Levitiko
5 “‘Tsopano munthu+ akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo,+ munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo* kuti akachitire umboni za wochimwayo koma iye osapita kukanena,+ ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.
2 “‘Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta, kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake,+ iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu.+ 3 Munthu akakhudza mosadziwa chodetsa chilichonse chochokera kwa munthu,+ chinthu chilichonse chodetsedwa chimene chingam’chititse kukhala wodetsedwa, koma wadziwa kuti wakhudza chodetsa, pamenepo wapalamula mlandu.
4 “‘Munthu akalumbira mpaka kulankhula mosalingalira bwino,+ mwa kunena kuti achita choipa+ kapena chabwino, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, koma akadziwa kuti walankhula mosalingalira bwino pa chilichonse chimene walumbira,+ pamenepo wapalamula mlandu pa chimene walumbiracho.
5 “‘Ndipo akadziwa kuti wapalamula mlandu pa chilichonse mwa zimenezi, pamenepo aziulula+ kuti wachimwa motani. 6 Ndiyeno azibweretsa kwa Yehova nsembe yake ya kupalamula+ chifukwa cha tchimo limene wachita. Azibweretsa nkhosa yaing’ono yaikazi+ kapena mbuzi yaing’ono yaikazi kuti ikhale nsembe yamachimo. Akatero wansembe aziphimba tchimo la munthuyo.+
7 “‘Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa,+ azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda kuti zikhale nsembe za kupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo+ ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 8 Pamenepo azizibweretsa kwa wansembe, ndipo wansembeyo azipereka nsembe yamachimo choyamba, ataicheka+ pakhosi koma osaduliratu mutu wake. 9 Kenako azidontheza ena mwa magazi a nsembe yamachimo m’mbali mwa guwa lansembe, koma magazi otsalawo aziwathira pansi pa guwa lansembelo.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10 Mbalame inayo aziipereka ngati nsembe yopsereza motsatira ndondomeko ya nthawi zonse.+ Choncho wansembe aziphimba machimo+ amene munthuyo wachita, ndipo azikhululukidwa.+
11 “‘Koma ngati sangakwanitse+ kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.*+ Azibweretsa ufa umenewu monga nsembe yake chifukwa cha tchimo limene anachitalo, kuti ukhale nsembe yamachimo. Asauthire mafuta+ ndipo asaikemo lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 12 Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuti ukhale chikumbutso+ cha nsembeyo. Kenako autenthe paguwa lansembe pamene pali nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 13 Ndiyeno wansembeyo aziphimba+ tchimo limene munthuyo wachita. Aziphimba tchimo lililonse mwa machimo amenewa, ndipo azikhululukidwa. Ufa wotsalawo uzikhala wa wansembe+ mofanana ndi nsembe yambewu.’”
14 Pamenepo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 15 “Munthu akachita mosakhulupirika mwa kuchimwira zinthu zopatulika za Yehova+ mosadziwa, pamenepo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake ya kupalamula.+ Nkhosayo mtengo wake uzikhala masekeli* asiliva+ ofanana ndi sekeli la kumalo oyera* kuti ikhale nsembe ya kupalamula. 16 Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera azilipira mwa kubweza zinthu zopatulikazo ndiponso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu+ a malipirowo. Malipirowo aziwapereka kwa wansembe, ndipo mwa kupereka nkhosa ya nsembe ya kupalamula, wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo azikhululukidwa.+
17 “Munthu akachimwa mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira,+ komabe wapalamula mlandu, pamenepo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+ 18 Azibweretsa kwa wansembe nkhosa yopanda chilema kuti ikhale nsembe ya kupalamula.+ Mtengo wa nkhosayo uzikhala wofanana ndi mtengo wake woikidwiratu. Ndiyeno wansembe aziphimba machimo+ a munthuyo chifukwa cha cholakwa chimene wachita mosadziwa, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, ndipo azikhululukidwa.+ 19 Imeneyi ndi nsembe ya kupalamula. Munthu ameneyo wapalamula mlandu+ kwa Yehova.”