33 Chotero Yowabu anapita kukaonana ndi mfumu ndipo anaiuza mawu amenewa. Ndiyeno mfumu inaitanitsa Abisalomu, moti iye anabwera kudzaonana ndi mfumu. Abisalomu atafika anagwada ndi kuwerama, kenako anadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Zitatero, mfumu inapsompsona Abisalomu.+