39 Pa tsiku la 15 m’mwezi wa 7, pamene mwakolola zinthu za m’munda m’dziko lanu, muzichita chikondwerero+ cha Yehova masiku 7.+ Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi tsiku lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzipumanso pa ntchito zanu zonse pa tsiku la 8.+