5 Sarai ataona zimenezi anauza Abulamu kuti: “Mlandu wa chipongwe chikundichitikirachi ukhale pa inu. Ine ndinapereka kapolo wanga kwa inu kuti akhale mkazi wanu, koma iye poona kuti watenga pakati wayamba kundichitira chipongwe. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu.”+