Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ana ako aamuna ndi ana ako aakazi adzaperekedwa kwa anthu ena+ iwe ukuona ndipo udzawalakalaka nthawi zonse, koma manja ako adzakhala opanda mphamvu.+

  • 2 Mafumu 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mfumuyo inatenga+ anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ mmisiri aliyense+ ndi munthu aliyense womanga makoma achitetezo, n’kupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu onyozeka+ okha a m’dzikolo.

  • Yeremiya 52:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Anthu onyozeka pakati pa Ayudawo, anthu ena onse amene anatsala mumzindamo,+ anthu amene anathawira ku mbali ya mfumu ya Babulo ndi amisiri onse aluso, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anawatenga kupita nawo ku ukapolo.+

  • Yeremiya 52:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 M’chaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadirezara, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga Ayuda 745 kupita nawo ku ukapolo.+

      Anthu onse amene anawatenga anali 4,600.

  • Maliro 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Adani ake akumulamulira.+ Anthu odana naye sakuda nkhawa.+

      Yehova wamuchititsa kukhala wachisoni chifukwa cha kuchuluka kwa machimo+ ake,

      Ndipo ana ake ayenda patsogolo pa adani awo atagwidwa ukapolo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena