8 Ndipo lamba womangira efodi,+ wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota, wabwino kwambiri.
5 Kenako utenge zovala+ zija ndi kuveka Aroni. Umuveke mkanjo ndi malaya odula manja a mkati mwa efodi.* Umuvekenso efodi ndi chovala pachifuwa. Efodiyo um’mange bwino ndi lamba wake.+