Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Aliyense wa iwo anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka njoka zazikulu. Koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zawo.

  • Ekisodo 7:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, utambasule dzanja lako+ ndi kuloza madzi a mu Iguputo. Uloze mitsinje yawo, ngalande zawo zochokera kumtsinje wa Nailo, zithaphwi zawo,+ ndi maiwe awo onse kuti asanduke magazi.’ Pamenepo madzi a m’dziko lonse la Iguputo, ngakhalenso madzi a m’mitsuko yawo ya mtengo ndi ya mwala adzakhala magazi.”

  • Numeri 17:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Bwezera ndodo+ ya Aroni patsogolo pa Umboni. Uisunge kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana a chipandukowa,+ n’cholinga chakuti aleke kudandaula motsutsana ndi ine, kuti angafe.”

  • Aheberi 9:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe,+ ndi likasa la pangano.+ Likasa lonseli linali lokutidwa ndi golide.+ M’likasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana.+ Munalinso ndodo ya Aroni imene inaphuka ija,+ komanso miyala yosema+ ya pangano.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena