Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa “Nkhunda Yosanena Kanthu” pakati pa okhala kutali. Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Afilisiti anamugwira ku Gati.+
56 Ndikomereni mtima inu Mulungu wanga, chifukwa munthu wopanda pake akufuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+
Akulimbana nane tsiku lonse ndi kundipondereza.+
2 Tsiku lonse adani anga akufuna kundiwakha ndi pakamwa pawo,+
Pakuti anthu ambiri akumenyana nane modzikuza.+
3 Ine ndidzadalira inu, tsiku lililonse limene ndingachite mantha.+
4 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu, ndidzatamanda mawu ake.+
Ine ndimadalira Mulungu, sindidzaopa.+
Kodi munthu angandichite chiyani?+
6 Amandiukira ndi kundibisalira,+
Iwo nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+
Pamene akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+
8 Inu mwalemba za kuthawathawa kwanga.+
Sungani misozi yanga m’thumba lanu lachikopa.+
Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?+
9 Pa nthawi imeneyo adani anga adzabwerera pa tsiku limene ndidzaitana inu.+
Ndikudziwa bwino kuti Mulungu ali kumbali yanga.+
10 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu,+ ndidzatamanda mawu ake.
Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Yehova, ndidzatamanda mawu ake.+