33 Pambuyo pake, anatembenuka ndi kulowera njira ya ku Basana.+ Pamenepo, Ogi+ mfumu ya Basana inatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kukamenyana nawo pankhondo ya ku Edirei.+
10 Tamvanso zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kutsidya lina la Yorodano. Mafumuwo ndiwo Sihoni+ mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi+ mfumu ya Basana, imene inali ku Asitaroti.+
22 “Pamenepo munawapatsa maufumu+ ndi mitundu ya anthu ndipo munawagawira dzikolo chigawo ndi chigawo.+ Iwo anatenga dziko la Sihoni,+ dziko la mfumu ya Hesiboni+ ndi dziko la Ogi+ mfumu ya Basana.+