Ekisodo
15 Pa nthawiyo Mose ndi ana a Isiraeli anayamba kuimbira Yehova nyimbo iyi, kuti:+
“Ndiimbira Yehova, pakuti iye wakwezeka koposa.+
Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.+
2 Mphamvu ndi nyonga yanga ndi Ya,*+ pakuti wandipulumutsa.+
Ameneyu ndi Mulungu wanga, ndidzam’tamanda.+ Ndiye Mulungu wa atate anga,+ ndidzam’kweza.+
3 Yehova ndi wankhondo.+ Dzina lake ndi Yehova.+
4 Magaleta a Farao ndi magulu ake ankhondo wawaponyera m’nyanja.+
Asilikali a Farao osankhidwa mwapadera amizidwa mu Nyanja Yofiira.+
5 Amizidwa ndi madzi amphamvu.+ Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+
6 Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, likusonyeza kupambana kwa mphamvu zake.+
Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.+
7 Ndipo mu ukulu wanu wopambana mumagwetsa otsutsana nanu.+
Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.+
8 Ndi mpweya wotuluka m’mphuno mwanu,+ madzi anaunjikika pamodzi.
Madzi oyenda anaima ngati khoma.
Madzi amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.
9 Mdaniyo anati, ‘Ndiwathamangira,+ ndi kuwapeza!+
Ndigawa chuma chawo.+ Pamenepo moyo wanga ukhutira ndi zimene ndawachita!
Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+
11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+
Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+
Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+
12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja,+ ndipo dziko lawameza.+
13 Mwa kukoma mtima kwanu kosatha, mwatsogolera anthu amene munawawombola.+
Mwa mphamvu yanu, inu mudzatengera anthu anu kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala.+
15 Pamenepo mafumu a ku Edomu adzasokonezeka.
Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera ndi mantha.+
Ndithu, anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+
16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+
Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala chete ngati mwala.
Kufikira anthu anu+ atadutsa, inu Yehova,
17 Mudzawabweretsa ndi kuwakhazikitsa m’phiri limene ndi cholowa chanu.+
Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukakhalemo,+ inu Yehova.
Malo opatulika+ amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.
18 Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale. Adzalamulira mpaka muyaya.+
19 Mahatchi a Farao,+ magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa m’nyanja,+
Yehova wabweza madzi a m’nyanjamo ndi kuwamiza.+
Koma ana a Isiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+
20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, mlongo wake wa Aroni,+ anatenga maseche m’manja mwake,+ ndipo akazi ena onse anam’tsatira akuimba maseche ndi kuvina.+ 21 Ndipo pamene amuna anali kuimba, Miriamu anathirira mang’ombe kuti:+
22 Kenako Mose anauza Isiraeli kuti anyamuke pa Nyanja Yofiira ndipo analowa m’chipululu cha Shura.+ Iwo anayenda m’chipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi.+ 23 Kenako anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. N’chifukwa chake anatcha malowo kuti Mara.*+ 24 Pamenepo anthu anayamba kung’ung’udza motsutsana ndi Mose,+ kuti: “Timwa chiyani?” 25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anam’sonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko m’madzi moti madziwo anakhala okoma.+
Pamenepo Mulungu anawakhazikitsira lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo pa nthawiyo anawayesa.+ 26 Ndiyeno anawauza kuti: “Ngati mudzamveradi mawu a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani miliri iliyonse imene ndinagwetsera Iguputo,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikukuchiritsani.”+
27 Kenako anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza.+ Iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.