Yobu
3 Amakuchititsa kumveka pansi ponse pa thambo,
Ndipo mphezi yake+ imafika kumalekezero a dziko lapansi.
4 Pambuyo pake pamamveka phokoso.
Iye amabangula+ ndi mawu ake amphamvu.+
Mawu ake akamveka, iye saletsa mphezizo.+
5 Mulungu amabangula ndi mawu ake+ mochititsa chidwi kwambiri.
Amachita zinthu zazikulu zimene sitingazidziwe.+
6 Chifukwa chipale chofewa amachiuza kuti, ‘Gwera padziko lapansi.’+
Amauzanso mvula zimenezi, ngakhalenso mvula yamphamvu ikamakhuthuka.+
7 Iye amatseka dzanja la munthu aliyense,
Kuti anthu onse adziwe ntchito ya Mulungu.
11 Iye amalemetsa mitambo ndi chinyontho.
Kuwala kwake+ kumamwaza mitambo younjikana pamodzi.
12 Amaizunguliza ndi kuiwongolera kuti igwire ntchito yake
Kulikonse kumene amailamula+ panthaka ya padziko lapansi.
13 Amagwiritsa ntchito mitamboyo kuti ipereke chilango,+ kuti inyowetse dziko lake,+
Komanso kuti iye asonyeze kukoma mtima kwake kosatha.+
15 Kodi mukudziwa nthawi imene Mulungu anapangana nazo,+
Komanso pamene anachititsa kuunika kwa mtambo wake kuti kuwale?
16 Kodi mukudziwa mmene mtambo umaimira,+
Ndiponso ntchito zodabwitsa za yemwe amadziwa zinthu bwino kwambiri?+
18 Kodi limodzi ndi iyeyo mungagangate* kuthambo,+
Komwe kuli ngati galasi lolimba lopangidwa ndi chitsulo chosungunula?
19 Tidziwitseni zoti timuuze.
Sitingathe kutulutsa mawu chifukwa cha mdima.