuyambitsa mipingo yambiri. Koma pamene zinthu zinasintha pa moyo wake n’kumalephera kuchita zambiri pa ntchito yolalikira, kodi Mulungu sankasangalala naye? Ayi. Iye anapitiriza kuchita zimene akanakwanitsa ndipo Mulungu anamudalitsa. (Mac. 28:30, 31) Mofanana ndi zimenezi, nthawi zina zimene timachita potumikira Yehova zikhoza kusintha. Koma chofunika kwambiri kwa iye ndi cholinga chimene tikuchitira zinthuzo. w24.03 13:7, 9
Lachisanu, September 26
M’mawa kwambiri, . . . Yesu anadzuka n’kutuluka panja ndipo anapita kumalo kopanda anthu. Kumeneko anayamba kupemphera.—Maliko 1:35.
Kudzera m’mapemphero ake kwa Yehova, Yesu anapereka chitsanzo choti otsatira ake azitengera. Pa nthawi yonse ya utumiki wake, Yesu ankapemphera pafupipafupi. Iye ankafunika kukonza nthawi yoti apemphere chifukwa nthawi zambiri ankakhala wotanganidwa komanso ankazunguliridwa ndi anthu ambiri. (Maliko 6:31, 45, 46) Ankadzuka m’mawa kwambiri kuti akakhale payekha n’kupemphera. Pa nthawi ina anapemphera usiku wonse asanasankhe zochita pa nkhani yofunika kwambiri. (Luka 6:12, 13) Ndipo pa usiku wake womaliza, iye anapemphera mobwerezabwereza poganizira mbali yomaliza ya utumiki wake padzikoli, yomwe inali yovuta kwambiri. (Mat. 26:39, 42, 44.) Chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa kuti kaya timatanganidwa bwanji, timafunika kupeza nthawi yopemphera. Mofanana ndi Yesu, mwina ifenso tingafunike kudzuka m’mawa kwambiri kapena kugona mochedwa kuti tipeze nthawi yopemphera. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti timayamikira Yehova potipatsa mphatso yapaderayi. w23.05 20:4-5
Loweruka, September 27
Mulungu amasonyeza kuti amatikonda pogwiritsa ntchito mzimu woyera umene amatipatsa.—Aroma 5:5.
Palembali, mawu amene anamasuliridwa kuti “amasonyeza kuti amatikonda” angamasuliridwenso kuti “amatikhuthulira chikondi chake.” Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti chikondichi chimabwera ngati mtsinje. Mawu amenewa ndi amphamvu ndipo amasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri odzozedwa. Odzozedwa amadziwa kuti “[Mulungu] amawakonda.” (Yuda 1) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene iwo amamvera polemba kuti: “Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza potitchula kuti ana ake.” (1 Yoh. 3:1) Kodi Yehova amakonda odzozedwa okha? Ayi, iye amatikonda tonsefe. Kodi njira yaikulu kwambiri imene Yehova wasonyezera kuti amatikonda ndi iti? Dipo ndi njira yaikulu kwambiri imene wasonyezera chikondi kuposa wina aliyense.—Yoh. 3:16; Aroma 5:8. w24.01 4:9-10
Lamlungu, September 28
Pa tsiku limene ndidzapemphe kuti mundithandize, adani anga adzathawa. Mulungu ali kumbali yanga. Sindikukaikira zimenezi.—Sal. 56:9.
Lembali likufotokoza chinthu chomwe chinathandiza Davide kuti asamachite mantha. Chinthu chake n’chakuti, ngakhale kuti moyo wake unali pangozi, iye ankaganizira zimene Yehova adzamuchitire m’tsogolo. Davide ankadziwa kuti Yehova adzamupulumutsa pa nthawi yoyenera. Ndipotu iye anali atanena kale kuti Davideyo ndi amene adzakhale mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 16:1, 13) Kwa Davide, zinali ngati chilichonse chomwe Yehova analonjeza chinali chitachitika kale. Kodi Yehova walonjeza kuti adzakuchitirani chiyani inuyo? Sitimayembekezera kuti azititeteza ku mavuto onse. Komabe kaya tikukumana ndi mayesero otani m’dziko loipali, tizikumbukira kuti Yehova adzawathetsa m’dziko latsopano. (Yes. 25:7-9) Mlengi wathu ndi wamphamvu kwambiri moti adzaukitsa akufa, kutichiritsa komanso adzaononga otsutsa onse.—1 Yoh. 4:4. w24.01 1:12-13
Lolemba, September 29
Wosangalala ndi munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake akhululukidwa.—Sal. 32:1.
Muziganizira chifukwa chake munadzipereka komanso kubatizidwa. Munachita zimenezi chifukwa chofuna kukhala ku mbali ya Yehova. Muzikumbukira chimene chinakutsimikizirani kuti munapeza choonadi. Munaphunzira mfundo zoona zokhudza Yehova ndipo munayamba kumukonda komanso kumulemekeza kwambiri monga Atate wanu wakumwamba. Munakhala ndi chikhulupiriro ndipo izi zinakuthandizani kuti mulape. Mtima wanu unakulimbikitsani kuti musiye makhalidwe oipa komanso kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Munamva bwino mutadziwa kuti Mulungu anakukhululukirani. (Sal. 32:2) Munayamba kupezeka pamisonkhano komanso kuuza ena zinthu zochititsa chidwi zimene munkaphunzira. Monga Mkhristu wodzipereka komanso wobatizidwa, panopa mukuyenda pamsewu wopita kumoyo ndipo ndinu wotsimikiza kuti mupitiriza kuyenda pamsewu umenewu. (Mat. 7:13, 14) Tiyeni tikhale olimba, osasunthika polambira Yehova ndipo tisamasiye kumvera malamulo ake. w23.07 31:14, 19
Lachiwiri, September 30
Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.—1 Akor. 10:13.
Kuganizira zimene munalonjeza Yehova podzipereka kungakupatseni mphamvu kuti muthe kukana mayesero alionse. Mwachitsanzo, kodi mungayambe kukopana ndi mwamuna kapena mkazi wamwini wake? Ayi simungatero, chifukwa munalonjeza kale Yehova kuti simungachite zinthu ngati zimenezo. Ngati simungalole kuti maganizo oipa akhazikike mumtima mwanu, pambuyo pake simudzavutika ndi kulimbana nawo kuti muwathetse. ‘Mudzapatuka’ kuti ‘musatengere zochita za anthu oipa.’ (Miy. 4:14, 15) Kuganizira mmene Yesu analili wotsimikiza kuti azisangalatsa Atate wake, kudzakuthandizani kuti mwamsanga komanso molimba mtima mukane zilizonse zomwe mukudziwa kuti sizingasangalatse Mulungu, yemwe munadzipereka kwa iye. (Mat. 4:10; Yoh. 8:29) Mayesero amene mumakumana nawo amakupatsani mwayi woti musonyeze kuti ndinu ofunitsitsa ‘kupitiriza kutsatira’ Yesu. Ndipo mukamachita zimenezi, mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakuthandizani. w24.03 10:8-10