Yoswa
20 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako+ imene ndinakuuzani kudzera mwa Mose, 3 kuti wopha munthu mwangozi* azithawirako pothawa wobwezera magazi.+ 4 Azithawira kumzinda umodzi mwa mizindayi.+ Akatero azikaima pageti+ nʼkufotokoza nkhani yake kwa akulu a mzindawo. Akuluwo azimulandira nʼkumupatsa malo mumzindamo ndipo azikhala nawo limodzi. 5 Ngati wobwezera magazi amene akumuthamangitsa wafika, akuluwo asamapereke wopha munthuyo kwa wobwezera magaziyo, chifukwa iye sanaphe munthuyo mwadala ndipo sankadana naye.+ 6 Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,*+ ndipo azikhalabe komweko mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Zikatero, wopha munthuyo akhoza kubwerera nʼkukalowa mumzinda wa kwawo komwe anathawa kuja, nʼkumakhala mʼnyumba mwake.’”+
7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya mʼdera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ mʼdera lamapiri la Efuraimu komanso Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, mʼdera lamapiri la Yuda. 8 Kuchigawo cha Yorodano, kumʼmawa kwa Yeriko, anasankha Bezeri,+ mʼchipululu cha mʼdera lokwererapo la fuko la Rubeni. Anasankhanso Ramoti+ ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi komanso Golani+ ku Basana mʼdera la fuko la Manase.+
9 Imeneyi inali mizinda imene inasankhidwa kuti Aisiraeli onse ndi alendo okhala pakati pawo, azithawirako akapha munthu mwangozi,+ kuti asaphedwe ndi wobwezera magazi asanakaonekere pamaso pa oweruza.*+