Levitiko 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 “‘Ngati akupereka ng’ombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza,+ azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako. Levitiko 22:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Isakhale yakhungu, yothyoka chiwalo, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo kapena zipere.+ Iliyonse yokhala ndi zimenezi musaipereke kwa Yehova ndipo musaike nsembe yotentha ndi moto+ ya nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova. Deuteronomo 15:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Akakhala ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, usamam’pereke nsembe kwa Yehova Mulungu wako.+ Deuteronomo 17:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Usapereke kwa Yehova Mulungu wako nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa yokhala ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa zimenezi ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wako.+
3 “‘Ngati akupereka ng’ombe kuti ikhale nsembe yake yopsereza,+ azipereka yamphongo, yopanda chilema.+ Aziipereka kwa Yehova mwa kufuna kwake,+ pakhomo la chihema chokumanako.
22 Isakhale yakhungu, yothyoka chiwalo, yotemeka, yokhala ndi njerewere, nkhanambo kapena zipere.+ Iliyonse yokhala ndi zimenezi musaipereke kwa Yehova ndipo musaike nsembe yotentha ndi moto+ ya nyama zoterezi paguwa lansembe la Yehova.
21 Akakhala ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, usamam’pereke nsembe kwa Yehova Mulungu wako.+
17 “Usapereke kwa Yehova Mulungu wako nsembe ya ng’ombe kapena nkhosa yokhala ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa zimenezi ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wako.+