Ekisodo 12:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Nkhosayo muisunge kufikira tsiku la 14 la mwezi uno.+ Kenako banja lililonse la Isiraeli lidzaphe nkhosa yawo madzulo kuli kachisisira.*+ Levitiko 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 M’mwezi woyamba,* pa tsiku la 14 m’mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la pasika+ wa Yehova. Numeri 28:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “‘M’mwezi woyamba, pa tsiku la 14, pazikhala pasika wa Yehova.+ Deuteronomo 16:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Muzisunga mwambo wa m’mwezi wa Abibu*+ pochita chikondwerero cha pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+ Yoswa 5:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ana a Isiraeliwo anakhalabe ku Giligala. Anachita pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ ali m’chipululu cha Yeriko. Maliko 14:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Tsopano pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pamene mwa mwambo anali kupereka nsembe nyama ya pasika, ophunzira ake+ anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tipite kuti kumene tikakukonzereni malo odyerako pasika?”+ 1 Akorinto 5:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano,+ popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu+ waperekedwa+ monga nsembe yathu ya pasika.+
6 Nkhosayo muisunge kufikira tsiku la 14 la mwezi uno.+ Kenako banja lililonse la Isiraeli lidzaphe nkhosa yawo madzulo kuli kachisisira.*+
5 M’mwezi woyamba,* pa tsiku la 14 m’mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la pasika+ wa Yehova.
16 “Muzisunga mwambo wa m’mwezi wa Abibu*+ pochita chikondwerero cha pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+
10 Ana a Isiraeliwo anakhalabe ku Giligala. Anachita pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ ali m’chipululu cha Yeriko.
12 Tsopano pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pamene mwa mwambo anali kupereka nsembe nyama ya pasika, ophunzira ake+ anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tipite kuti kumene tikakukonzereni malo odyerako pasika?”+
7 Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano,+ popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu+ waperekedwa+ monga nsembe yathu ya pasika.+