NYIMBO 135
Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”
zosindikizidwa
	- 1. Mwana wanga undipatse - mtima wako. - Yemwe akunditonza - aone yekha. - Ukudziperekadi - mofunitsitsa; - Anthu adziwe - kuti umandikonda. - (KOLASI) - Mwana wanga wokondedwawe, - Khalatu wanzeru chonde. - Kutitu unditumikire, - Inde mwakufuna kwako. 
- 2. Uzinditumikira - mosangalala, - Ngakhale ukapunthwa, - ndidzakudzutsa. - Wina ngakhale - angakukhumudwitse, - Usadere nkhawa - ndidzakhala nawe. - (KOLASI) - Mwana wanga wokondedwawe, - Khalatu wanzeru chonde. - Kutitu unditumikire, - Inde mwakufuna kwako. 
(Onaninso Deut. 6:5; Mlal. 11:9; Yes. 41:13.)