13 Koma ngati munthu ali wosadetsedwa, kapena sanapite pa ulendo, ndipo wanyalanyaza kukonza nsembe ya pasika, munthuyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake,+ chifukwa sanapereke nsembeyo kwa Yehova pa nthawi yake yoikidwiratu. Munthuyo adzafa chifukwa cha kuchimwa kwake.+