Masalimo
74 Inu Mulungu, n’chifukwa chiyani mwatitaya?+
N’chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukuyakira nkhosa zimene mukuweta?+
2 Kumbukirani anthu amene munawatenga kukhala anu kalelo,+
Fuko limene munaliwombola monga cholowa chanu,+
Ndi phiri la Ziyoni ili mmene inu mukukhala.+
4 Anthu amene akukuchitirani zoipa afuula mosangalala kuti apambana m’malo anu olambiriramo.+
Aikamo mbendera zawo monga zizindikiro.+
5 Iwo amatchuka ngati munthu amene amagwetsa mitengo ndi nkhwangwa m’nkhalango.
6 Ndipo tsopano zojambula mochita kugoba za m’makoma a malo opatulika, onse amazichotsa ndi nkhwangwa komanso ndodo zokhala ndi chitsulo kumutu kwake.+
8 Iwo, ngakhalenso ana awo, onse pamodzi anena mumtima mwawo kuti:
“Malo onse olambiriramo a Mulungu ayenera kutenthedwa m’dzikoli.”+
9 Zizindikiro zathu sitinazione, ndipo palibenso mneneri amene watsala,+
Pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zikhala choncho mpaka liti.
10 Inu Mulungu, kodi mdani adzakuchitirani mopanda ulemu kufikira liti?+
Kodi mdani adzanyoza dzina lanu kwamuyaya?+
11 N’chifukwa chiyani mwachotsa dzanja lanu, dzanja lanu lamanja,+
Pachifuwa panu koma osachitapo kanthu? Kodi mukatero ife sitiwonongedwa?
12 Koma Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale,+
Iye ndiye wondipatsa chipulumutso chachikulu padziko lapansi.+
14 Inu munaphwanya mitu ya Leviyatani*+ kukhala zidutswazidutswa.
Munaipereka kwa anthu monga chakudya, munaipereka kwa anthu okhala m’madera opanda madzi.+
15 Ndinu amene munang’amba nthaka ndi kupanga akasupe ndi makwawa.+
Inu munaumitsa mitsinje imene inali kukhala ndi madzi nthawi zonse.+
17 Ndinu amene munaika malire onse a dziko lapansi.+
Munapanga nyengo yachilimwe ndi nyengo yachisanu.+
18 Kumbukirani izi: Inu Yehova, mdani wakuchitirani mopanda ulemu,+
Ndipo anthu opusa anyoza dzina lanu.+
19 Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo chakuthengo.+
Musaiwale kwamuyaya moyo wa anthu anu osautsika.+
20 Kumbukirani pangano limene munachita nafe,+
Pakuti malo a mdima a dziko lapansi adzaza ndi chiwawa.+
21 Musalole kuti munthu woponderezedwa achite manyazi.+
Munthu wosautsika ndi wosauka atamande dzina lanu.+