Ekisodo 6:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Chifukwa cha dzanja lamphamvu, iye awalola kuchoka, ndipo chifukwa cha dzanja lamphamvu awatulutsa m’dziko lake.”+ Ekisodo 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Patsala mliri umodzi wokha woti ndikanthe nawo Farao ndi Iguputo. Kenako adzakulolani kuchoka m’dziko lino.+ Pokulolani kuchoka ndi zonse zimene muli nazo, adzachita kukupitikitsani.+ Ekisodo 12:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Choncho Aiguputo anaumiriza anthuwo kuti achoke m’dzikolo mofulumira.+ Iwo anati, “chifukwa tonsefe tikungokhala ngati tafa kale!”+ Salimo 105:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Aiguputo anasangalala pamene Aisiraeli anatuluka m’dzikolo,Pakuti anali kuwaopa kwambiri.+
6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Chifukwa cha dzanja lamphamvu, iye awalola kuchoka, ndipo chifukwa cha dzanja lamphamvu awatulutsa m’dziko lake.”+
11 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Patsala mliri umodzi wokha woti ndikanthe nawo Farao ndi Iguputo. Kenako adzakulolani kuchoka m’dziko lino.+ Pokulolani kuchoka ndi zonse zimene muli nazo, adzachita kukupitikitsani.+
33 Choncho Aiguputo anaumiriza anthuwo kuti achoke m’dzikolo mofulumira.+ Iwo anati, “chifukwa tonsefe tikungokhala ngati tafa kale!”+