9 Koma ine ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene iwo anali kukhala pakati pawo,+ pakuti ndinawachititsa kuti andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo powatulutsa m’dziko la Iguputo.+
22 “Chotero uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo a nyumba ya Isiraeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mwalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapita.”’+