NYIMBO 138
Imvi Ndi Chisoti cha Ulemerero
zosindikizidwa
1. Pano tili ndi anthu
Achikulire.
Akukondabe M’lungu;
Sanamusiye.
Enatu umasiye
Ukuwawawa
Tate, atonthozeni,
Alimbitseni.
(KOLASI)
Mumakumbukira
Zochita zawo.
Tate auzeni:
“Mwachita bwino!”
2. Imvi za olungama
Ndi zokongola.
Zimasangalatsadi
Tate Yehova.
Ife tikumbukire
Pa nthawi ina.
Pa unyamata wawo
Ankayesetsa.
(KOLASI)
Mumakumbukira
Zochita zawo.
Tate auzeni:
“Mwachita bwino!”
(Onaninso Sal. 71:9, 18; Miy. 20:29; Mat. 25:21, 23; Luka 22:28; 1 Tim. 5:1.)