Oweruza
15 Kenako, pa nthawi yokolola tirigu, Samisoni anapita kukaona mkazi wake uja ndipo anatenga kamwana ka mbuzi. Atafika anati: “Ndikufuna ndilowe kuchipinda kwa mkazi wanga.” Koma bambo a mkaziyo anamukaniza kulowa. 2 Iwo anati: “Ine ndinkaganiza kuti unadana naye,+ choncho ndinamʼpereka kwa mmodzi wa anyamata amene ankakhala nawe aja.+ Mngʼono wakeyu ndi wokongola kuposa iyeyu. Bwanji utenge ameneyu mʼmalomwake?” 3 Koma Samisoni anati: “Ulendo uno sindikhala ndi mlandu ndi Afilisiti ndikawachitira zoipa.”
4 Choncho Samisoni ananyamuka nʼkukagwira nkhandwe 300. Kenako anatenga nkhandwezo ziwiriziwiri nʼkuzimanga michira. Atatero, anaika muuni umodzi pakati pa michira iwiriyo. 5 Kenako anayatsa miyuniyo ndi moto, nʼkukusira nkhandwezo mʼminda ya Afilisti ya mbewu zosakolola. Choncho anayatsa chilichonse, kuyambira mitolo ya mbewu, mbewu zosakolola, minda ya mpesa komanso minda ya maolivi.
6 Zitatero, Afilisiti anafunsa kuti: “Wachita zimenezi ndi ndani?” Ndiyeno anauzidwa kuti: “Ndi Samisoni, mkamwini wa munthu wa ku Timuna uja, chifukwa munthuyu anatenga mkazi wa Samisoni nʼkumupereka kwa mmodzi mwa anyamata amene ankakhala ndi Samisoni ngati anzake a mkwati.”+ Afilisiti atamva zimenezi anapita kukatentha ndi moto mtsikanayo pamodzi ndi bambo ake.+ 7 Koma Samisoni anawauza kuti: “Ngati khalidwe lanu ndi limeneli, ndiye sindikusiyani mpaka ndibwezere.”+ 8 Ndiyeno anayamba kuwapha mmodzimmodzi. Kenako anapita nʼkumakakhala kuphanga la thanthwe la Etami.
9 Patapita nthawi, Afilisiti anabwera nʼkumanga msasa ku Yuda ndipo ankayendayenda ku Lehi.+ 10 Ndiyeno anthu a ku Yuda anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzatiukira?” Iwo anayankha kuti: “Tabwera kudzagwira* Samisoni kuti timʼchite zimene iye watichitira.” 11 Zitatero, amuna 3,000 a ku Yuda anapita kuphanga la thanthwe la Etami nʼkuuza Samisoni kuti: “Kodi iwe, sukudziwa kuti Afilisiti ndi amene akutilamulira?+ Ndiye nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi?” Iye anawayankha kuti: “Ndawachita zimene iwo anandichitira.” 12 Koma iwo anamuuza kuti: “Tabwera kudzakugwira* kuti tikakupereke kwa Afilisiti.” Samisoni anayankha kuti: “Lumbirani kuti inuyo simundichitira chilichonse choipa.” 13 Iwo anamuyankha kuti: “Ayi, sitikupha. Tingokumanga nʼkukakupereka kwa iwowo.”
Choncho anamʼmanga ndi zingwe ziwiri zatsopano nʼkumʼtulutsa kuphangako. 14 Atafika naye ku Lehi, Afilisiti nʼkumuona, anafuula chifukwa chosangalala. Ndiyeno mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu,+ ndipo zingwe zimene anamʼmanga nazo manja zija zinadukaduka ngati ulusi wowauka ndi moto nʼkugwa pansi.+ 15 Zitatero, anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo ndipo analitenga nʼkupha nalo amuna 1,000.+ 16 Kenako Samisoni anati:
“Ndi fupa la nsagwada za bulu, milumilu!
Ndi fupa la nsagwada za bulu, ndapha anthu 1,000.”+
17 Atamaliza kulankhula zimenezi, anataya fupalo ndipo malowo anawapatsa dzina lakuti Ramati-lehi.*+ 18 Ndiyeno anamva ludzu koopsa, ndipo anafuulira Yehova kuti: “Ndinu amene mwandipulumutsa ine mtumiki wanu. Ndiye kodi ndife ndi ludzu, nʼkufera mʼmanja mwa anthu osadulidwa?” 19 Choncho Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi ndipo panayamba kutuluka madzi.+ Samisoni atamwa madziwo, ludzu lake linatha ndipo anapezanso mphamvu. Nʼchifukwa chake anapatsa malowo dzina lakuti Eni-hakore.* Malo amenewa ali ku Lehi mpaka lero.
20 Samisoni anaweruza Isiraeli zaka 20 pa nthawi ya Afilisiti.+