-
2 Mafumu 16:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiyeno Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uliya+ kuti: “Paguwa lansembe lalikululi uziwotchapo nsembe yopsereza yam’mawa,+ nsembe yambewu yamadzulo,+ nsembe yopsereza ya mfumu+ ndi nsembe yake yambewu, nsembe yopsereza ya anthu onse a m’dzikoli ndi nsembe yawo yambewu, ndiponso nsembe zawo zachakumwa. Magazi onse a nsembe yopsereza ndi magazi onse a nsembe zina uziwawaza paguwa langali. Koma guwa lansembe lamkuwalo, ndiona chochita nalo.”
-