Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+

  • Ekisodo 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

      Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+

      Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+

  • Ekisodo 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndiye wamkulu kuposa milungu ina yonse.+ Zimenezi zinaoneka Aiguputo atasonyeza kudzikuza pamaso pa Aisiraeli.”

  • Yoswa 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ Tinamvanso za mmene munaphera+ mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya kwa Yorodano.

  • Nehemiya 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+

  • Yesaya 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+

  • Aroma 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena