NYIMBO 2
Dzina Lanu Ndinu Yehova
zosindikizidwa
	- 1. Mulungu woona— - Mlengi wa zinthu zonse - Mulungu wamuyaya— - Ndinudi Yehova. - Ndifetu amwayi - Kukhala anthu anu. - Tilengeza za inu, - Ku mitundu yonse. - (KOLASI) - Yehova, Yehova, - M’lungu ndinu nokha. - Kumwambako ndi padziko - Palibenso wina. - Ndinudi Wamphamvuyonse - Onsetu adziwe. - Yehova, Yehova, - M’lungu wathu ndinu nokha. 
- 2. Tingathe kukhala - Chilichonse mwafuna. - Tigwire ntchito yanu— - Ndinudi Yehova. - Mwatipatsa dzina - Tikhale Mboni zanu. - Uwu ndi mwayi wathu— - Tikutamandani. - (KOLASI) - Yehova, Yehova, - M’lungu ndinu nokha. - Kumwambako ndi padziko - Palibenso wina. - Ndinudi Wamphamvuyonse - Onsetu adziwe. - Yehova, Yehova, - M’lungu wathu ndinu nokha. 
(Onaninso 2 Mbiri 6:14; Sal. 72:19; Yes. 42:8.)