-
Levitiko 5:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 “‘Koma ngati sangakwanitse+ kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.*+ Azibweretsa ufa umenewu monga nsembe yake chifukwa cha tchimo limene anachitalo, kuti ukhale nsembe yamachimo. Asauthire mafuta+ ndipo asaikemo lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo.+
-
-
Levitiko 14:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 “Koma ngati munthuyo ali wosauka+ ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi,+ azibweretsa nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi monga nsembe ya kupalamula. Nsembeyo aziiweyulira uku ndi uku kuti am’phimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu.
-