-
Ezekieli 8:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi a nyumba ya Yuda akuona ngati ndi chinthu chaching’ono kuchita zinthu zonyansa zimene akuchita panozi? Kodi akufunanso kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ n’kundikwiyitsa kachiwiri? Kodi waonanso kuti iwowo akulozetsa nthambi* kumphuno kwanga?
-
-
Danieli 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ife manyazi aphimba nkhope zathu lero.+ Manyazi aphimba nkhope za amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kumayiko onse akutali kumene munawabalalitsira chifukwa cha zinthu zosakhulupirika zimene anakuchitirani.+
-