Ekisodo 4:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+ Ekisodo 9:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+ Ekisodo 10:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma Yehova analola Farao kuumitsabe mtima wake,+ ndipo sanalole ana a Isiraeli kuchoka. 1 Samueli 6:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Komanso, mukuumitsiranji mitima yanu mmene Aiguputo ndi Farao anaumitsira mitima yawo?+ Si paja Mulungu atangowakhaulitsa+ analola Aisiraeli kupita, ndipo iwo anapitadi?+ Yesaya 26:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ngakhale munthu woipa atachitiridwa zabwino, sangaphunzire chilungamo.+ M’dziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zopanda chilungamo+ ndipo sadzaona ukulu wa Yehova.+
21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+
16 Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+
6 Komanso, mukuumitsiranji mitima yanu mmene Aiguputo ndi Farao anaumitsira mitima yawo?+ Si paja Mulungu atangowakhaulitsa+ analola Aisiraeli kupita, ndipo iwo anapitadi?+
10 Ngakhale munthu woipa atachitiridwa zabwino, sangaphunzire chilungamo.+ M’dziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zopanda chilungamo+ ndipo sadzaona ukulu wa Yehova.+