Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe motsatira Mbawala Yaikazi ya M’bandakucha. Nyimbo ya Davide.
22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+
N’chifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?+
N’chifukwa chiyani simukumva mawu a kubuula kwanga?+
2 Inu Mulungu wanga, ine ndimaitana usana koma simundiyankha.+
Usiku ndimaitanabe, moti sindikukhala chete.+
5 Iwo anali kufuulira inu,+ ndipo anali kupulumuka.+
Anali kudalira inu, ndipo simunawachititse manyazi.+
7 Anthu onse ondiona amandinyodola.+
Iwo amandinyogodola ndi pakamwa pawo, ndipo amapukusa mitu yawo mondinyoza.+ Iwo amati:
9 Pakuti ndinu amene munanditulutsa m’mimba,+
Amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinali kuyamwa mabere a mayi anga.+
10 Ndinaponyedwa m’manja mwanu kuchokera m’mimba.+
Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.+
11 Musakhale kutali ndi ine, chifukwa zondisautsa zili pafupi,+
Ndiponso chifukwa ndilibe mthandizi winanso.+
12 Ng’ombe zazing’ono zamphongo zochuluka zandizungulira.+
Nkhunzi zamphamvu za ku Basana zandizinga.+
14 Ndathiridwa pansi ngati madzi.+
Mafupa anga onse alekanalekana.+
Mtima wanga wakhala ngati phula,+
Wasungunuka mkati mwanga.+
15 Mphamvu yanga yauma gwaa, ngati phale.+
Lilime langa lamamatira kunkhama zanga,+
Ndipo mwandikhazika m’fumbi la imfa.+
20 Landitsani moyo wanga ku lupanga,+
Moyo wanga wokhawu umene ndili nawo muulanditse m’kamwa mwa galu.+
21 Ndipulumutseni m’kamwa mwa mkango,+
Ndipo mundiyankhe ndi kundipulumutsa ku nyanga za ng’ombe zamphongo zam’tchire.+
23 Inu oopa Yehova, m’tamandeni!+
Inu nonse mbewu ya Yakobo, m’patseni ulemerero!+
Ndipo muopeni, inu nonse mbewu ya Isiraeli.+
Kapena kunyansidwa ndi nsautso ya munthu wosautsidwa.+
Ndipo sanam’bisire nkhope yake.+
Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+
25 Chifukwa cha zimene mwachita ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+
Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu oopa iye.+
26 Ofatsa adzadya ndi kukhuta.+
Ofunafuna Yehova adzamutamanda.+
Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.+
27 Anthu onse okhala kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kubwerera kwa iye.+
Ndipo mafuko onse a anthu a mitundu ina adzagwada pamaso panu.+