-
Numeri 28:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Pang’ombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu.+ Ufawo uzikhala wothira mafuta. Nkhosa yamphongo imodziyo+ muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Ufawo uzikhala wothira mafuta.
-
-
Numeri 29:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza+ ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo malinga ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zotentha ndi moto zopereka fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+
-
-
1 Mbiri 21:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Koma Orinani anauza Davide kuti: “Ingotengani malowa akhale anu,+ ndipo mbuyanga mfumu chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino. Taonani, ineyo ndipereka ng’ombe+ kuti zikhale nsembe zopsereza ndi chopunthira tirigu+ kuti chikhale nkhuni,+ ndiponso ndipereka tirigu kuti akhale nsembe yambewu. Ndikupereka zonsezi.”+
-