13 Ansembe 7 onyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa, omwe anali kukhala patsogolo pa likasa la Yehova, anali kuyenda akuliza malipenga mosalekeza. Patsogolo pawo panali gulu la asilikali onyamula zida, ndipo pambuyo pa likasa la Yehova panali kubwera asilikali ena, malipenga akulira mosalekeza.+