28 Kenako munthu wa Mulungu woona+ uja anapita kwa mfumu ya Isiraeli n’kuiuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza Asiriya anena kuti: “Yehova ndi Mulungu wa mapiri, osati Mulungu wa zigwa,” ndipereka khamu lalikulu lonseli m’manja mwako,+ ndipo anthu inu mudziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+