Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
5 Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo.+
Iwo agona tulo,
Asilikali onse analibe mphamvu.+
6 Chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo,
Hatchi komanso wokwera galeta, onse agona tulo tofa nato.+
7 Inu nokha ndinu wochititsa mantha.+
Ndi ndani angapirire mkwiyo wanu waukulu?+
8 Munapereka chiweruzo muli kumwamba.+
Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala chete+
9 Pamene Mulungu ananyamuka kuti apereke chiweruzo,
Kuti apulumutse anthu onse ofatsa apadziko lapansi.+ (Selah)
10 Chifukwa mkwiyo wa munthu udzachititsa kuti mutamandidwe.+
Mudzadzikongoletsa ndi mkwiyo wawo wotsala.
11 Chitani malonjezo anu kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse+
Anthu onse amene amuzungulira abweretse mphatso zawo mwamantha.+
12 Mulungu adzachititsa manyazi atsogoleri onyada.
Iye amachititsa kuti mafumu apadziko lapansi akhale ndi mantha.