Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 140
  • Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Zimene Tiyenera Kuchita Kuti Tipulumuke
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Ndiwo Okha Amene Adzapulumuke?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Tiyenera Kuchitanji Kuti Tipulumutsidwe?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Munthu Amene Analandira Khristu Ndiye Kuti Basi Sangawonongedwe?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 140
Yesu wazunguliridwa ndi anthu a mitundu yosiyanasiyana

Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?

Yankho la m’Baibulo

Yesu atapereka moyo wake ngati nsembe ya dipo, anathandiza kuti anthu okhulupirika apulumuke. (Mateyu 20:28) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Mpulumutsi wa dziko.” (1 Yohane 4:14) Limanenanso kuti: “Chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”—Machitidwe 4:12.

Yesu ‘analawa imfa m’malo mwa munthu aliyense’ amene angasonyeze chikhulupiriro mwa iye. (Aheberi 2:9; Yohane 3:16) Kenako “Mulungu anamuukitsa kwa akufa” ndipo anabwerera kumwamba komwe anakakhalanso ndi moyo wauzimu. (Machitidwe 3:15) Panopo Yesu amatha “kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.”—Aheberi 7:25.

N’chifukwa chiyani Yesu amafunika kuchonderera m’malo mwathu?

Anthu tonse ndife ochimwa. (Aroma 3:23) Uchimo uli ngati chotchinga pakati pa anthufe ndi Mulungu ndipo timafa chifukwa chakuti ndife ochimwa. (Aroma 6:23) Koma Yesu ndi “mthandizi” wa onse amene amakhulupirira nsembe ya dipo yomwe anapereka. (1 Yohane 2:1) Yesu amathandiza anthu powachonderera kwa Mulungu kuti amve mapemphero awo. Ndipo Mulungu amakhululukira anthuwo chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Mateyu 1:21; Aroma 8:34) Yesu akamachonderera, Mulungu amamva chifukwa amaona kuti zopemphazo ndi zogwirizana ndi chifuniro chake. Mulungu anatumiza mwana wake padzikoli “kuti mwa iye, dziko lipulumutsidwe.”—Yohane 3:17.

Kodi kungokhulupirira Yesu n’kokwanira kuti tidzapulumuke?

Ayi. Pali zambiri zomwe zimafunika kuti tidzapulumuke osati kungokhulupirira Yesu kokha. (Machitidwe 16:30, 31) Baibulo limati: “Monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa, nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yakobo 2:26) Kuti tidzapulumuke tiyenera:

  • Kuphunzira za Yesu ndi Atate wake yemwe ndi Yehova.​—Yohane 17:3.

  • Kusonyeza kuti timakhulupirira Yesu komanso Yehova ​—Yohane 12:44; 14:1

  • Kusonyeza chikhulupiriro chathu pomvera malamulo omwe amatipatsa. (Luka 6:46; 1 Yohane 2:17) Yesu anaphunzitsa kuti si aliyense amene adzamutchule kuti “Ambuye” amene adzapulumuke. Koma okhawo amene “akuchita chifuniro cha Atate [wake] wakumwamba.”—Mateyu 7:21.

  • Kupitiriza kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro ngakhale kuti timakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Yesu anasonyeza kuti zimenezi ndi zofunika kwambiri pamene ananena kuti: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.”—Mateyu 24:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena