6 Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,+ komanso mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Izi zikachitika, wopha munthuyo akhoza kubwerera kwawo,+ n’kukalowa m’nyumba mwake, mumzinda momwe anathawamo muja.’”